Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndilembe Chizindikiro pa Thupi Langa?

Kodi Ndilembe Chizindikiro pa Thupi Langa?

Achinyamata Akufunsa Kuti . . .

Kodi Ndilembe Chizindikiro pa Thupi Langa?

“Zizindikiro zina zimakhala zokongola kwambiri. Zimaoneka kuti panagona luso kwambiri pozijambula.”—Anatero Jalene. *

“Kwa zaka ziŵiri ndinali kulakalaka n’tadzakhalako ndi chizindikiro pa thupi langa.”—Anatero Michelle.

ANTHU kulikonseko amalemba zizindikiro pa thupi lawo. Anthu otchuka pa nyimbo za rock, pa zamaseŵera olimbitsa thupi, pa zovala za mafashoni, ndiponso pa za mafilimu amaonetsa zizindikiro za pa thupi lawo. Achinyamata ambiri amatsanzira zimenezi pomaonetsera poyera zizindikiro zojambulidwa pa mapeŵa awo, manja awo, ziuno zawo ndiponso akakolo awo. Andrew anati: “Kukhala ndi chizindikiro n’kutsogola. Munthu angathe kukhala nacho kapena kusakhala nacho malinga n’kukonda kwake.”

Buku la World Book Encyclopedia linati: “Zizindikiro za pathupi ndi zojambula zokhalitsa zimene zimalembedwa pathupi. Amazilemba poboola timabowo ting’onoting’ono pakhungu la munthu ndi kamtengo kosongoka kwambiri, fupa, kapena singano zomwe amaziviika mu inki.”

Ngakhale kuti n’zovuta kudziŵa bwinobwino kuti pali anthu angati amene amalembetsa zizindikiro, magazini ina inati anthu 25 pa anthu 100 alionse a za 15 mpaka 25 ku United States ali ndi zizindikiro. Sandy anati: “N’zimene aliyense akuchita.” Koma kodi n’chifukwa chiyani achinyamata ena amakopeka ndi zizindikirozi?

Kodi Zatchukiranji?

Ena amaona kuti zizindikiro zimaonetsa kuti munthuyo ngodziŵadi chikondi. Michelle anati: “Mchimwene wanga analemba dzina la chibwenzi chake pa kakolo wake.” Nanga kodi pali vuto pamenepa? Inde, chifukwa “chibwenzicho chinatha.” Magazini ya Teen inati “madokotala amati mwina anthu 30 pa 100 alionse ofufutitsa zizindikiro zawo amakhala atsikana ofuna kufufutitsa dzina la chibwenzi chawo chakale.”

Achinyamata ena amaona zizindikirozi ngati zinthu zongosonyeza luso lapamwamba. Ena amaziona ngati zinthu zosonyeza kuti ali ndi ufulu wochita zimene akufuna. Josie anati: “Ndine wamkulu, ndimadziŵa chimene ndikuchita,” ndipo anawonjezera kuti kulemba chizindikiro pa thupi lake “ndi nkhani yokhayo yaikulu kwambiri pa moyo wanga yomwe ndinaiganizirapo pandekha.” Achinyamata ena amalemba zizindikiro pa thupi lawo pofuna kulaŵako moyo wina, moyo womachita zinthu modziimira pankhani ya maonekedwe awo. Zizindikiro zingasonyezenso moyo wogalukira kapena woloŵerera. Motero pali zizindikiro zina zimene zimakhala ndi mawu ndiponso zithunzi zolaula kapenanso mawu amtopola.

Komano ambiri mwa achinyamataŵa amangokhala akutsanzira zimene zatchuka basi. Koma kodi inuyo muyenera kulemba chizindikiro pa thupi lanu chifukwa chakuti aliyense ali nacho?

Zinayamba Kalekale

Kulemba zizindikiro pa thupi sikunayambe lero ayi. Ofufuza anapeza mitembo yokhala ndi zizindikiro ku Aigupto ndi ku Libya, yakale kwambiri, zaka mazanamazana Kristu asanabwere. Mitembo yokhala ndi zizindikiro anaipezanso ku South America. Zambiri mwa zizindikirozo zinali zokhudzana kwambiri ndi kulambira milungu yachikunja. Wofufuza wina, Steve Gilbert anati “chizindikiro chakale kwambiri chimene tikuchidziŵa chomwe chimasonyeza chithunzi cha chinthu chodziŵika, osangoti chojambula chopanda tanthauzo, ndi chizindikiro cha mulungu wotchedwa Bes. Pa zikhulupiriro zakale za anthu a ku Aigupto, Bes ndiye anali mulungu wokonda zachiwerewere wa madyerero a chipwirikiti.”

M’pofunikanso kudziŵa kuti m’Chilamulo cha Mose Mulungu analetsa anthu kulemba zizindikiro pa matupi pawo. Lemba la Levitiko 19:28 linati: “Musamadzicheka matupi anu chifukwa cha akufa, kapena kutema mphini; ine ndine Yehova.” Olambira achikunja, monga Aigupto, ankatema mphini kapena kuti kudzilemba mayina kapena zizindikiro za milungu yawo pa mabere awo kapena m’mikono mwawo. Pomvera lamulo la Yehova loletsa zizindikiro zotere, Aisrayeli akanasiyana ndi anthu a mitundu inayo.—Deuteronomo 14:1, 2.

N’zoona kuti masiku ano Akristu sayendera Chilamulo cha Mose koma m’pofunikabe kuganizapo bwino pa lamulo loletsa zizindikiro. (Aefeso 2:15; Akolose 2:14, 15) Ngati muli Mkristu, n’zachidziŵikire kuti simungafune kulemba zizindikiro, ngakhale kwa nthaŵi yochepa chabe, pamene mukudziŵiratu kuti zizindikiro zotere zimayenderana ndi kupembedza kwa chikunja kapena zipembedzo zonyenga.—2 Akorinto 6:15-18.

Zingadzetse Matenda

Muyeneranso kuganizira za matenda amene kulemba zizindikiro kungakubweretsereni. Dr. Robert Tomsick, yemwe ndi wachiŵiri kwa pulofesa wa za khungu anati: “Mukadzilemba chizindikiro kwenikweni mumakhala mutaboola khungu lanulo n’kuthiramo inki. Ngakhale kuti singano wake sachita kuloŵa kwambiri pakhungupo, munthu akangoboola khungu, m’posavuta tizilombo toyambitsa matenda kuloŵapo. Ndingoti nthaŵi zambiri [kulemba zizindikiro pa thupi] kumangoputa matenda ali khale.” Dr. Tomsick anapitiriza kuti: “Inki ikangoloŵa pa khungu, ngakhale patati pasaloŵe tizilombo, n’kutheka kuti ingaŵenge munthu, ingabweretse matenda a pa khungu ndipo khungu lingawonongeke zomwe zingalichititse kufiira, kutupa, kukakala ndiponso kumanyereretsa.”

Ngakhale kuti anthu akamalemba zizindikiro cholinga chawo chimakhala chakuti zisadzafufutike mpaka kalekale, pali njira zingapo zimene ena amatsata poyesa kuzichotsa. Njira zake ndi monga kuwaula pakhungupo ndi moto wamagetsi, kuchitapo opaleshoni, kukwechapo ndi bulashi ya mawaya yomwe imachotsapo khungulo, kupaviika m’mankhwala amchere, ndiponso kuotchapo ndi asidi kuti pangokhala chipsera. Njira zonsezi n’zokwera mtengo kwambiri ndipo nthaŵi zina zimapweteka kwabasi. Magazini ya Teen inati: “Kuchotsa chizindikiro powaula khungu ndi moto wamagetsi kumawawa kwambiri kuposa kulemba chizindikirocho.”

Kodi Ena Angakuganizireni Zotani?

Muyeneranso kuganizapo mofatsa pankhani ya mmene anthu ena angaganizire pokuonani muli ndi chizindikiro, chifukwatu ambiri sagwirizana nazo zimenezi. (1 Akorinto 10:29-33) Mkazi wina wa ku Taiwan, dzina lake Li analemba chizindikiro pathupi pake ali ndi zaka 16 chifukwa choti zinangom’bwerera m’mutu basi. Panopo ali ndi zaka 21 ndipo amagwira ntchito mu ofesi. Iyeyu anati: “Zimandiipira kwambiri ndikamaona anzanga ogwira nawo ntchito akuyang’ana chizindikiro changacho ndi diso loŵeruza.” Theodore Dalrymple, yemwe ndi wa ku Britain ndipo amagwira ntchito yothandiza anthu pa matenda a maganizo, anati anthu ambiri amaona kuti zizindikiro “nthaŵi zambiri zimaonetsa kuti munthu . . . ali m’gulu la anthu achiwawa, zigandanga, anthu opulukira, ndiponso ochita zinthu zosokoneza.”

Nkhani ina m’magazini ya American Demographics inatchulanso mfundo yofanana ndi imeneyi ponena kuti: “N’zachidziŵikire kuti anthu ambiri a ku America amaona kuti munthu sangachite zinthu momasuka ngati ali ndi chizindikiro chinachake choonekera. [Achinyamata] 85 pa 100 alionse amavomerezana nawo mawu akuti ‘anthu amene ali ndi zizindikiro zoonekera . . . ayenera kuzindikira kuti zofuna zawozo zingawaike m’mavuto pamoyo wawo wa kuntchito ngakhalenso pa zochita zawo ndi anthu ena.’”

Ganizaniponso mofatsa pankhani ya mmene kukhala ndi chizindikiro kungakuthandizireni kapena kukulepheretsani kuchita zinthu zoyenererana ndi Mkristu. Kodi anthu ena ‘sangakhumudwe’ nazo? (2 Akorinto 6:3) N’zoona kuti achinyamata ena analemba zizindikirozi m’malo obisika a thupi lawo. N’kutheka kuti ngakhale makolo awo sadziŵa kuti anawo ali ndi zizindikiro zobisikazi. Koma chenjerani! Kachinsinsi kanuko kadzaululika tsiku lina mukadzapezeka kuti mwapita kuchipatala chifukwa cha zinthu zochitika mwadzidzidzi kapena mukamadzasamba kusukulu! Ndibwino ‘kukhala ndi makhalidwe abwino m’zonse,’ n’kumapeŵa kuchita chinyengo chopanda pake.—Ahebri 13:18.

Zizindikiro zingathe fasho nthaŵi ina iliyonse monga mmene mafasho ena onse amachitira. Kodi moti n’zoona kuti inuyo muli ndi chovala chinachake, kaya ndi jinzi, shati, diresi, kapena nsapato chomwe mumachikonda kwambiri moti mungalolere kuti muzichivala kwa moyo wanu wonse? N’zosatheka zimenezo! Zinthu zotchuka monga masitayelo, kametedwe, ndiponso mitundu, zimasinthasintha. Komano zizindikiro n’zosiyana ndi zinthu monga zovala chifukwa zimavuta kuchotsa. Komanso zinthu zimene mungazione ngati “zotsogola” pamene muli ndi zaka 16 sizingadzakusangalatseni mukadzafika zaka 30.

Anthu ambiri anong’onezapo bondo chifukwa choti anasintha mmene amaonekera moti sangabwererenso mwakale. Amy anati: “Ndinadzilemba chizindikiro ndisanayambe kuphunzira za Yehova. Panopo ndimayesetsa kuchiphimba. Koma zimandichititsa manyazi kwambiri anthu ena mumpingo mwathu akachiona mwatsoka.” Kodi pamenepa pali phunziro lotani? Pali phunziro lakuti osapupuluma kudzilembetsa zikangokubwererani m’mutu. Musasankhe kuchita zinthu zimene pambuyo pake mudzanong’oneza nazo bondo.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Mayina ena tawasintha.

[Chithunzi patsamba 17]

Nthaŵi zambiri zizindikiro zimasonyeza khalidwe logalukira

[Chithunzi patsamba 17]

Ambiri amene analemba chizindikiro pa thupi pawo amadzanong’oneza bondo pambuyo pake

[Chithunzi patsamba 18]

Osapupuluma kudzilembetsa zikangokubwererani m’mutu