Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kulankhulana Kumene Kumapatsa Moyo

Kulankhulana Kumene Kumapatsa Moyo

Kulankhulana Kumene Kumapatsa Moyo

PA ZOLENGEDWA zonse za padziko lapansi, ndi anthu okha amene sakhutira kulankhulana ndi anthu anzawo okha basi. Kaya ndi a mtundu wanji, otukuka motani, kaya ndi aamuna kaya aakazi, kaya ndi ophunzira bwanji, anthu onse amasonyeza kuti mwachibadwa chawo amafuna kulankhulana ndi Mulungu, yemwe ali woposa zonse.

Kodi kuteroku n’kukhulupirira zachabechabe? Ayi si choncho! Monga mmene nkhani yam’mbuyo ija yanenera, Mulungu analenga anthu m’chifanizo chake. Iye anatilenga mwakuti tizitha kumvetsa zinthu zauzimu. Zimenezi zikuphatikizapo kukhala ndi chikhumbo chofuna kulankhula naye monga Atate wathu wakumwamba. (Genesis 1:27; Mateyu 5:3) Ndipotu Mulungu amaona kuti n’kofunika kwambiri kuti anthufe tizilankhula naye moti mpaka amatchedwa kuti “Wakumva pemphero.”—Salmo 65:2.

Kupemphera kwa Wamphamvuyonse, ndithudi ndi mwayi wosaneneka! Anthu ambiri amaona kuti ndi mwayi wapadera kulankhula ndi munthu wapamwamba, monga pulezidenti kapenanso nduna yaikulu. Komatu Yehova Mulungu ndiye wapamwamba kwambiri m’chilengedwe chonse! Ndipo sitifunika kuchita kupangana naye kuti tilankhule naye. Tingathe kupemphera nthaŵi iliyonse komanso tili kwina kulikonse. Tingathe kupemphera kwa Mulungu ngakhale chamumtima. (1 Samueli 1:12-15) Komano Yehova amafuna kuti tizipemphera moona mtima ndiponso kuti tizimvera zonena zake. (Mika 6:8; Mateyu 6:5-13) Kodi suja kulankhulana kwabwino kumafuna kuti aliyense azilankhulapo pamene winayo akumvetsera?

Kodi Mumamvetsera Mulungu Akamalankhula?

Kodi munthu amamvetsera bwanji Mulungu akamalankhula? Amatero makamaka poŵerenga ndi kutsatira ziphunzitso zolembedwa m’Mawu ake, Baibulo Lopatulika. (2 Timoteo 3:16; 2 Petro 1:20, 21) Yesu anati: ‘Munthu adzakhala ndi moyo ndi mawu onse akutuluka mkamwa mwa Mulungu.’ (Mateyu 4:4) Kodi inuyo mumamvetsera Mulungu poŵerenga ndiponso kutsatira Mawu ake olembedwa?

Anthu amene amalankhula ndi Yehova nthaŵi zonse, iyeyo amawakonda ndipo amakhala ndi “mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse.” (Afilipi 4:6, 7; Miyambo 1:33) Komanso akuyembekeza kudzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi m’paradaiso, popanda moyo wa nkhaŵa kapena wovutika wangati wa masiku anowu. (Salmo 37:29; Yohane 17:3) Koma ndiye kudalatu! Zonsezi chifukwa chogwiritsira ntchito bwino luso lathu la kulankhulana kwanzeru.

[Chithunzi patsamba 26]

Kuŵerenga Baibulo ndiponso kupemphera ndi kulankhulana ndi Mulungu