Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kulankhulana N’kofunika Kwambiri Pakati pa Zachilengedwe za Padziko Lapansi

Kulankhulana N’kofunika Kwambiri Pakati pa Zachilengedwe za Padziko Lapansi

Kulankhulana N’kofunika Kwambiri Pakati pa Zachilengedwe za Padziko Lapansi

JULIE ali khanda, makolo ake ankangoyembekezera nthaŵi imene adzayambe kulankhula. Mayi a Julie anati: “Palibe kholo limene lingalongosole bwinobwino mmene zimasangalatsira kumva mawu akuti ‘Amama’ ndi ‘Ababa’ akuchoka pakamwa pa mwana wako. Nthaŵi yoyamba imene Julie anandiitana kuti ‘Amama,’ ndinkangomva ngati kuti wandikupatira ndi timanja take ndipo akunena kuti: ‘Mayi anga ndi inuyo. Ndimakukondani, ndipo ndikufuna kulankhula nanu.’ Nthaŵi imeneyo sindidzaiiŵala ayi.” N’zoonadi kuti kulankhulana ndi mphatso yamtengo wapatali!

Inde, si anthu okha amene analengedwa moti azitha kulankhulana. Ngakhale kuti nthawi zambiri nyama zimachita zinthu mwa chibadwidwe chawo, nazo zimalankhulana m’njira zodabwitsa kwambiri. Mwachitsanzo, chaka chilichonse, nyengo yachisanu ikayandikira, mbalame zotchedwa emperor penguin za m’dera lozizira kwambiri lotchedwa Antarctica, zikamatomerana zimayamba kulira mopokolezana. Mbalamezi sikuti zimatero chifukwa chongosangalala ayi koma zimatero poganizira tsogolo la mwanapiye wa banja lililonse la mbalamezo. Chimachitika n’chiyani makamaka?

Mbalame yaikazi ikaikira dzira, imalisiya m’manja mwa mbalame yaimuna kuti ilifungatire poliika m’kathumba komwe kamakhala pamimba pake, ikatero yaikaziyo imapita kunyanja kuti ikadye. Pakatha masiku mwina 65, yaikazi ija imabwerako ndipo mwina imatha mtunda wokwana makilomita 150 ikuyenda mwachinyachinya ndi miyendo pamadzi oundana kapena kudzikhwekhwereza pamadzipo ndi mimba yake. Kupeza gulu la mbalame zinzakezo pakokha n’kodabwitsa, komano kodi zimatheka bwanji kuti mbalame yaikaziyi ipeze mwamuna wake ndiponso mwanapiye wawo amene wangoswayo pakati pa chigulu cha mbalame zinzake zikwizikwi zomwenso zimakhala zikulira? Chimachitika n’chakuti mbalame ziŵirizi zikamatomerana muja, iliyonse imaloŵeza mosamalitsa kaliridwe ka inzakeyo moti ngakhale patatha miyezi zitapatukana, zimathabe kupezana!

Kuphatikiza pa kulira kosiyanasiyana kochititsa chidwi, nyama zimalankhulana ndi thupi lawo lonse, mtundu wa bweya wawo wochititsa chidwi zinzake, kuwala kophanimaphanima, ndiponso fungo losiyanasiyana. Ngakhale kuti n’zovuta kumvetsa, koma ndithu n’zoona kuti zomera nazo zimalankhulana ndiponso zimalankhulitsa nyama zinazake, monga mmene timvere bwino lino. N’zoona, kulankhulana n’kofunikadi pakati pa zachilengedwe zosiyanasiyana za padziko lapansi zomwe zimadalirana kwambiri.

Kodi mukufuna mutadziŵa njira zina zodabwitsa zimene zachilengedwe zimalankhulirana? Ndipo kodi mukufuna mutamanyadira kwambiri luso lanu la kulankhula mwinanso kulinola kumene? Nkhani zotsatirazi zingakuthandizeni kutero.

[Chithunzi patsamba 19]

Kodi mbalame zazikazi za emperor penguin zimadziŵa bwanji pamene pali amuna awo?