Mavuto A Zaulimi Adzatha
Mavuto A Zaulimi Adzatha
“ANTHU ena omwe si alimi akamaona zimene alimi amakumana nazo amadabwa chifukwa chake anthu akupitirizabe ulimi,” anatero Rodney, yemwe agogo ake ndiwo anayamba ulimi umene akuchita. Komatu anthu miyandamiyanda padziko lonse akulimabe. M’mayiko ena amene akukwera kumene n’kovuta kupeza ntchito ina, moti ulimi ndiwo ungathandize banja kuti lizipeza chakudya.
Ndiponso, mabanja ambiri amaona kuti ulimi si ntchito yongopezerapo ndalama chabe, koma kuti ndicho chikhalidwe chawo. Kuchuluka kwa anthu amene apitirizabe ulimi ngakhale kuti kunali chilala, matenda, mavuto a zachuma, ndi mavuto ena kukupereka umboni wakuti anthuŵa ali ndi khama losaneneka ndiponso kuti amakonda ulimi. Tisanaone njira zothetsera mavuto a ulimi, tiyeni choyamba tione mmene alimi ena athandizikira.
Mmene Ena Amathandizikira
Ulimi umakhala ndi zovuta zosapeŵeka zambiri. Tifunika kuvomereza kuti sitingalamulire nyengo, kayendedwe ka chuma, komanso zinthu zina zambiri. Lipoti la bungwe la North Carolina Cooperative Extension Service linati: “Alimi ambiri zimawawawa kuzindikira kuti si nthaŵi zonse pamene kugwira ntchito zolimba kumapindulitsa. Si nthaŵi zonse pamene mzimu wogwira ntchito molimbika, umene mlimi aliyense amakhala nawo, umam’bweretsera phindu lomwe amaliyembekezera. Pali zochitika ndi zinthu zina zimene mlimi wina aliyense palibe chimene angachitepo.” Mlimi wina wokalamba anafotokoza zimene ankachita kuti akhalebe wachimwemwe, ndipo anati: “Ndangophunzira kusada nkhaŵa kwambiri ndi zinthu zosapeŵeka.”
Mwambi wina wakale umati: “Woyang’ana mphepo sadzafesa; ndi wopenya mitambo sadzakolola.” (Mlaliki 11:4) Kukayikakayika komanso kulephera kusankha zochita kungalefule munthu. Simungapanikizike kwambiri ngati muyamba kuchita zinthu zothandiza m’malo moganiza zofooketsa.
N’kothandizanso kudya bwino, kupumula mokwanira, ndi kuchita maseŵera olimbitsa thupi oyenerera. Magazini ya The Western Producer inati alimi amene amakhala ndi thanzi labwino “amaganiza bwino pochita zinthu.” Mlimi wina wotchedwa Eugene limodzi ndi mkazi wake Candace anafotokozera wolemba magazini ya Galamukani! kuti: “Kupuma mokwanira kumatithandiza kuti tisakhale pampanipani. Tikapumula mavuto amaoneka ochepa ndi osavuta kuthetsa. Kudya moyenerera kumathandizanso, makamaka banja lonse likamadyera pamodzi.” Malangizo ameneŵa akugwirizana ndi zimene Baibulo limanena kuti: “Munthu yense adye namwe naone zabwino m’ntchito zake zonse; ndiwo mtulo wa Mulungu.”—Kuthandiza Banja
Mlimi wina anauza wolemba Galamukani! kuti: “Mabanja ambiri a alimi amafunika kugwira ntchito zina osati zaulimi kuti azipeza zinthu zofunika pamoyo wawo. Ngakhale kuti amachita izi n’cholinga chakuti asamavutike kupeza ndalama, zingayambitse mavuto ena pa unansi wawo. Mabanja ena a alimi amene kale anali ogwirizana kwambiri lero aliyense akungochita zofuna zake.” Kodi mabanja angathandizike bwanji?
Zaka pafupifupi 2,700 zapitazo, Miyambo 24:27) Randy, yemwe ali ndi ana ndipo akupitiriza ulimi umene anayamba agogo awo a abambo ake, anati: “N’kofunika kwambiri kupeza nthaŵi yokhala pansi n’kuyamikira aliyense m’banja. Aliyense m’banja amafuna kulimbikitsidwa ndi kusonyezedwa chikondi. Kulankhula mawu okoma ndi kuchita zinthu mokoma mtima kumapangitsa aliyense kuona kuti ndi wofunikira ndiponso kuti mumamuyamikira.”
mitu ya mabanja inalangizidwa kuti: “Longosola ntchito yako panjapo, nuikonzeretu kumunda; pambuyo pake ndi kumanga nyumba yako.” (Makamaka ana amafunika kuwakhazika mtima pansi zinthu zikasintha kwambiri. Ena amati banja likalandidwa famu, ana a m’banjalo amamva mofanana ndi mmene amamvera ana omwe makolo awo asudzulana kapena kumwalira. Amafunika kudziŵa kuti vutolo silinabwere chifukwa cha iwowo komanso kuti nonse m’banjamo muzikhalabe pamodzi.
Mmene Ena Angathandizire
Alimi amene maganizo awathina kwambiri sangafune kuchita zinthu ndi ena, ndipo angamapeŵe ngakhale azinzawo. (Miyambo 18:1) Komabe, pamene munthu ali m’mavuto m’pamenetu amafunika kwambiri anthu ena kuti amuthandize!
Kodi anzanu ena kapena anthu ena m’mudzi mwanu akuvutika ndi mavuto a zaulimi? Anthu oterowo zingawathandize kwambiri mutangowasonyeza kuti mukuwamvera chifundo. Mlimi wina dzina lake Ron anati: “N’zolimbikitsa kwambiri kuti anzathu akuzindikira mavuto amene tikukumana nawo.” Inde, yambani ndinu kuchezera anzanu ndipo amvetsereni akamatulutsa zakukhosi kwawo.
Jack zinkamuthandiza kwambiri anzake akamuchezera. Iye anasimba kuti: “Ndimakonda kukumbukira nthaŵi zimene anzanga mwachikondi chawo anali kubwera kudzandilimbikitsa akaona kuti ndili pampanipani.” Sizilira kuti mudziŵe bwino kwambiri zaulimi kuti muthe kuthandiza munthu wina. Rodney, tinamutchula poyambirira uja, anati: “Mfundo yokhayo yakuti anzanga akudziŵa kuti ndili ndi ntchito yambiri imandipatsa mphamvu komanso chikhumbo chofuna kuyesetsa kuchita zimene ndingathe.” Izitu zikutikumbutsa mwambi wa m’Baibulo wakuti: “Bwenzi limakonda nthaŵi zonse; ndipo mbale anabadwira kuti akuthandize pooneka tsoka.”—Miyambo 17:17.
Njira Yothetseratu Vutoli
Mavuto aulimi ndi umboni umodzi chabe mwa maumboni ambirimbiri osonyeza kuti anthu akulephera kugwiritsa ntchito bwino dziko lapansi ndi zinthu zake. Mneneri Yeremiya anati: “Inu Yehova, ndidziŵa kuti njira ya munthu sili mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.” (Yeremiya 10:23) N’zachionekere kuti anthu afunika thandizo la Mulungu. Ndipotu mungakhale n’chidaliro chakuti thandizo limenelo lili m’njira.
Nkhani ya m’Baibulo imati: “Yehova Mulungu anatenga munthuyo, namuika iye m’munda wa Edene kuti aulime nauyang’anire.” (Genesis 2:15) Inde, Mlengi wathu ndiye analamula kuti pakhale ulimi! Patapita zaka mazana ambiri, Mulungu anapititsa anthu ake Aisrayeli ku dziko la Kanani. Nkhani youziridwa ndi Mulungu imanena za dziko limenelo kuti: “Limamwa madzi a mvula ya kumwamba; ndilo dziko loti Yehova Mulungu wanu alisamalira, maso a Yehova Mulungu wanu akhalapo chikhalire, kuyambira chaka mpaka kutsiriza chaka.” (Deuteronomo 11:11, 12) Yehova anaperekanso malamulo omwe anateteza Dziko Lolonjezedwalo kuti anthu asaliwononge. Mwachitsanzo, chaka cha seveni chilichonse Aisrayeli ankafunika kugoneka minda yawo ya mphesa, ya azitona, ndi ya mbewu zina. (Eksodo 23:10, 11) Potero nthaka inali kukhalabe yachonde.
Tingakhale n’chidaliro chakuti m’tsogolomu panthaŵi ya ulamuliro wa Ufumu wa Mulungu, womwe ndi boma lakumwamba lolamuliridwa ndi Yesu Kristu, padziko lapansi padzakhala ulimi wadzaoneni. (Yesaya 35:1-7) Ali padziko lapansi, Yesu Kristu, yemwe anasankhidwa kukhala Wolamulira wa Ufumu umenewu, anaonetsa kuti ndi wokhoza kulamulira zinthu zachilengedwe zimene zimakhudza ulimi. (Marko 4:37-41) Salmo 72 limalongosola mmene zinthu zidzakhalira iye akadzagwiritsa ntchito mphamvu zimenezi kukonza dziko lapansi ndi zonse zili mmenemo. Limatitsimikizira kuti: “M’dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka pamwamba pa mapiri; zipatso zake zidzati waa, ngati za ku Lebano: Ndipo iwo a m’mudzi adzaphuka ngati msipu wapansi.” (Salmo 72:16) M’dziko latsopano lomwe lalonjezedwalo, anthu a Mulungu akuyembekezera kudzatuta n’chimwemwe chodzadza tsaya zokolola za mwana alirenji.
[Mawu Otsindika patsamba 9]
“Alimi ambiri zimawawawa kuzindikira kuti si nthaŵi zonse pamene kugwira ntchito zolimba kumapindulitsa”
[Zithunzi patsamba 10]
Anthu m’banja lanu zingawathandize kwambiri mukamaganizira nkhaŵa za mumtima mwawo ndiponso zofunika zawo zauzimu
[Chithunzi patsamba 10]
Mu ulamuliro wa Mulungu, padziko lapansi padzakhala chakudya cha mwana alirenji
[Mawu a Chithunzi patsamba 9]
Garo Nalbandian