Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zitaphulika

Zitaphulika

Zitaphulika

YOLEMBEDWA NDI WOLEMBA GALAMUKANI! KU ECUADOR

PA NOVEMBER 20, chaka cha 2002, linali tsiku labwino kwambiri mu mzinda wa Riobamba m’dziko la Ecuador. Kumwamba kunali kuwala bwino, ndipo kunali mitambo yapatalipatali. Mapiri okututidwa chipale chofewa pamalowo anali kuoneka bwino kwambiri. Anthu okwana 124,000 okhala mu mzindawu, pa mtunda wa mamita 2,700 kuchokera ku mapiri a Andes, anali kuchita ntchito zawo za masiku onse osadziŵa kuti kunja kwa bataku kugwa chiyani. Mwadzidzidzi, chakumadzulo batalo linatha chifukwa cha kuphulika kogonthetsa m’khutu! Mawindo ndi simenti zinayamba kunjenjemera. Mtambo wochititsa mantha wonga bowa unayamba kupangika ndipo unali kumangokulirakulirabe.

Pasanathe mphindi teni panamvekanso kuphulika kwina kumene kunachititsa zinthu kunjenjemera mwamphamvu komwe kunawononga mawindo ndi kuzuliratu zitseko. Panaoneka mtambo woyenda mozungulira wa moto ndi utsi ndipo kukula kwake kunaposeratu mtambo woyamba uja. Panamveka kuphulika kotsatizanatsatizana pamodzi ndi kung’anima.

José ndi mkazi wake, Ana omwe ndi Mboni za Yehova a zaka za m’ma 60 anali kukhala pa mtunda wa mamita 400 kuchokera pamalo angoziwo. Onse anaponyedwa pa simenti ndi mphamvu ya kuphulikako. Mkazi wa José anali ataimirira pafupi ndi chitseko chakutsogolo chomwe chinazuka mwamphamvu n’kukachimenyetsa ku khoma lakumbuyo. Denga linayamba kugwera banja la nkhaŵa limeneli pamene linkathaŵira kukhomo la kumbuyo. Mosadziŵika bwino anatha kutulukira kubwalo podzera pampata waung’ono kumbuyo kwa nyumba yawoyo, komwe anakumbatirana nayamba kupemphera. Mwamwayi, patapita mphindi 15 mwana wawo anafika ndi galimoto nawatengera kumalo ena.

Si onse amene zinthu zinawayendera bwino chonchi. Anthu anali ndi mantha aakulu pambuyo pa kuphulikako. Anthu ambirimbiri anathaŵa wapansi. Uku anthu akufuula ndi kukuwa, ena anali kugwera pa magalasi ophwanyika omwe anali mbwee mphepete mwa msewu. Magalimoto aang’ono, mabasi ndi magalimoto akuluakulu anali kuyenda mwa ngozi mu mzindawu chifukwa anali kuthamanga kwambiri ndiponso kuyenda mbali yolakwika ya misewu. Anthu ambiri omwe anathaŵa kuchokera kusukulu ndi kuntchito sanadziŵe zimene zinachitikira achibale awo kapena kumene anali, kwa maola pafupifupi 24.

Kodi n’chiyani chinachititsa chipwirikiti chonsechi? Unali moto umene unabuka m’nkhokwe ya zida za nkhondo ya pansi pa nthaka ku malo a asilikali. Motowo unagwirira mizinga, mabomba a manja, akasinja ndi mfuti. Kuphulikako kuli mkati, galimoto za polisi zinkalengeza kuti anthu onse atalikirane ndi mzindawu kwa makilomita pafupifupi 15.

Posapita nthaŵi mu mzinda wa Riobamba munali zii. Anthu ambirimbiri anadzadza msewu wonse wa kunja kwa mzindawu, naunjikana malo amodzi pamtetete opanda zovala zamphepo. Patapita maola angapo, kuphulikako kunayamba kuchepa. Chifukwa cha chisanu, anthuwo anayamba kubwerera kumzindawo koma mosamala kwambiri. Tsiku lotsatira chakummaŵa, anthu ambiri anaona kuti mawindo, zitseko, madenga, ndi makoma a nyumba zawo zinali zitawonongeka. Banja lina linapeza tizidutswa ta magalasi tonga mipeni titabayabaya matiresi awo. Mabanja ena anapeza tizidutswa ta zitsulo tili mbwee m’nyumba mwawo ndi panja pomwe.

Malipoti oyambirira anasonyeza kuti, anthu seveni anafa, 538 anavulala, ndipo nyumba zokwana 18,000 zinagwa. Mumzindawu munali Mboni za Yehova zokwana 950, koma panalibe ndi m’modzi yemwe amene anafa, ngakhale kuti aŵiri anapatsidwa thandizo chifukwa anali ndi mabala oopsa.

Kuthandiza Ovutika

Kuphulikako kutatha, m’maŵa mwake akulu a mpingo wa Mboni za Yehova wakumaloko, anayamba kuyendera abale awo achikristu kuti aone kuti zinthu zinawathera bwanji. Kenako patapita nthaŵi pang’ono tsiku lomwelo, mtumiki woyendayenda wa Mboni za Yehova anakumana ndi akulu ochokera m’mipingo 13 ya m’mzindawo komanso yozungulira mzindawo kuti aone zinthu zowonongeka ndi anthu ovulala. Iye analimbikitsa akuluwo kuti asonyeze chikondi ndi kupereka zofunika zauzimu kwa anthu opulumukawo. Kupezeka pamisonkhano yachikristu panthaŵi yovutayi kunali kofunika kwambiri! (Ahebri 10:24, 25) Moti chakumadzulo vutolo litatha, mipingo yakumeneko inapanga misonkhano yawo yomwe imachita nthaŵi zonse.

Pofika Lachinayi ndi Lachisanu, lipoti lonse lokhudza nyumba zowonongeka za Mboni linapangidwa ndipo linatumizidwa ku ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Guayaquil m’dzikolo. Lipotilo linafotokoza kuti thandizo la mwamsanga lokonzanso mawindo a nyumba ambirimbiri linali kufunika n’cholinga choteteza anthuwo ku chisanu. M’maola ochepa chabe, ofesi ya nthambi inagula mipukutu ya mapepala a pulasitiki, masilotepi, ndi misomali yoloŵa pansi pa simenti zopangira malo ongoyembekezera.

Galimoto yaikulu yonyamula katundu yochokera ku ofesi ya nthambi inafika Loŵeruka m’maŵa nthaŵi ya 9 koloko. Magulu a amuna ndi akazi a Mboni anali atafika kale kuthandiza Mboni zinzawo kuchotsa magalasi ophwanyika m’nyumba zawo kuti ntchito yoika mapulasitiki iyambe. Nyumba ya Ufumu ya kumaloko inasanduka malo olinganizira zonse. Kuti adule mapulasitikiwo mwamsanga, anali kulemba zizindikiro pa simenti. Pogwiritsa ntchito miyeso imene anabweretsa magulu opereka thandizo, mapulasitiki ankadulidwa moyenerera nawapereka ku magulu otseka m’mawindo omwe anali kuyembekezera ku nyumbazo.

José, yemwe tamutchula poyamba mu nkhani ino anati: “Panthaŵi yakumadzulo imene tinafika kunyumba kuphulikako kutatha, tinapeza abale atayamba kale kuchotsa zidutswa. Loŵeruka munthu woyandikana naye nyumba anafika ndipo anadabwa ndi ntchito yapamwamba yoika mapulasitiki yomwe inachitika panyumba yanga, ndipo anafunsa kuti ‘Kodi ntchito yonseyi yakudyerani ndalama zochuluka motani?’” Anadabwatu kwambiri atamva kuti ntchitoyo inapangidwa kwaulere!

Pofika usiku wa Loŵeruka, antchito ongodzipereka pafupifupi 200 ochokera ku mipingo yoyandikira mzindawo, anali atatseka mawindo a nyumba za Mboni zokwana 91. Anthu enanso omwe sanali Mboni analandira thandizolo. Nyuzipepala ya m’dzikolo inatulutsa chithunzi cha nyumba yokonzedwa ndi Mboni, ndipo inati munthu mmodzi yekha mwa anthu eiti omwe amakhala m’nyumbayo ndiye wa Mboni za Yehova.

Analimbikitsidwa Kuti Asataye Mtima

N’zosadabwitsa kuti kuphulika kwa zinthuku kunapangitsa kuti anthu ataye mtima kwambiri. Lolemba, pa November 25, nthaŵi ya 5 koloko madzulo kunapangidwa msonkhano pofuna kulimbikitsa Mboni za m’deralo. Woimira ofesi ya nthambi ya m’dzikolo anatumidwa kukachititsa msonkhanowo. Chifukwa chakuti kunalibe magetsi, msonkhanowo sukanachitika madzulo kwambiri. Ndipo anthu pafupifupi 600 ndiwo anali kuyembekezedwa kufika kumsonkhanoko popeza sunachitike nthaŵi yabwino. Komatu gulu la anthu lokwana ngati 1,421, kuphatikizapo omwe sanali Mboni anadzadza Nyumba ya Msonkhano ya ku Riobamba! Lemba lalikulu lomwe linafotokozedwa pa pulogalamuyi ndi Salmo 4:8 lomwe limati: “Ndi mtendere ndidzagona pansi, pomwepo ndidzagona tulo; chifukwa Inu, Yehova, mundikhalitsa ine, ndikhale bwino.” Anthu onse amene anapezekapo anayamikira kwambiri pulogalamu ya chitonthozo chauzimu imeneyi.

Makope ambirimbiri a nkhani yakuti “Masoka Achilengedwe—Kuthandiza Mwana Wanu Kulimbana Nawo” yochokera mu Galamukani! ya July 8, 1996 anaperekedwa kwa makolo pamapeto pa pulogalamuyo. Ndime imodzi ya nkhaniyo imati:

“Federal Emergency Management Agency (FEMA) ya ku United States imanena kuti mwamsanga pambuyo pa tsoka, mwachibadwa ana amaopa kuti (1) adzasiyidwa okha, (2) adzasiyanitsidwa ndi banja, (3) chochitikacho chidzabwerezanso, ndipo (4) wina wake adzavulazidwa kapena kuphedwa.” M’nkhani yomweyi, makolo analimbikitsidwa izi:

1. Kuyesetsa kuchititsa banja kukhala pamodzi.

2. Kupatula nthaŵi ya kufotokoza mofatsa.

3. Kulimbikitsa ana kulankhula.

4. Kuphatikiza ana pantchito zoyeretsa.

Makope ena a nkhani ya mu Galamukani! imeneyi anaperekedwa kwa ophunzira Baibulo ndi oyandikana nawo nyumba.

Patapita milungu itatu chichitikireni tsokalo, panagulidwa zipangizo zokonzera zinthu zinawonongekazo monga kuika mawindo atsopano, ndi kukonzanso denga. Patapita milungu ina itatu, ntchito imeneyi inali itatheratu kuphatikizaponso Nyumba za Ufumu. Anthu ambiri anayamikira zedi thandizo lachikondi limeneli.

Masoka osiyanasiyana ngosachita kunena “masiku otsiriza” ano. (2 Timoteo 3:1-5) Komabe, thandizo limene Mboni za Yehova zimapereka kwa a Mboni anzawo ndi anthu ena limapereka umboni wakuti Chikristu choona si mawu okha komanso zochitika. José sanazengereze kunena kuti: “Gulu la Yehova silichedwa kupereka thandizo pamene tikulifuna mwamsanga.”

[Zithunzi patsamba 15]

Mboni zoposa 200 zinadzipereka kuyeretsa. Anayesa, kudula, ndi kuika mawindo atsopano. Anabwezeretsa madenga.