Chiyambi cha Moyo Wanga Wokhutiritsa
Chiyambi cha Moyo Wanga Wokhutiritsa
YOSIMBIDWA NDI ERNEST PANDACHUK
Ndinabadwira ku Canada, m’dera lina lopanda mitengo, m’chigawo chotchedwa Saskatchewan. Nditakwanitsa zaka 23, ndinapita ku Africa komwe ndinakhalako zaka 35 ndikukomedwa nawo moyo wa umishonale. Kodi zinatheka bwanji kuti mpaka ndifike pamenepa? Si kuti zinangochitika zokha. Imani ndikuuzeni.
NYUMBA yathu yoyamba inali yamitengo, yochita kuphoma ndi dothi, komanso ya udzu, koma inkatiteteza ndithu ku chisanu chimene chimawomba m’derali. Mu 1928, ambiri mwa ana 9 m’banja mwathu tisanabadwe, Bambo ndi Mayi analandira mabuku ofotokoza za m’Baibulo amene mlendo wina amene anafika kunyumba kwathu anawapatsa. Itafika nyengo yachisanu, iwo anaphunzira Baibulo m’nyengo yonseyo mothandizidwa ndi mabuku ameneŵa. Mmene nyengo yotentha inkayamba, n’kuti atakhutira kuti apezadi choonadi. Ndipo ankauza abale awo, anzawo, ndiponso anthu ena oyandikana nawo koma makamaka ana awofe, za choonadi chimenechi.
Ndinabadwa m’chaka cha 1931, ndipo sipanatenge nthaŵi kuti ndikhale ndi azing’ono anga asanu. M’banja mwathu kuŵerenga ndi kuphunzira Baibulo kunali kudya kwathu. Ndimakumbukira kwambiri zimene tinkachita mmaŵa uliwonse. Bambo ankatitsogolera pokambirana lemba la m’Baibulo, ndipo ankachita zimenezi ngakhale alendo akhalepo. Mayi ndi Bambo, komanso ana okulirapo, ankasinthana kuŵerenga mokweza nkhani zochokera m’mabuku ofotokoza za m’Baibulo.
Bambo sanalekere pongotiphunzitsa kuŵerenga ndi kulemba basi, koma anatiphunzitsanso mmene tingafufuzire nkhani pogwiritsira ntchito anamulozera a nkhani za m’Baibulo. Sitinachedwe kudziŵa kugwiritsira ntchito Baibulo pofotokozera anthu ena zimene timakhulupirira. Nkhani zosangalatsa zimene tinkakambiranazi zinandithandiza kumaganizira mozama nkhani za m’Baibulo. Patapita nthaŵi, ndinayamba kutha kufotokoza ziphunzitso zimene zinali zonama pogwiritsira ntchito Baibulo. Ndinayamba kutha kufotokoza bwinobwino kuti palibe mbali inayake ya munthu imene siifa munthu akamwalira, kuti kulibe moto wa helo, ndiponso kuti Mulungu ndi Yesu si ofanana mphamvu kapena kuti sali mbali inayake imene amati Utatu.—Mlaliki 9:5, 10; Ezekieli 18:4; Yohane 14:28.
Bambo ndi Mayi ankatiphunzitsanso zinthu zina chifukwa cha zitsanzo zawo ndipo ankatilimbikitsa kusagonja pochita zabwino, ngakhale zitakhala zoti zipangitsa anzathu kuti asagwirizane nafe. Mwachitsanzo, iwo sankasuta fodya, ndipo ankatichenjeza za kuopsa kwake kwa fodyayo ndiponso mmene anzathu azidzachitira zinthu zotilimbikitsa kusuta. Ndimakumbukira Bambo akutiuza kuti: “Ena azidzakunenani kuti ndinu ogona mutawakanira kusuta. Koma muzidzangofunsa wokunenaniyo kuti, ‘Kodi wogona ndani? Kodi angakhale munthu wochita zinthu motumidwa ndi fodya kapena wokana kugonjera zimene fodya amafuna?’”
Chiyeso china chofuna kuona ngati ndikanatsatira zinthu za m’Baibulo zimene ndinaphunzira ndili mwana chinachitika pamene ndinali ndi zaka 11. Panthaŵi imeneyo n’kuti nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse itayambika, ndipo ana kusukulu ankafunika kuti azichitira sawatcha mbendera. Pophunzira Baibulo ndinazindikira kuti kuchita zimenezo n’kulambira komwe, choncho ndinakana kutero. Zimenezi zinachititsa kuti andichotse sukulu kwa miyezi isanu ndi umodzi.
Komabe, sukulu ndinadzamaliza, ndipo m’mwezi wa March 1947, ndinasonyeza kudzipatulira kwanga kwa Yehova Mulungu mwa kubatizidwa m’madzi. Patatha miyezi isanu ndi umodzi ndinakhala mpainiya, munthu wolengeza uthenga wabwino nthaŵi zonse. Poyamba, ndinkatumikira cha kummwera kwa chigawo cha Saskatchewan, n’kumalalikira kwa alimi a mbewu ndi a ziŵeto m’dera lalikulu kwambiri limeneli. M’chilimwe ndinkayenda pa hatchi, ndipo m’chisanu ndinkayenda pa ngolo yokokedwa ndi hatchi yotchingidwa bwinobwino ndipo tinkangoitcha kuti kathole. M’ngolomo ndinkaikamo mbaula yamakala kuti muzikhala motenthera bwino, choncho ndinkachita zinthu mosamala kuti ngoloyo isagubuduke.
Anthu a kumidzi anali aubwenzi ndiponso odziŵa kulandira alendo. Ndikafika pakhomo pawo madzulo kwambiri, nthaŵi zambiri ankandipempha kuti ndigone konko. Sindiiwala n’komwe nkhani zolimbikitsa za m’Baibulo zimene tinkakambirana ndikagona konko! Banja la a Peterson linali limodzi mwa mabanja amene anagwirizana nawo uthenga wabwino titakambirana usiku wonse. Earl ndi amayi ake anadzakhala Mboni za Yehova zolimbikira kwabasi.
Kutumikira ku Quebec
Mu 1949, ndinavomera pempho lofuna apainiya oti akathandize pa ntchito yolalikira m’chigawo cha ku Quebec. Pafupifupi apainiya 200 ochokera m’dera la kumadzulo m’dziko la Canada anavomera pempholi. Apainiyaŵa anafika mumzinda wa Montreal m’mwezi wa September, ali okonzeka kupita kulikonseko kumene angauzidwe m’chigawo cha Quebec. Panthaŵiyi n’kuti mtsogoleri wa Akatolika dzina lake Maurice Duplessis akulamulira. Iyeyu analumbira kuti adzatha a Mboni onse m’chigawochi.
Nthaŵi imeneyo tinali otanganidwadi ndipo panali zosangalatsa komanso zovuta zambiri. Tinali kuphunzira chinenero cha Chifalansa komanso kumangidwapo ndi kukumanapo ndi zipolowe ndiponso kujejemetsedwa pa misonkhano yathu ikuluikulu ya Chikristu ndi anthu osokoneza kwambiri. Komabe, zinthu za chisokonezo zoterezi sizinandiopse kapena kundijejemetsa pa ntchito yanga yotumikira Mulungu. Makolo anga anali atandiphunzitsa mokwanira kukonda zabwino ndiponso kukhala ndi chidaliro chakuti ntchito ya padziko lonse yolalikira imene Yesu analosera idzakwaniritsidwa, ngakhale ena akhale otsutsa bwanji.—Mateyu 24:9, 14.
Ndili ku Quebec, ndinakumana ndi Emily
Hawrysh, yemwe anali mpainiya wokhulupirika wa ku Saskatchewan. Kungoyambira pamene tinakwatirana pa January 27, 1951, Emily wagwira nane ntchito mokhulupirika ndiponso wakhala akundilimbikitsa. Popeza kuti cholinga chathu chinali choti tizichita kwambiri utumiki, tinalemba kalata yopempha kuti tikaloŵe nawo Sukulu ya Gileadi ya Watchtower Yophunzitsa Baibulo, komwe anthu amakhalako kwa miyezi ingapo akuphunzira za utumiki wa umishonale, ndipo anatilola kutero. Tinali m’kalasi ya Gileadi ya nambala 20, ndipo tinamaliza maphunziro athu m’mwezi wa February mu 1953.Poyembekezera makalata athu oloŵera mu Africa kuti atuluke, anatipempha kuti tikathandize mipingo ya Mboni za Yehova m’zigawo za Alberta ndi Ontario, ku Canada. M’masiku amenewo poyendera mipingo, tinkayenda pa galimoto zokwera aliyense. Pachifukwachi tinaphunzira kusalira zambiri m’moyo wathu ndipo tinkanyamula katundu wathu yense m’sutikesi. Patangotha miyezi yochepa, makalata athu oyendera ndiponso oloŵera m’dziko lina atatuluka, tinanyamuka ulendo wathu wopita ku Southern Rhodesia, kumene masiku ano amati ku Zimbabwe.
Kuyamba Kuzoloŵera Moyo wa ku Africa
Mmene miyezi isanu imatha titafika kumeneko, tinali titapatsidwa ntchito yoyendera magulu a Mboni za Yehova ku Zimbabwe komanso ku Botswana ndi madera a kummwera kwa Northern Rhodesia (kumene panopa amati ku Zambia). Tili ku Sukulu ya Gileadi tinalimbikitsidwa kuti tisamayerekezere utumiki wa m’dziko limene tikutumikiramo ndi wa m’dziko la kwathu ndiponso kuti tizikumbukira kuti tingathe kuphunzirapo kanthu pa chilichonse chimene tingakumane nacho. Mawu anzeru otereŵa anatithandiza kusintha zimene tinkaganiza. Mpakana panopa, ine ndi Emily timavomereza mawu aja akuti: “Muzipezerapo mwayi pa zilizonse zimene zingakugwereni; chifukwa mwina sizingakuonekereninso.”
Kulikonse kumene tinkapita, tinkayenda pa sitima ya pamtunda, pa basi, pa galimoto, kapena pa njinga, mwachidule tingoti chilichonse chimene tikanatha kuchipeza. Ngakhale kuti zimenezi zinali zotopetsa kale n’kale, panalinso zina zimene zinkapangitsa kuti zitivute kugwiritsira ntchito mawu aja akuti “muzipezerapo mwayi pa zilizonse zimene zingakugwereni.” Kwa zaka ziŵiri zoyambirira, Emily sankayenda nane limodzi m’madera a mafuko a kumeneko chifukwa cha malamulo oletsa zimenezo. Motero, mkazi wanga yemwe ndinali nditangom’kwatira kwa zaka zochepa zokha ankatsala yekhayekha m’matauni a kufupi ndi kumathero kwa njanji, komwe nthaŵi zambiri kunkakhala kopanda a Mboni ena. Chikhulupiriro cha Emily, kulimba mtima kwake, ndiponso kutsimikiza kwake kuchita zinthu, zinandigometsa ndipo zinapangitsa kuti ndizim’konda kwambiri, komanso kuwonjezera pamenepo, zinabweretsa zipatso za Ufumu m’maderaŵa.
Emily ankangoti akapeza munthu womusunga wakumeneko, nthaŵi yomweyo ankayamba kulalikira m’deralo mpaka ine nditabwera kuchokera m’dera la fuko limene ndinapita. Nthaŵi zina ankatha kutumikira ali yekha kwa mwezi wonse. Ankalimbikitsidwa ndiponso kukhala wotetezeka podalira dzanja lamphamvu la Yehova, ndipo utumiki wake unabala zipatso. Nthaŵi inayake Rita Hancock analola kuphunzira za choonadi cha m’Baibulo, kenaka mwamuna wakenso. Mwamunayu anakhala mbale wokhulupirika ndipo anali mkulu wachikristu mpaka imfa yake. Panopa m’matauni ena mmene Emily anadzala mbewu za choonadi cha m’Baibulo muli mipingo yamphamvu.
Kuchereza Alendo kwa Anthu a ku Africa Komanso Luso Lawo
Chimene chinandichititsa chidwi kwambiri panthaŵi imene ndinali m’madera a mafuko a m’dzikomo, ndicho mmene Mboni za ku Africa zimakondera gulu la Yehova ndi nthumwi zake zimene zimagwira ntchito yoyendera mipingo. Abale achikristu ameneŵa ankandisamala bwino kwambiri. Lolemba lililonse ndinkachoka kumalo ena a msonkhano n’kupita kwinanso. Kumene ndipiteko ankandimangira nyumba yaudzu, ndipo zimenezi zinkandikumbutsa nyumba yathu kumudzi kwathu ku Saskatchewan. Ankagoneka udzu wambiri wofika mpaka masentimita 30 kuchindikala kwake n’kuyalapo nsalu, ndipo limeneli ndilo linali bedi langa.
Kaŵirikaŵiri misonkhano imene tinkachitira m’madera ameneŵa tinkaichitira ku nkhalango. Anthu osonkhana ankalambula malowo, n’kusiya mitengo ya masamba ambiri kuti pakhale mthunzi. Pansi ankaikapo mitolo yaudzu yomangidwa bwino ili m’mizeremizere kuti anthu akhalire. Akatha zonsezi, ankamanga mpanda wa tsekera kuzungulira malowo kuti akhale otchinga bwino. Nthaŵi zonse mawu a nthetemya opokolezana mosaiwalika amene abale ndi alongo athu a ku Africa ankaimba m’nkhalangomu potamanda Yehova ankandifika pamtima kwabasi.
Zosaiwalika
Ndili m’kati mwa utumiki wangawu, ndinakumana ndi Gideon Zenda, yemwe anali wamkulu wa oyang’anira masukulu a mishoni a tchalitchi cha
Anglican. Gideon anaphunzitsidwa ndi tchalitchi chimenechi mpakana ku yunivesite. Ngakhale zinali choncho, iye anali asanayankhidwe mokhutiritsa mafunso a nkhani za m’Baibulo amene anali nawo. Choncho anapempha kuti ndikumane naye pamodzi ndi anzake ochuluka ndithu kuti ndidzayankhe mafunso ameneŵa. Anthu okwanira 50 anasonkhana nthaŵi imeneyo, ndipo anthuwo anali akuluakulu oyang’anira masukulu, aphunzitsi aakulu, ndi aphunzitsi ena. Gideon ndiye anali tcheyamani wa zokambirana zathuzo. Tinakambirana bwinobwino nkhani iliyonse payokhapayokha. Pankhani iliyonse ndinkayankhula kwa mphindi 15 kenaka n’kuyamba kuyankha mafunso. Kukambiranako kunatenga maola angapo ndithu.Zimene zinadzachitika chifukwa chokhala ndi msonkhano wosayembekezereka ngati umenewu n’zakuti Gideon, banja lake, ndiponso ochuluka mwa anzake aja, onseŵa anakhala atumiki a Yehova odzipatulira, ndiponso obatizidwa. Bishopu wakumeneko anawachotsa ntchito m’masukulu awo a Anglican. Komabe, onseŵa sanachite nazo mantha ndipo anakhalabe olimbikira mu utumiki wa Yehova, moti ena anasankha kuchita utumiki waupaniya.
Zimene Zinachitika Titaonetsa Filimu Yosangalatsa
Mu 1954, Mboni za Yehova zinapanga filimu ya mutu wakuti The New World Society in Action. M’chaka chotsatira, lamulo lija loletsa mkazi kuyenda ndi mwamuna wake m’madera a mafuko a m’dzikolo linathetsedwa. Zimenezi zinam’masula Emily kuti aziyenda nane m’madera ameneŵa. Panthaŵiyi n’kuti atatipatsa galimoto, jenereta ya magetsi, ndiponso kanema kuti tionetse filimuyo m’madera onsewo. Anthu ambiri anali asanaonepo kanema chibadwireni, choncho mmene timaonetsa kanemayi, ambiri anachita nayo chidwi kwabasi. M’kanemayo anasonyezamo mwatsatanetsatane mmene amasindikizira mabaibulo ndi mabuku ofotokoza za m’Baibulo pa makina athu osindikizira aakulu mumzinda wa Brooklyn, ku New York.
Mu filimuyi ankasonyezanso ubale wapadziko lonse wa Mboni za Yehova pozionetsa zikulambirira pamodzi ku Yankee Stadium, mumzinda wa New York, mu 1953. Anthu a ku Africa ameneŵa anali asanaonepo zoterozo, kuti anthu ochokera m’mafuko osiyanasiyana n’kumakhala ogwirizana komanso n’kumakondana choncho. Kanema imeneyi inalimbikitsa mabanja ambiri a ku Zimbabwe kuyamba kuphunzira Baibulo ndi kuyamba kusonkhana ndi a Mboni. Aphunzitsi aakulu ambirimbiri m’dziko lonselo amene anaona kufunika kophunzitsa ana awo asukulu poonerera kanemayo ankatipempha kuti tikaonetse kanemayi.
Tsiku lina usiku kwambiri ndinadzutsidwa ndi a Mboni ena amene anapempha kuti ndiwaonetse filimuyi. Sindinakhulupirire kuti anthu pafupifupi 500 anali atayenda wapansi kwa maola ochuluka kuti adzaonerere nawo filimuyi. Iwo anali atamva kwa anthu ena kuti ndili m’derali ndipo ndakhala ndikuonetsa filimuyi. Mmene chikhamu cha anthuŵa chinkachoka, n’kuti chigulu chinanso cha anthu okwana 300 chitafikanso. Choncho ndinaonetsanso filimuyi. Mmene anthu omalizira kuionerera ankachoka, n’kuti nthaŵi ili 3 koloko ya kum’bandakucha! Kwa zaka zoposa 17, ku Zambia kokha, anthu oposa wani miliyoni anaonerera filimu yolimbikitsayi!
Kutumizidwa Kumadera Atsopano mu Africa
Titatumikira kwa zaka zoposa zisanu ndi theka tili m’dziko la Zimbabwe, anatitumiza ku South Africa. Apa ndiye kuti tinayenera kuphunzira chinenero cha Chiafirikanzi. Kenako tinaphunziranso Chisutu ndi Chizulu. Kukhala okhoza kuphunzitsa anthu Mawu a Mulungu mu zinenero zinanso kunatithandiza kwambiri kuti zinthu zizitiyendera bwino mu utumiki ndipo mumtimamu tinkamva kuti tikuchita zakupsa ndithu.
Chakumayambiriro kwa m’ma 1960 anatitumiza kumadera a kummwera kwa Africa kuti tizikayendera mipingo. Kwa zaka 27 zotsatira, tinayendera madera ambiri kwabasi a ku Lesotho, Namibia, South Africa, ndi Swaziland komanso a ku zisumbu za Ascension ndi St. Helena zimene zili ku South Antlantic Ocean. Mtunda wonse umene tayendapo potumikira abale ndi alongo athu achikristu ngwa makilomita masauzande ambirimbiri. Chikhulupiriro chawo ndi kukhulupirika kwawo m’nthaŵi zovuta zatilimbikitsa kuti tisasiye utumiki wathu.
Mwachitsanzo, ndinadziŵanapo ndi a Mboni a ku Swaziland amene sanalolere kuchita zosemphana ndi chikhulupiriro chawo Mfumu Sobhuza yachiŵiri itamwalira. Popeza kuti iwo anakana kuchita nawo miyambo yosagwirizana ndi Malemba imene inachitika pamaliro a munthu wolemekezeka ameneyu, anachotsedwa ntchito ndipo analibe ufulu wochita zinthu
ngati nzika za dzikolo. Ngakhale kuti zaka zambiri zinadutsa akumanidwa zambiri ndiponso akuvutika, iwo sanasiye n’komwe chikhulupiriro chawo. Kudziŵana ndiponso kulankhulana pamaso m’pamaso ndi abale ndi alongo achikristu abwinoŵa ndi mwayi wanga waukulu womwe umandipangitsa kuthokozabe Yehova nthaŵi zonse.Ndiye palinso Philemon Mafereka, mpainiya wa m’mudzi mwa Mokhotlong, ku Lesotho. Mudziwu uli m’mapiri, ndipo ngokwera mamita 3,000. Chifukwa kunalibe magalimoto, iye ndi mkazi wake wokondeka, ana awo aŵiri, ndi anthu ena anayi amene ankafuna kukabatizidwa, anayenda wapansi mtunda wa makilomita oposa 100 kuti akafike komwe kunali msonkhano umene unachitikira pamalo okwera mamita 1,200. Njirayi inali yotsetsereka kwambiri m’malo ochuluka. Akamakwera ndi kutsetsereka zitunda ankachita kukwaŵa ndipo anadutsa makwawa ndi mitsinje yambiri.
Pobwerera kwawo msonkhano utatha, ananyamula mabuku 100 akuti Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya. Iwo ankafuna kuti akagaŵire mabukuŵa anthu a kumudzi kwawo ku Mokhotlong. Komano mabuku onseŵa anathera m’njira chifukwa chokumana ndi anthu amene ankachita chidwi ndi mabuku ofotokoza za m’Baibuloŵa. Timaona kuti ndi mwayi wathu, ine ndi Emily, kuona maso ndi maso kulimbikira ndiponso kudzipereka kwa abale ndi alongo achikristu ngati Philemon ndi mkazi wake, ndipo mpakana pano sitiiwala zimenezi.
Nthaŵi zina, tinkakumana ndi njoka zoopsa, monga mibobo, komanso madzi osefukira ndi zinthu zinanso zoopsa. Zinthu zoterezi, ngakhale kuti panthaŵiyo zinali zochititsa mantha, n’zosanunkha kanthu n’komwe tikayerekezera ndi madalitso komanso zinthu zosangalatsa zimene tapeza pogwira ntchito yotumikira Yehova. Tinazindikira kuti iye sataya anthu ake okhulupirika.
Emily akadwala kwambiri, Yehova ankatipatsa nzeru yoti tithe kuchita zinthu mosapupuluma. Kusintha zakudya zimene tinkadya ndiponso kuchita zinthu zaukhondo kunkathandiza kuti azichira mwamsanga. Tinakonza kanyumba pa galimoto yathu kuti Emily azikhala motetezeka tikamayenda, ndipo mapeto ake, anachiriratu.
Kubwerera ku Canada
Mu 1988, titatha zaka 35 tikuchita umishonale mu dziko lochititsa chidwi la Africa, anatitumizanso ku Canada. Kenaka mu 1991, ndinayambiranso kutumikira monga woyang’anira woyendayenda. Patatha zaka zisanu ndi zitatu ndinadwala sitiroko. Ngakhale kuti kungoyambira nthaŵi imeneyi zochita zanga zabwerera m’mbuyo kwambiri, ndimasangalalabe kuti ndine mkulu pa mpingo umodzi mwa mipingo ya muno mumzinda wa London, ku Ontario.
Panopa ndimakhutitsidwa kwambiri ndikakumbukira nthaŵi imene ndinayamba upainiya zaka pafupifupi 56 zapitazo, ndikumayenda nditakwera hatchi kummwera kwa chigawo cha Saskatchewan. Ndimakondwa kwambiri kuti Bambo ankalimbikira kutiphunzitsa kuganiza ngati anthu auzimu, kuti tisamachite mantha poikira kumbuyo choonadi ndi chilungamo. Anandiphunzitsa Mawu a Mulungu, omwe anandipezetsa moyo wokhutiritsa. Zimene ndinatengera kwa Bambo zimenezi zandithandiza m’moyo wanga wonse. Sindidzalola kuti china chilichonse m’dzikoli chindilepheretse kutumikira Yehova.
[Chithunzi patsamba 27]
Apa ndi mu 1949, ndipo m’banja mwathu tinalipo ana nayini, Mayi anyamula chitsirizira. Ine ndine uyo amene waima kumbuyo kwawoko
[Chithunzi patsamba 28]
Ndinakonza “kathole” kameneka kuti kazindithandiza mu utumiki wanga
[Chithunzi patsamba 28]
Akazi amene anamangidwa chifukwa cholalikira ku Quebec
[Chithunzi pamasamba 30, 31]
Ndinaphunzitsa nawo oyang’anira oyendayenda aŵa ku Zimbabwe
[Chithunzi patsamba 31]
Tinamanga kanyumba aka pa galimoto yathu kuti Emily azikhalamo akadwala
[Chithunzi patsamba 31]
Chithunzi chaposachedwapa ndili ndi Emily