Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Magazini Yoyenera Kupukusidwa’

‘Magazini Yoyenera Kupukusidwa’

‘Magazini Yoyenera Kupukusidwa’

DAVID akuphunzira za malamulo pa yunivesite ya ku Nigeria yotchedwa Obafemi Awolowo. Chaposachedwapa analembera kalata ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ya kumeneko kuti: “Nthaŵi ndi nthaŵi ndimakapereka Galamukani! kwa pulofesa wina wa zaka 70 wolemekezeka, yemwe ali m’dipatimenti yophunzitsa zamalamulo. Tsiku lina mmaŵa atalandira magazini atsopano, anauza munthu amene anali mu ofesi yake kuti: ‘Mabuku ena n’ngofunika kuwalawa, ena kuwameza, koma ena oŵerengeka ayenera kutafunidwa ndi kupukusidwa. Koma Galamukani! ndi magazini yoyenera kutafunidwa ndi kupukusidwa.’”

Nthaŵi inanso atatuluka mu ofesi ya pulofesayo, David ananena kuti anamva pulofesayo akunena za ubwino wa Galamukani! kwa munthu winanso. Iye anati: “Pulofesayo ankayankhula motamanda kwambiri nkhani za mu Galamukani! kuti zimakhala zoti azifufuza mozama kwambiri asanafike pozilemba komanso kuti zimakhala zonena chilichonse mwatsatanetsatane ndiponso mosapsatira. Ndinamumva akunena kuti: ‘Ndimaŵerenga magaziniŵa mosamala kwambiri. Mulungu ayenera kuti ndiye amene amapatsa nzeru anthu amene amalemba nkhani zabwino kwambiri chonchi.’”

Mu Galamukani! mumakhala nkhani zosiyanasiyana zophunzitsa anthu. Chachikulu n’chakuti nkhanizo zimalimbikitsa anthu kudalira lonjezo la Mlengi limene lili m’Baibulo lakuti kudzakhala dziko latsopano lamtendere limene lidzaloŵe m’malo mwa dziko lilipoli. Kabuku ka masamba 32 kakuti Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? kamafotokoza bwino za cholinga cha Mulungu chimenecho, ndipo kamatidziŵitsa zimene zili m’Baibulo kuti tione zomwe tiyenera kuchita kuti Mulungu atiyanje. Mungathe kuitanitsa kabuku kanu polemba zofunika m’kabokosi kali pamunsika ndi kukatumiza ku adiresi ili pomwepoyo kapena ku adiresi imene ili patsamba 5 la magazini ino.

□ Nditumizireni kabuku kakuti Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?

□ Chonde nditumizireni munthu kuti ayambe kuchita nane phunziro la Baibulo lapanyumba laulere.