Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Okondedwa Anu Akakhala Achikhulupiriro China

Okondedwa Anu Akakhala Achikhulupiriro China

Lingaliro la Baibulo

Okondedwa Anu Akakhala Achikhulupiriro China

KAFUKUFUKU wina anasonyeza kuti padziko lonse pali zipembedzo ndi magulu a mpatuko zopitirira 10,000. M’dziko lina anthu akuluakulu 16 pa 100 alionse, anayamba asiyapo chipembedzo china n’kuloŵa china. Ndiyetu n’zosadabwitsa kuti pamakhala kusagwirizana pankhani ya zikhulupiriro m’zipembedzo pakati pa anthu a pachibale ngakhalenso anthu ogwirizana. Nthaŵi zina zimenezi zimachititsa kuti anthu afike mpaka podana. N’chifukwa chake pali funso lakuti, Kodi Akristu ayenera kumaona bwanji okondedwa awo achikhulupiriro china?

Mgwirizano Wapadera

Mwachitsanzo, taganizirani zimene Baibulo limanena pankhani ya ubale umene umakhalapo pakati pa makolo ndi ana awo. Palibe malire a msinkhu wa munthu amene anaikidwa pa lamulo limene lili pa Eksodo 20:12 lakuti “uzilemekeza atate wako ndi amako.” Moti n’zosachita kufunsa kuti pamene Yesu ankakamba za lamulo limeneli, lomwe lili pa Mateyu 15:4-6, ankakamba za kulemekeza kumene ana akuluakulu angachitire makolo awo.

Buku la m’Baibulo la Miyambo limachenjeza kuti sibwino kuchita zinthu zonyoza makolo. Lemba la Miyambo 23:22 limatilangiza kuti “usapeputse amako atakalamba.” Kuwonjezeranso pamenepo, lemba la Miyambo 19:26 limachenjeza mwamphamvu kuti munthu “wolanda za atate, ndi wopitikitsa amayi, ndiye mwana wochititsa manyazi ndi wogwetsa nkhope.”

Malemba amanena momveka bwino kuti sitiyenera kunyoza makolo athu. Sikuti makolo athu akakhala osagwirizana ndi chipembedzo chathu ndiye kuti palibenso ubale pakati pa ifeyo ndi iwowo. Mfundo za m’Baibulo zimenezi zimagwiranso ntchito chimodzimodzi kwa abale athu enieni ndiponso kwa munthu ndi mkazi wake kapena mwamuna wake. Ndithudi, mogwirizana ndi kakhalidwe kabwino ndiponso Malemba, Akristu ndi ofunikabe kukonda achibale awo.

M’pofunika Kumaganiza Bwino

Inde, Baibulo limachenjeza kuti sibwino kuyanjana ndi anthu okonda zoipa, ndipo anthuŵa angakhale achibale enieni a munthu. (1 Akorinto 15:33) Atumiki a Mulungu ambirimbiri akale analimbikira kuchitabe zabwino ngakhale kuti makolo awo sanagwirizane nazo. Izi ziyenera kuti n’zimene ana aamuna a Kora anachita. (Numeri 16:32, 33; 26:10, 11) Akristu oona sayenera kuchita zinthu zosemphana ndi chikhulupiriro chawo kuti asangalatse ena, ngakhale atakhala achibale awo enieni.—Machitidwe 5:29.

Nthaŵi zina makolo kapena okondedwa ena amatsutsa kwambiri zimene Mkristu wina amakhulupirira. Ena angafike mpaka podana ndi Chikristu choona. Zikafika poterepa Akristu amachita zinthu zimene zingathandize kuti ateteze moyo wawo wauzimu. Moyenerera Yesu anati: “Apabanja ake a munthu adzakhala adani ake. Iye wakukonda atate wake, kapena amake koposa Ine, sayenera Ine, ndipo iye wakukonda mwana wake wamwamuna, kapena wamkazi koposa Ine, sayenera Ine.”—Mateyu 10:36, 37.

Komano kaŵirikaŵiri Akristu satsutsidwa mochita kudetsa nkhaŵa ndi okondedwa awo. Zimangokhala kuti achibalewo samva zimene Baibulo limaphunzitsa mofanana ndi iwowo. Malemba Oyera amalimbikitsa otsatira Kristu kuti azichita zinthu “mofatsa” ndiponso mwa “mantha” kapena kuti mwa ulemu waukulu kwa osakhulupirira. (2 Timoteo 2:25; 1 Petro 3:15) Moyenerera Baibulo limalangiza kuti: “Kapolo wa Ambuye sayenera kuchita ndewu, komatu akhale woyenera, waulere pa onse.” (2 Timoteo 2:24) Mtumwi Paulo analangizanso Akristu kuti “asachitire mwano munthu aliyense, asakhale andewu, akhale aulere, naonetsere chifatso chonse pa anthu onse.”—Tito 3:2.

Osawaiwala Ndipo Muzisonyeza Kuti Mumawakonda

Pa 1 Petro 2:12, Akristu akulimbikitsidwa kuti: “Mayendedwe anu mwa amitundu [osakhulupirira] akhale okoma, kuti . . . akalemekeze Mulungu pakuona ntchito zanu zabwino.” Kaŵirikaŵiri, okondedwa athu achikhulupiriro chosiyana ndi chathu amaona mmene Baibulo latithandizira kusintha pa moyo wathu. Musaiwale kuti anthu ambiri amene analibe chidwi kapena amene ankatsutsa kumene choonadi cha m’Baibulo anasintha maganizo awo. Kwa anthu ena zikhoza kutheka kuti zatenga zaka zambiri akumangoyang’anitsitsa khalidwe labwino la mkazi kapena mwamuna wawo kapenanso la mwana wawo kuti afike poyamba kufufuza chifukwa chake ali ndi khalidwelo. Anthu akamakana kumvera choonadi cha m’Baibulo, zisakhale choncho chifukwa chakuti ananyalanyazidwa ndi wachibale wawo yemwe ndi Mkristu.

Inde, n’zoona kuti moyo wa anthu umasiyanasiyana, ndipo Akristu ena a Mboni amakhala kutali ndi makolo awo. Kungakhale kovuta kuwayendera kaŵirikaŵiri monga mmene amafunira. Koma okondedwa athu angatsimikize kuti timawakonda tikamawalembera makalata, kuwaimbira foni, kapena kuyankhulana nawo m’njira zina nthaŵi zonse. Anthu ambiri amene si Akristu oona amakonda makolo awo ndi achibale ena ndipo amayankhulana nawo nthaŵi ndi nthaŵi mosaganizira zoti ndi osiyana zikhulupiriro. Ndiye ngati zili choncho, kodi Akristu a Mboni n’kulekeranji kutero?

[Chithunzi patsamba 22]

Kuyankhulana ndi okondedwa anu kungawatsimikizire kuti mumawakonda