Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Anthu Amatengera Mmene Mlengi Analengera Zinthu

Anthu Amatengera Mmene Mlengi Analengera Zinthu

Anthu Amatengera Mmene Mlengi Analengera Zinthu

Kodi zimatheka bwanji kuti magolobo a magetsi omwe ndi opyapyala kwambiri asamaphwanyike powakanikiza kuti alowe moikamo magolobo? Malinga ndi zimene linanena buku lotchedwa How in the World?, yankho lake ndi mmene golobolo linapangidwira, limene anatengera “mmene dzira linapangidwira.” Ngakhale kuti chakunja cha dzira n’chopyapyala kwambiri, mazira saphwanyika ndi kulemera kwa mbalame ikamakhalira. Zimenezi zili choncho chifukwa mmene dzira linapangidwira limakhala lamphamvu moti silingaphwanyike. (Chakunja cha dzira chochindikala chingalepheretse kamwana kuti katuluke m’dzira.) Potengera mmene Mlengi analengera zinthu, magolobo ndi ozungulira moti akakanikizidwa, “sapanikizika malo amodzi okha koma kukanikizako kumapita mbali zonse za golobolo.” Choncho, monga mmene zilili ndi dzira, kukanikiza kwamphamvu sikukhala malo amodzi, ndipo golobo siliphwanyika. Anthu adziŵa zambiri pophunzira chilengedwe!