Kodi Ndingathe Bwanji Kukamba Nkhani Bwino Pagulu?
Achinyamata Akufunsa Kuti . . .
Kodi Ndingathe Bwanji Kukamba Nkhani Bwino Pagulu?
“Ndinkangoona ngati anthu akuona zonse zimene ndikulakwitsa ndiponso kuti ndikuchita mantha. Ndinkalephera kuganizira bwino zimene ndinali kuyankhula. Ndinkangoona ngati anthuwo akundiseka mumtima mwawo,” anatero Sandy. *
HOLO ya sukulu yadzaziratu. Kenaka dzina lanu likumveka pa chokuzira mawu, ndipo nthaŵi yomweyo anthu onse maso angoti dwii pa inu. Kamtunda kochoka pamene mwakhalapo kuti mukafike kutsogolo, kakuoneka ngati ndi chimtunda chachitali. M’manja mwayamba thukuta, maondo angoti zii kulobodoka, ndipo mwadzidzidzi milomo yauma gwaa. Kenaka mwangozindikira kuti chithukuta chikuyenderera kumaso. N’zamanyazi bwanji! Mukudziŵa kuti palibe yemwe akufuna kukuwomberani ndi mfuti, koma mmene mukumvera, zikungokhala ngati kuti wina akufuna kukuwomberanidi.
Tisakane ayi: Ambirife zokamba nkhani pagulu zimatipatsa chinthenthe. (Yeremiya 1:5, 6) Anthu ena anafika ponena kuti amaopa kwambiri kukamba nkhani pagulu kuposa kufa! Kaya inuyo mumaona bwanji za nkhani imeneyi, pali zifukwa zabwino zoti mukhale ndi chidwi ndi kukamba nkhani pagulu. Tiyeni tione zina mwa zifukwa zimenezo ndiponso mmene mungakhalire munthu wotha kukamba nkhani bwinobwino pagulu.
Mukauzidwa Kuti Mudzayankhulepo
“Kuyankhula pagulu ndi luso lofunika kwa aliyense.” Amatero ponenera maphunziro enaake ophunzitsa anthu kuyankhula pagulu. Inde, kaya mufune kapena musafune, nthaŵi inayake mudzafunikabe kuyankhula pamaso pa anthu. Ndiponsotu, m’masukulu ambiri ana amawaphunzitsa kuyankhula pagulu. Mtsikana wina dzina lake Tatiana anati: “Pali nthaŵi zambiri zimene ndinkayankhula kutsogolo kwa anzanga m’kalasi.” Nthaŵi zambiri ana asukulu amafunika kukhala okonzeka kupereka lipoti linalake, kufotokoza za m’buku linalake, kukamba nkhani inayake pogwiritsira ntchito wailesi ndi vidiyo kapena kompyuta, ndiponso kuchita mtsutso.
Kenaka mukadzayamba ntchito, mwina mudzafunika kuphunzitsa anzanu a kuntchito zinthu zinazake, kufotokoza zinthu mwatsatanetsatane kwa kasitomala wanu, kapena kufotokoza ndondomeko yoyendetsera ndalama kwa akuluakulu. Kunena mwachidule, luso loyankhula bwino ndi lofunika kwambiri m’ntchito zambiri, monga za utolankhani, umanijala, kukhala woyankhulira kampani, ndiponso za malonda.
Nanga bwanji ngati mukufuna ntchito ya ulebala kapena ya ukalaliki? Kudziŵa kuyankhula bwino poyankha mafunso ofuna kuona ngati muli woyenerera kulembedwa ntchitoyo, kungathandize kuti akulembeni ntchitoyo koma ngati mukulephera kuyankhula bwino mwina sangakulembeni. Ndiye mukayamba ntchitoyo, zingakuthandizeni ngati mumayankhula bwino. Corrine atamaliza maphunziro ake anagwira ntchito yoperekera zakudya kwa zaka zitatu. Iye anati: “Ukamadziŵa kuyankhula bwino, amakuona kuti ndiwe
munthu wokhwima maganizo amene akhoza kukupatsa udindo waukulu. Zikhoza kutheka mpaka kukupatsa ntchito yabwinopo, kukuwonjezera malipiro, kapena kungokupatsa ulemu waukulu.”Komanso, Akristu achinyamata nthaŵi zambiri amayankhula pamaso pa anthu ena monga mbali ya kupembedza kwawo. (Ahebri 10:23) Taneisha ananena kuti: “Ndi bwino kukhala munthu womasuka kwambiri poyankhula.” Iye ananenanso kuti: “Tili ndi mwayi wapadera wolalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu.” (Mateyu 24:14; 28:19, 20) Mu mpingo ndiponso polalikira kwa anthu, Akristu achinyamata sangathe ‘kuleka kuyankhula zimene anaona ndi kzimva.’—Machitidwe 4:20; Ahebri 13:15.
Motero kuphunzira kuyankhula bwino kungakuthandizeni m’njira zambiri. Ngakhale zili choncho, mukhozabe kukhala ndi nkhaŵa mukaganizira zoti muimirire pagulu. Kodi chilipo chimene mungachite kuti muthetse manthawo? Inde.
Kuthetsa Mantha
“Kuti muziyankhula bwino pagulu, si zolira kuti mukhale katswiri kapena kuti munthu wosalakwitsa kalikonse ayi,” anatero Dr. Morton C. Orman, yemwe ndi katswiri wodziŵa zinthu zoyambitsa nkhaŵa ndiponso wodziŵa kukamba nkhani pagulu. Iye anapitiriza kuti: “Chinsinsi chokamba nkhani pagulu ndi ichi: auzeni anthuwo zinthu zaphindu.” Zimenezi zikutanthauza kuti, muziganizira kwambiri za uthenga umene mukufuna kuwauza, osati za inuyo kapena zimene mukuopa. Anthu ena a m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino ankaganiza kuti mtumwi Paulo sanali munthu wodziŵa kuyankhula bwino, koma chifukwa chakuti nthaŵi zonse iye ankakamba zinthu zaphindu, anakhalabe wothandiza kwambiri. (2 Akorinto 11:6) N’chimodzimodzi inunso, ngati mutakamba zinthu zimene mukukhulupiriradi kuti n’zaphindu, mantha anu angathe mosavuta.
Ron Sathoff, yemwe amadziŵanso kwabasi kukamba nkhani ndiponso kuphunzitsa anthu kukamba bwino nkhani, anatchula mfundo iyi: Nkhani yanu musaitenge ngati muli pa chionetsero. Muziitenga ngati mukukambirana ndi winawake. Inde, yesetsani kuyankhula ndi anthu amene akumvera nkhani yanuyo, osati monga gulu ayi, koma mmodzi ndi mmodzi, kumangoyankhula ngati mmene mumayankhulira ndi munthu aliyense. Omvera anu asonyezeni kuti mukuwaganizira, ndipo ayankhuleni mmene mumayankhulira nthaŵi zonse. (Afilipi 2:3, 4) Mukamayankhula ngati mukukambirana nawo nkhani, m’pamenenso mungakhale womasuka kwambiri.
Chifukwa chinanso chimene anthu ambiri amakhalira ndi nkhaŵa n’chakuti amakhala akuopa kuchita manyazi kapena kuneneredwa zoipa ndi anthu amene akuwamvera. Lenny Laskowski, yemwe amadziŵa kukamba nkhani pagulu ndi kuphunzitsa anthu kukamba bwino nkhani, anati tisaiwale kuti kaŵirikaŵiri anthu akamamvetsera nkhani iliyonse amafuna kuti iyende bwino. “Amakufunirani zabwino, safuna kuti zikulakeni ayi,” anatero Laskowski. Ndiye musaganize zambiri. Ngati n’kotheka, anthu ena amene amvere nkhani yanu akamafika, yesani kuwapatsa moni. Muziwaona kuti ndi anzanu, osati adani anu ayi.
Kumbukiraninso kuti, si kuti mantha onse ndi oipa ayi. Katswiri wina anati: “Mosiyana ndi zimene anthu ambiri amakhulupirira, kukhala ndi mantha ndi kwabwino ndipo kumathandiza pokamba nkhani.” N’chifukwa chiyani zili choncho? N’chifukwa chakuti Miyambo 11:2) Akatswiri ambiri a maseŵera olimbitsa thupi, a zoimbaimba, ndiponso a zisudzo amaona kuti akakhala n’timantha pang’ono m’pamene amachita bwino ntchito yawo, ndipo zimenezi zikhoza kukhalanso zoona kwa okamba nkhani pagulu.
penapake kukhala ndi mantha kumasonyeza kudzichepetsa, ndipo kutero kungakuthandizeni kuti musafike podzithemba. (Zina Zimene Zikhoza Kukuthandizani
Potsatira mfundo zotsatirazi ndi zinanso, Akristu ena achinyamata pakali pano afika kale poyamba kuzoloŵera ndipo akukamba nkhani bwino kusukulu, kuntchito, ndiponso m’mipingo yawo. Onani ngati mfundo zawo zina zochepa chabezi zingakuthandizeni.
Jade: “Nkhaniyo muziikamba mmene inuyo mumayankhulira. Khalani wokhutira kuti zinthu zimene mufunika kunena ndi zaphindu. Mukamaona kuti nkhani yanu ndi yofunika kwambiri, nawonso okumverani adzaiona chimodzimodzi.”
Rochelle: “Ndinaona kuti zimathandiza kudzijambula ndekha pavidiyo. N’zochititsa manyazi koma zimathandiza. Chinanso, yesani kupeza mutu wa nkhani umene umakusangalatsani. Omvera anu adzaonanso kuti nkhani imeneyo imakusangalatsani.”
Margrett: “Ndimaona kuti ndimayankhula mwachibadwa kwambiri ndiponso monga ngati ndikuyankhulana ndi winawake ngati ndangolemba mfundo zikuluzikulu za nkhani yanga m’malo molemba nkhani yonseyo mwatsatanetsatane kuti ndizikachita kuŵerenga. Chinanso n’chakuti, ndikapuma kaye mokoka mpweya wambiri ndisanayambe kuyankhula zimandithandiza kuti ndikhazikitse mtima pansi.”
Corrine: “Osalephera kudziseka ngati mwalakwitsa penapake. Aliyense amalakwitsa. Chachikulu n’kuyesetsa basi.”
Inde, monga mmene zimakhalira poyesetsa kuchita zinazake, kaya pa maseŵera olimbitsa thupi, luso la zolembalemba, kapena zoimbaimba, zonsezo zimadalira kuzoloŵera ndiponso kuyeseza kaye maulendo ambirimbiri. Tatiana amalimbikitsa zokonzeratu nkhani yanu nthaŵi idakalipo yambiri kuti mukhale ndi nthaŵi yokwanira yoyesezera. Ndipo osataya mtima. “Ndimati ndikamakamba nkhani pagulu kaŵirikaŵiri, m’pamenenso mantha amayamba kundithera,” iye anatero. Koma palinso wina amene angakuthandizeni amene simuyenera kumuiwala, makamaka mukauzidwa kuti mudzakambe nkhani yokhudza za kulambira koona.
Kuthandizidwa ndi Wodziŵa Kuyankhula Kuposa Anthu Onse
Davide, yemwe anadzakhala mfumu ya Aisrayeli, adakali mnyamata ankadziŵika kuti anali “wochenjera manenedwe ake,” kapena kuti woyankhula mwaluso kwabasi. (1 Samueli 16:18) Kodi n’chifukwa chiyani anali wotero? Zimaoneka kuti paunyamata wake, nthaŵi imene ankakhala maola ambiri akuŵeta nkhosa kubusa, Davideyo anayamba kukondana kwambiri ndi wina wodziŵa kuyankhula kuposa anthu onse, yemwe ndi Yehova Mulungu, kudzera m’pemphero. (Salmo 65:2) Patapita nthaŵi, ubwenzi umenewu unamuthandiza kuti aziyankhula zomveka, zamphamvu, ndiponso zolimbikitsa ngakhale panthaŵi zovuta.— 1 Samueli 17:34-37, 45-47.
Mukhoza kukhala wotsimikiza kuti panthaŵi imene mukulambira, Mulungu angakuthandizeninso kuyankhula zinthu zolimbikitsa, ngati mmene anathandizira Davide, pokupatsani “lilime la ophunzira.” (Yesaya 50:4; Mateyu 10:18-20) Inde, panopo mukayamba kugwiritsira ntchito zonse zokuthandizani kuwonjezera luso lanu lodziŵa kuyankhula bwino, mukhoza kukhala munthu wodziŵa kukamba nkhani pagulu!
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 3 Mayina ena tawasintha.
[Bokosi patsamba 18]
Kuphunzitsidwa Kuyankhula Pagulu
M’mipingo ya Mboni za Yehova padziko lonse, sabata iliyonse mumakhala sukulu yophunzitsa zinthu zochokera m’Baibulo imene amaitcha kuti Sukulu ya Utumiki wa Mulungu. Ophunzira amakambirana, amakamba nkhani pamaso pa mpingo, ndipo aliyense amathandizidwa kuti afike podziŵa kuyankhula bwino. Kodi sukulu imeneyi imathandizadi? Tiyeni timulole Chris, yemwe ali ndi zaka 19 atiuze zimene anaonapo.
“Ndisanalembetse sukulu imeneyi, sindinkakhala womasuka pa anthu,” iye anatero. Ndiye anawonjezera kuti: “Zoti ndingadzafike pomaima kutsogolo kwa anthu sindinkalotako ngakhale pang’ono. Koma anthu ena mu mpingo anandilimbikitsa atanena kuti ngakhale nkhani yonse itati ithe ndikuchita chibwibwi, iwo angaimvebe bwino, podziŵa mmene ndavutikira kuti ndifike pokaima kutsogolo. Kenaka, iwo ankandiyamikira pa nkhani iliyonse imene ndakamba. Zimenezo zinandithandiza kwabasi.”
Tikunena pano, patatha zaka zisanu chilembetsereni sukulu imeneyi, Chris akukonzekera kuti akambe nkhani yake yoyamba ya mphindi 45. Kodi mukuchita zotheka kuti sukulu imeneyi mupindule nayo?
[Zithunzi pamasamba 16, 17]
Kukhala munthu wodziŵa kuyankhula pagulu kungakuthandizeni m’njira zambiri pa moyo wanu