Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Zokambirana za Mayiko Zidzabweretsa Mtendere Padziko Lonse?

Kodi Zokambirana za Mayiko Zidzabweretsa Mtendere Padziko Lonse?

Lingaliro la Baibulo

Kodi Zokambirana za Mayiko Zidzabweretsa Mtendere Padziko Lonse?

KODI mumafuna kuona nkhondo zonse zitatha? Ndithudi kuti nkhondo zapachiweniweni ndiponso za pakati pa mayiko zithetsedwe, m’pofunika patakhala zokambirana za mtendere. Anthu ambiri amaona kuti atsogoleri a mayiko atati agwirizane chimodzi, nkhondo ingatheretu. Komabe, mwina n’kutheka kuti mumakhumudwa poona kuti zokambirana za mayiko siziphula kanthu. Kwa zaka zambirimbiri nthumwi za mayiko zakhala zikuchita mapangano, kuyesa kupeza mfundo zoti mayiko azitsatira, ndiponso zachititsa misonkhano, koma ndi mavuto ochepa chabe amene athetsedwa.

Baibulo lili ndi nkhani zambiri zokhudza zokambirana zamtendere. Limayankha mafunso otsatiraŵa: Kodi ndi zinthu zotani zimene panopa zikulepheretsa kuti zokambirana za mayiko zibweretse mtendere? Kodi Akristu ayenera kumakhala nawo pazokambirana za mayiko? Kodi pamapeto pake mtendere weniweni udzapezeka bwanji?

Kodi Chikulepheretsa Mtendere N’chiyani?

Nkhani zambiri m’Baibulo zimasonyeza mmene kukambirana pamaso m’pamaso kungabweretsere mtendere. Mwachitsanzo, Abigayeli anayankhula mwanzeru mpaka n’kukhutiritsa Davide ndi ankhondo ake kuti asabwezere zoipa banja lake. (1 Samueli 25:18-35) Yesu anafotokoza fanizo la mfumu imene inagwira njakata kenaka n’kutumiza akazembe ake kuti akapemphe mtendere. (Luka 14:31, 32) Inde, Baibulo limasonyeza kuti zokambirana zina zingathetse mikangano. Nangano n’chifukwa chiyani kaŵirikaŵiri zokambirana zoti akhazikitse mtendere pakati pa mayiko amene akuchita nkhondo zimangothandiza kwa nthaŵi yochepa chabe?

Baibulo linalosera kale molondola kuti nthaŵi yathu ino idzakhala yovuta kwambiri. Chifukwa cha mphamvu yoipa ya Satana Mdyerekezi, anthu adzakhala “osayanjanitsika” koma adzakhala “aukali, osakonda abwino, aliuma olimbirira, otukumuka mtima.” (2 Timoteo 3:3, 4; Chivumbulutso 12:12) Kuwonjezera pamenepo, Yesu analosera kuti anthu adzadziŵa kuti mapeto ali pafupi chifukwa cha “nkhondo ndi mbiri zake za nkhondo.” (Marko 13:7, 8) Ndani angatsutse kuti zimenezi zikufala kwambiri? Ndiye poti n’zoona zimenezo, kodi n’zodabwitsa, kuti zimene mayiko amayesetsa kuchita kuti pakhale mtendere pakati pawo kaŵirikaŵiri siziphula kanthu?

Komanso, ganizirani mfundo yoona iyi: Nthumwi za mayiko zimayesetsa kuti kukangana kusakhalepo, koma aliyense cholinga chake chachikulu pochita zimenezo chimakhala chokokera kuti zinthu ziwayendere m’dziko mwawo. Chimenecho ndicho cholinga chenicheni cha zokambirana za anthu andale. Kodi Akristu ayenera kuloŵerera mu zokambirana zoterozo?

Mmene Akristu Amaonera Zokambirana za Mayiko

Baibulo limalangiza kuti: “Musamakhulupirira zinduna, kapena mwana wa munthu, amene mulibe chipulumutso mwa iye.” (Salmo 146:3) Zimenezi zikutanthauza kuti kaya akhale ndi zolinga zotani, oimira mayiko sangathe kapena kuti alibe mphamvu yomanga mfundo yothetseratu mavuto onse.

Yesu akuimbidwa mlandu pamaso pa Pontiyo Pilato, ananena kuti: “Ufumu wanga suli wa dziko lino lapansi; ufumu wanga ukadakhala wa dziko lino lapansi, anyamata anga akadalimbika nkhondo, kuti ndisaperekedwe kwa Ayuda; koma tsopano ufumu wanga suli wochokera konkuno.” (Yohane 18:36) Nthaŵi zambiri njira zokhazikitsira mtendere zimasokonezeka chifukwa cha kudana kwa mayiko ndiponso chifukwa chadyera pa ndale. Choncho, Akristu oona amapeŵa kuloŵerera m’mikangano ya mayiko yotereyi ndi mfundo zimene amamanga pa zokambirana zawozo.

Kodi zimenezi zikutanthauza kuti Akristu sachita chidwi ndi zochitika padziko pano ndiponso kuti siziwakhudza? Kodi samva chisoni ndi kuvutika kwa anthu? Si choncho ayi. Mosiyana ndi zimenezo, Baibulo limafotokoza kuti opembedza Mulungu oona, aliyense payekha, “akuusa moyo ndi kulira” chifukwa cha zinthu zoipa zimene amaona zikuchitika. (Ezekieli 9:4) Kungoti Akristu amadalira Mulungu kuti ndiye adzabweretse mtendere mongadi mmene analonjezera. Kodi kwa inuyo mtendere umatanthauza kuti kulibenso nkhondo? Ufumu wa Mulungu udzachititsa kuti zimenezo zithekedi. (Salmo 46:8, 9) Koma chinanso n’chakuti, ufumuwo udzaonetsetsa kuti aliyense wokhala padziko lapansi akhale mopanda mantha ndiponso akhale ndi zonse zofunikira pa moyo. (Mika 4:3, 4; Chivumbulutso 21:3, 4) Mtendere wosaneneka ngati umenewo sungapezeke chifukwa cha zokambirana za mayiko kapena kuyesetsa kwa mabungwe a anthu “okhazikitsa mtendere.”

Ulosi wa m’Baibulo ndiponso zimene zakhala zikuchitika kumbuyoku zikuonetseratu poyera kuti kukhulupirira zokambirana za anthu kuti zibweretse mtendere kungangochititsa anthu kudzanong’oneza bondo. Anthu amene amakhulupirira kwambiri kuti amene angabweretse mtendere ndi Yesu Kristu n’kumagwirizana ndi Ufumu wa Mulungu adzaona zimene amalakalaka zokhala pamtendere weniweni zikuchitikadi. Komanso, adzakhala pamtenderewo kwamuyaya!—Salmo 37:11, 29.

[Mawu Otsindika patsamba 15]

Kaya akhale ndi zolinga zotani, oimira mayiko sangathe ndiponso alibe mphamvu yomanga mfundo yothetseratu mavuto onse

[Mawu a Chithunzi patsamba 14]

Pansipa: Photo by Stephen Chernin/Getty Images