Kubadwira M’dziko Lopanda Chikondi!
Kubadwira M’dziko Lopanda Chikondi!
MWANA akabadwa amaona kuti wafika m’dziko lankhanza, losoŵa chikondi, lokhala ndi mavuto ambirimbiri. Ngakhale kuti mwana wakhanda sangatulutse mawu ofotokoza zimene akuganiza, akatswiri ena asayansi amati mwana amazindikira zimene zikuchitika ngakhale asanabadwe.
Buku lofotokoza za mwana yemwe sanabadwe lotchedwa The Secret Life of the Unborn Child limati: “Tsopano tikudziŵa kuti mwana yemwe ali m’mimba akangokwanitsa miyezi isanu ndi umodzi kapena kuposa (mwinanso asanakwanitse miyezi imeneyo) amakhala munthu wotha kuzindikira, amene amadzidzimuka zinazake zikachitika ndipo amakhala akuganiza ndithu.” Akatswiri ena asayansi amaona kuti mmene mwanayo amavutikira pobadwa zimatha kudzakhudza moyo wake m’tsogolo, ngakhale kuti mwana wakhanda sangakumbukire zimenezo.
Mwana akabadwa, amapitirizabe kuvutika. Akatuluka m’mimba mwa amayi ake, sapezanso chakudya kudzera m’chakudya chimene amayi ake adya. Nchombo umene anali kupumira ndi kudyera adakali m’mimba umakhala utaduka. Kuti akhale ndi moyo, ayenera kuyamba kupuma ndi kudya payekha. Amafunikira munthu woti azimudyetsa ndi kumusamalira pa zinthu zina ndi zina zofunikira.
Mwanayo ayeneranso kukula m’maganizo, mu mtima, ndiponso m’moyo wauzimu. Choncho payenera kukhala munthu woti n’kumalera mwana wakhandayo. Kodi ndani makamaka amene ali woyenera kugwira ntchito imeneyi? Kodi mwana wakhanda amafuna kuti makolo ake azim’chitira chiyani? Kodi zinthu zofunikira zimenezi zingachitidwe motani makamaka? Nkhani zotsatirazi zitithandiza kuyankha mafunsoŵa.