Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kukhala ndi Matenda a Maganizo

Kukhala ndi Matenda a Maganizo

Kukhala ndi Matenda a Maganizo

MATENDA a maganizo a mitundu yosiyanasiyana n’ngofala modetsa nkhaŵa kwambiri. Mwachitsanzo akuti anthu pafupifupi mamiliyoni 330 padziko lonse amadwalika kwambiri ndi matenda a maganizo ochititsa munthu kungokhala woipidwa. Matenda amene tikunenaŵa ndi matenda amene wodwala amangokhala wokwiya kwambiri ndiponso wosasangalala ndi zochitika za tsiku n’tsiku. Akuti podzatha zaka 20 m’tsogolomu, matenda a maganizo ochititsa munthu kungokhala woipidwa azidzaposedwa ndi matenda okhudza mtima basi. Moti n’zosadabwitsa kuti anthu ena amati “pa matenda osiyanasiyana a maganizo, matenda ochititsa munthu kungokhala woipidwa ali ngati chimfine.”

Posachedwapa matenda ena a maganizo ochititsa munthu kusinthasintha zochitika anayamba kudziŵika kwambiri. Munthu amene ali ndi matendaŵa amasintha kwambiri zochitika, kumati pena akhale woipidwa kwambiri kenaka n’kukhala wosangalala mochita kunyanyira. Buku lina la posachedwapa, lofalitsidwa ndi bungwe la American Medical Association, linati, “panthaŵi yomwe umakhala woipidwayo, ungathe kumavutika ndi maganizo oti ungodzipha. Panthaŵi yomwe umakhala wosangalala mochita kunyanyira, nzeru zako zimatha kubalalika ndipo sungaone kuti zimene ukuchitazo n’zoopsa motani.”

Akuti n’kutheka kuti anthu aŵiri pa anthu handiredi alionse ku United States amadwala matenda a maganizo ochititsa munthu kusinthasintha zochitikaŵa, kutanthauza kuti m’dziko limeneli lokha muli odwala matendaŵa mamiliyoni ambimbiri. Komabe, manambala paokha sangathe kusonyeza nsautso yokhala ndi matenda a maganizo.

Matenda a Maganizo Amene Wodwala Amangokhala Woipidwa

Ambirife timadziŵa mmene zimakhalira munthu ukakhala kuti china chilichonse chikungokuipira. Pakapita nthaŵi, mwina maola kapena masiku ochepa chabe, umasintha n’kuyamba kusanguluka. Komano zimakhala zosautsa kwabasi akhala matenda ochititsa munthu kungokhala woipidwa. Zimakhala bwanji makamaka? Dr. Mitch Golant, ananena kuti: ‘Anthu amene tilibe matendaŵa tikakhala osasangalala timadziŵa ndithu kuti ifika nthaŵi imene tisanguluke, komano kwa munthu amene ali ndi matendaŵa, zimenezi zimam’chitikira kaŵirikaŵiri ndipo sadziŵa bwinobwino kuti zisiya bwanji, kapena kuti zisiya liti, mwinanso sadziŵa ngati zisiye n’komwe.’

Anthu amadwala mosiyanasiyana matenda ochititsa munthu kungokhala woipidwa. Mwachitsanzo, anthu ena amadwala moyendera nyengo. Iwo amadwala kwambiri panyengo inayake yokha pachaka, kaŵirikaŵiri nyengo yachisanu. Buku lofalitsidwa ndi bungwe la People’s Medical Society linati: “Anthu odwala matenda a maganizo amene amayendera nyengo amanena kuti matendaŵa amawapezeketsa kwambiri akamakhala m’madera a kumpoto kwambiri kwa dziko lapansili ndiponso kunja kukhala kwa mitambo. Ngakhale kuti amati matendaŵa amapezeketsa anthu kumadera amene dzuŵa silioneka m’nyengo yachisanu, pali anthu ena amene akhala akuwapezeketsa chifukwa chogwira ntchito m’malo osawala bwino, kapena chifukwa choti kunja kwachita mitambo pa nyengo yosayenerera mitambo ndiponso chifukwa chosaona bwino.”

Kodi n’chiyani chimayambitsa matenda a maganizo ochititsa munthu kungokhala woipidwa? Sichidziŵika bwinobwino ayi. Inde, nthaŵi zina zimaoneka ngati n’zakumtundu, komano zimaoneka kuti nthaŵi zambiri matendaŵa amagwira munthu makamaka chifukwa cha zimene zamuchitikira pamoyo wake. Akutinso akazi amene amawapeza ndi matendaŵa ndi ochuluka moŵirikiza kaŵiri poyerekezera ndi amuna. * Koma zimenezi sizikutanthauza kuti amuna sagwidwa kwenikweni ndi matendaŵa, chifukwatu, akuti pa amuna 5 mpaka 12 pa 100 alionse adzadwalapo matendaŵa m’moyo wawo.

Matenda otereŵa akagwira munthu amakhudza pafupifupi chinthu chilichonse pa moyo wake. Wodwala wina wotchedwa Sheila anati: “Amakuloŵerera kwabasi, kukuchititsa kuti uzidzikayikira, uzidzidelera, usamaganize ndi kuchita zinthu zakupsa, ndipo akakufooketseratu, amachita kukupondaponda kuti aone ngati ungalimbelimbe.”

Nthaŵi zina wodwala angathe kulimbikitsidwa kwambiri pokambirana za mumtima mwake ndi munthu yemwe angamvetse vuto lakelo. (Yobu 10:1) Komabe tiyenera kudziŵa kuti ngati munthu akudwala matendaŵa chifukwa chakuti zinthu zasokonekera m’thupi mwake, n’zosatheka kuchira chifukwa chongosiya kuganiza kwambiri. Chifukwatu ngati zinthu zasokonekera m’thupi, maganizo akewo sakhala oti iye angawathetse mwakufuna kwake. Ndiponso n’kutheka kuti nayenso wodwalayo sakudziŵa kwenikweni chimene chikum’chitikira monganso abale ake ndiponso anzake.

Chitsanzo ndi Paula, * mayi wachikristu amene anali kuvutika kwambiri pomangokhala woipidwa asanadziŵe kuti ali ndi matenda a maganizo. Iye anati: “Nthaŵi zina tikamaliza misonkhano yachikristu ndinkangothamangira m’galimoto yanga n’kuyamba kulira, popanda chifukwa chilichonse. Ndinkangomva kukhala wosungulumwa kwabasi ndipo ndinali kungomva kupweteka mumtima. Ngakhale kuti ndinkachita kuona ndekha kuti pali anzanga ambirimbiri ondiganizira, zonsezo sizinkandikhudza mtima n’komwe.”

Zangati zomwezi zinam’chitikiranso Ellen, yemwe anagonekedwa m’chipatala chifukwa cha matenda a maganizo ochititsa munthu kungokhala woipidwa. Iye anati: “Ineyo ndili ndi ana aamuna aŵiri, azipongozi aŵiri abwino kwambiri, komanso ndili ndi mwamuna ndipotu anthu onseŵa si mmene amandikondera.” Apatu bwenzi Ellen akuoneratu yekha kuti moyo n’ngokoma ndiponso kuti anthu a m’banja lake amam’ganizira kwambiri. Koma matenda a maganizo akam’tengetsetsa munthu, munthuyo amangoganizira zinthu zosathandiza.

Ndi bwinonso kukumbukira kuti banja lonse lingakhudzidwe kwambiri ngati mmodzi m’banjamo ali ndi matenda a maganizo. Dr. Golant anati: “Munthu amene mumam’konda akadwala matenda a maganizo, mumangokhala nkhaŵa ili bii, osadziŵa kwenikweni kuti achira liti kapena kuti zimuyambiranso liti. Moyo ungakuipireni kwambiri, mwinanso mungakhale achisoni ngakhale okwiya kumene chifukwa choti moyo wanu wasintha, moti mwina sudzabwereranso mwakale.”

Nthaŵi zambiri ana amatha kudziŵa ngati kholo lawo likudwala matenda a maganizo ochititsa munthu kungokhala woipidwa. Dr. Golant anati: “Mwana amene mayi wake ali ndi matendaŵa, amatsata bwinobwino mmene maganizo a mayi akewo akuyendera ndipo amatha kuona kalikonse kamene iwo asintha.” Dr. Carol Watkins anati ana a mayi kapena bambo wokhala ndi matendaŵa “kaŵirikaŵiri amakhala opulukira, ouma mutu, ndiponso olephera kukhala bwino ndi anzawo. Komanso m’posavuta kuti nawonso agwidwe matendaŵa.”

Matenda a Maganizo Amene Wodwala Amangosinthasintha Zochitika

N’zoona kuti matenda a maganizo ochititsa munthu kungokhala woipidwa n’ngovutadi. Komano akaphatikizana ndi kusangalala konyanyira amasanduka matenda a maganizo omwe wodwala amangokhalira kusinthasintha zochitika. * Lucia, yemwe amadwala matendaŵa anati: “Chimene sichisintha pa matendaŵa n’chakuti amangokhalira kusintha.” Chikalata cha The Harvard Mental Health Letter chinati panthaŵi imene wodwalayo akusangalala monyanyira, “amatha kumangoloŵerera pa zinthu zosam’khudza, kumangofuna kulamulira ena, ndipo mwadzidzidzi amatha kungosintha khalidwe lochita zinthu mothamanga magazili n’kuyamba kuipidwa mwinanso kulusa.”

Lenore ananenapo zimene zinkam’chitikira pa nthaŵi imene matendaŵa amam’chititsa kusangalala monyanyira. Iye anati: “M’thupimu ndinkachita kumva mphamvu zikudzadzanamo. Anthu ambiri ankangoti ndine mayi wogwira ntchito modabwitsa. Anthu ankangoti, ‘Ine ndimakhumbira n’takhala ngati anzathunu.’ Ndinkakhala ndi mphamvu zadzaoneni, ndipo ndinkaona kuti ndingathe kuchita ntchito ina iliyonse. Ndinkachita maseŵera olimbitsa thupi mosatopa n’komwe. Koma ngakhale ndinkachita zinthu zonsezi, ndinkangogona maola aŵiri kapena atatu basi, usiku onse. Komabe ndinkadzuka ndi nyonga kwabasi.”

Koma patapita nthaŵi, zinthu zinayamba kusamuyendera bwino Lenore. Iye anati: “Ndinkati ndikafika pachimake posangalala monyanyira ndinkamva penapake cham’katikatimu kuti chinachake chikundinyong’onya ndipo zinali zosatheka kuchiletsa. Zikangotero ndinkasinthiratu n’kusanduka muntu wolusa ndiponso wowononga zinthu. Ndinkalalatira aliyense wakwathu popanda chifukwa chenicheni. Ndinkakhala wolusa, wolunda, ndiponso wosamva zonena za ena. Ndikachita zoopsazi ndinkapezeka kuti ndatoperatu, misonzi yalengeza m’maso, ndiponso ndaipidwa mapeto. Ndinkadziona kuti ndine munthu wopanda ntchito ndiponso woipa. Komano pena ndinkatha kungosintha n’kuyambanso zanga zokhala wosangalala zija, ngati kuti palibe chilichonse chinalakwika.”

Khalidwe losinthasinthali limene anthu odwala matendaŵa amachita limasokoneza kwambiri achibale awo. Mary, mwamuna wake amadwala matendaŵa ndipo anati: “Ndimasokonezeka ndikaona kuti mwamuna wanga akusangalala, akulankhulalankhula ndipo kenaka mwadzidzidzi n’kungokhala ndwii osafuna kulankhula ndi aliyense. Zimandivuta kwambiri kuzoloŵera kuti iyeyu sachitira dala zimenezi.”

Komatu nthaŵi zambiri, ngakhale wodwalayo amasautsika mtima kwambiri ndi matendaŵa. Munthu wina wodwala matendaŵa, dzina lake Gloria anati: “Ndimakhumbira anthu amene moyo wawo uli wokhazikika ndiponso wosasinthasintha. Kwa ife odwala matenda ochititsa munthu kusinthasintha zochitika, moyo wokhala bwinobwino osasinthasintha timangoulaŵa basi. Palibe aliyense wa ife amene nthaŵi zonse amakhala ndi moyo woterowo.”

Kodi n’chiyani chimayambitsa matenda a maganizo ochititsa munthu kusinthasintha zochitika? Nthaŵi zina zimakhala zakumtundu ndipotu matenda a maganizo ameneŵa savuta kugwira munthu kuchokera kwa achibale powayerekezera ndi aja ochititsa munthu kungokhala woipidwa. Bungwe la American Medical Association linati: “Malingana ndi zimene asayansi ena anafufuza, anthu a m’banja la odwala matenda a maganizo ochititsa munthu kusinthasintha zochitika, monga makolo awo, azing’ono awo ndi azikulu awo, kapenanso ana awo angathe kudwala mosavuta kwambiri matendaŵa kusiyana ndi anthu amene m’banja mwawo mulibe munthu wodwala matendaŵa. Kuphatikizanso apo, m’banja mwanu mukakhala wina amene akudwala matendaŵa, m’posavuta kuti inuyo mudwale matenda a maganizo aakulu.”

Mosiyana ndi matenda a maganizo ochititsa munthu kumangokhala woipidwa, zimaoneka kuti matenda a maganizo ochititsa munthu kusinthasintha zochitika amagwira amuna ndi akazi mofanana. Nthaŵi zambiri amagwira anthu pamene ali m’zaka za m’ma 20 kapena kuposerapo, koma anthu ena apezekapo ndi matendaŵa ali ndi zaka za pakati pa 13 ndi 19, ena ngakhale ali aang’ono kuposa pamenepa. Mulimonsemo, chinthu chovuta kwambiri, ngakhale kwa dokotala wodziŵa bwino matendaŵa ndicho kuonetsetsa bwino zizindikiro zake kenaka n’kutsimikiziradi kuti wodwalayo ali ndi matenda amenewo kapena ayi. Dr. Francis Mark Mondimore wa pa yunivesite ya zachipatala ya Johns Hopkins University School of Medicine anati: “Pa matenda ena onse a maganizo, matenda ochititsa munthu kusinthasintha zochitika ali ngati birimankhwe chifukwa wodwala aliyense amakhala ndi zizindikiro zakezake, zomwenso zimasintha wodwalayo akasintha zochitika, ndipo ngakhale wodwala mmodzi yemweyo amangokhalira kusinthasintha zizindikiro. Matendaŵa sizidziŵika kuti atulukira chifukwa amangomupezeketsa munthu mwadzidzidzi n’kumuchititsa kuipidwa kwambiri koma kenaka n’kukhalanso bwinobwino kwa zaka zambiri ndithu. Komano amadzamupezeketsanso mwa njira ina yodabwitsa kwabasi pomuchititsa kukhala wosangalala mochita kunyanyira.”

N’zoonekeratu kuti matenda a maganizo a mitundu yosiyanasiyana n’ngovuta kuwazindikira ndipo n’ngosautsa kwambiri ukakhala nawo. Koma pali nkhani yabwino kwa odwala matendaŵa.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 8 Chifukwa chimodzi n’chakuti akazi amatha kukhala ndi vuto losokonezeka maganizo akabereka ndiponso thupi lawo limasintha akaleka kusamba. Chinanso n’chakuti, akazi sachita mphwayi kupita kuchipatala, motero matenda awo amadziŵika.

^ ndime 11 Mayina ena amene ali m’nkhani zino tawasintha.

^ ndime 16 Madokotala amanena kuti nthaŵi zambiri, wodwala angathe kukhala woipidwa kwa miyezi ingapo ndithu kenaka n’kukhala wosangalala kwambiri kwa miyezi ina ingaponso. Komabe amati odwala ena amasintha nthaŵi zingapo ndithu pachaka. Mwa apo ndi apo, odwalawo amatha kusintha ngakhale pa maola 24 okha.

[Mawu Otsindika patsamba 6]

“Kwa ife odwala matenda ochititsa munthu kusinthasintha zochitika, moyo wokhala bwinobwino osasinthasintha timangoulaŵa basi. Palibe aliyense wa ife amene nthaŵi zonse amakhala ndi moyo woterowo,” anatero GLORIA

[Bokosi/Chithunzi patsamba 5]

Zizindikiro za Matenda Aakulu a Maganizo *

Munthu amangokhala woipidwa nthaŵi yochuluka patsiku kapenanso pafupifupi tsiku lonse, kwa milungu yosachepera iŵiri

Sachitanso chidwi ndi zinthu zimene kale zinali zomusangalatsa

Amawonda kapena kunenepa kwambiri

Amagona kwambiri kapena amasoŵeratu tulo

Amachita zinthu mofulumira kapena mwapang’onopang’ono kwambiri

Amatopa kwambiri, popanda chifukwa chodziŵika bwino

Amadzimva ngati munthu wopanda ntchito kapenanso kudzimva ngati wolakwa koma popanda chifukwa chilichonse

Amavutika kuganizira zinthu bwinobwino

Amaganizaganiza zongodzipha

Zina mwa zizindikirozi zingakhalenso zizindikiro za matenda a maganizo enanso amene sam’pezeketsa kwambiri wodwala koma amakhala kwa nthaŵi yaitali

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 31 Zizindikiro zimene tazilembazi cholinga chake n’kuthandiza anthu kuti akhale ndi chithunzithunzi cha matendaŵa koma osati kuti azitha kudziŵa okha kuti ali ndi matendaŵa. Chinanso n’chakuti zina mwa zizindikirozi pazokha zingasonyeze matenda ena osati matenda a maganizo amene tikukamba panoŵa okha.