Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kukhalabe Osangalala Ngakhale M’mavuto

Kukhalabe Osangalala Ngakhale M’mavuto

Kukhalabe Osangalala Ngakhale M’mavuto

Mogwirizana ndi zimene Baibulo linaneneratu, tili mu “nthaŵi zowawitsa.” (2 Timoteo 3:1) Mavuto a m’banja, matenda, ndiponso mavuto a za chuma, zangokhala zina chabe zimene mwina zikukusautsani. Nthaŵi zina, mungamaone ngati simungathenso kupirira nazo. Komabe, mungakhalebe wosangalala ngakhale m’mavutowo. Taonani chitsanzo ichi.

Duŵa linalake lotchedwa Teide violet limamera m’dera lokwera mamita 3,700 pa chisumbu chotchedwa Tenerife chomwe chili mbali ya kugombe la ku North Africa. Phiri la Pico de Teide ndi lalitali kwambiri pa chisumbucho, ndipo pamaphulika chiphalaphala chotentha. Dzina la duwali linachokera pa dzina la phirili. Pamalo otsetsereka amene ali cha kumtunda kwa maloŵa pamaoneka kuti sipamera zomera. Koma nyengo yotentha ikayamba, madzi oundana chifukwa chozizira omwe amayamba kusungunuka amakhala okwanira kuti maluŵa ameneŵa aphukirenso bwinobwino n’kukongoletsa dera lonseli ndi mtundu wake wofiirira. Ndithudi, duŵali limaoneka lonyozoloka ndiponso losalimba, koma limatha kupulumuka bwinobwino n’kumasangalala m’dera limeneli limene zomera zina sizimeramo.

Mofanana ndi duŵa limeneli, inunso mungathe kupirira mukakumana ndi zinthu zosautsa kwambiri. Baibulo lathandiza anthu ambiri a Mboni za Yehova kuchita zimenezo ngakhale m’nthaŵi zovuta kwambiri. Mwachitsanzo, anthu amene anatsekeredwa m’ndende mu ulamuliro wa chipani cha Nazi ku Germany anakhoza kukhalabe osangalala. Mtolankhani wina wa ku Sweden dzina lake Björn Hallström anati: “Anthu ameneŵa ankachitiridwa nkhanza kuposa wina aliyense, koma chifukwa chokhulupirira Mulungu, anakwanitsa kukhalabe bwinobwino kusiyana ndi ena onse.”

Kaya muli m’mavuto otani, Baibulo likhoza kukuthandizani kuti muzikhalabe osangalala ngakhale m’mavutowo. Kumanani ndi Mboni za Yehova kwanuko, kapena lemberani kalata ku adiresi yoyenera imene ili patsamba 5 la magazini ino kuti munthu wina aziphunzira nanu Baibulo panyumba panu kwaulere.