Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mmene Ena Angathandizire

Mmene Ena Angathandizire

Mmene Ena Angathandizire

N’KUTHEKA kuti mukudziŵapo munthu winawake amene akudwala matenda a maganizo ochititsa munthu kungokhala woipidwa kapena ochititsa munthu kusinthasintha zochitika. Ngati n’choncho kodi mungamuthandize bwanji? D. J. Jaffe wa m’bungwe lotchedwa National Alliance for the Mentally Ill anapereka malangizo abwino aŵa: “Musaone ngati munthuyo ndiye matendawo; danani ndi matendawo koma munthuyo muzim’konda.”

Mzimayi wina wotchedwa Susanna anachitadi zimenezi moleza mtima ndiponso mwachikondi. Iye anali ndi mnzake wodwala matenda a maganizo ochititsa munthu kusinthasintha zochitika. Susanna anati: “Nthaŵi zina iye sankafuna n’komwe kucheza nane.” M’malo mongomunyanyala mnzakeyo, Susanna anafufuza za matendaŵa kuti awadziŵe bwino. Iye anati: “Panopa, ndimatha kumvetsa mmene matendaŵa ankasokonezera zochitika za mnzangayu.” Susanna amaona kuti kuyesetsa kumumvetsa wodwalayo kungakuthandizeni m’njira yapadera kwambiri. Iye anati: “Kungakuthandizeni kuti wodwalayo muzim’konda ndiponso kumuona kuti n’ngofunika kwambiri ngakhale kuti akudwala.”

Ngati wodwalayo ali wachibale, m’pofunika kwambiri kumuthandiza ndi mtima wonse. Mario, yemwe tam’tchulapo kale m’nkhani ina m’mbuyomu anadziŵa mwamsanga zimenezi. Mkazi wake Lucia, amenenso tam’tchulapo kale m’mbuyomu, amadwala matenda a maganizo ochititsa munthu kusinthasintha zochitika. Mario anati: “Poyamba, chinandithandiza n’chakuti ndinkam’perekeza mkazi wanga kuchipatala ndiponso ndinkaŵerenga mabuku ondithandiza kuti ndimvetsetse matenda odabwitsaŵa pofuna kudziŵa mmene tingalimbanirane nawo. Chinanso, ine ndi Lucia tinkakambirana zinthu zambiri ndipo tinkayesetsa kulimbana ndi vuto lililonse limene latigwera.”

Thandizo Lochokera Kumpingo Wachikristu

Baibulo limalimbikitsa Akristu onse kuti ‘alimbikitse amantha mtima,’ kapena kuti ovutika maganizo, ndi kuti ‘akhale oleza mtima pa onse.’ (1 Atesalonika 5:14) Kodi mungachite bwanji zimenezi? Choyamba, m’pofunika kumvetsa kusiyana kwa matenda amaganizo ndi matenda auzimu. Mwachitsanzo, wolemba Baibulo Yakobo ananena kuti pemphero lingathe kupulumutsa munthu wodwala matenda auzimu. (Yakobo 5:14, 15) Koma Yesu anavomereza kuti anthu amene ali ndi matenda m’thupi mwawo amafunikira dokotala. (Mateyu 9:12) Inde, nthaŵi zonse n’koyenerera ndipo n’kothandiza kupemphera kwa Yehova tikakhala ndi nkhaŵa ina iliyonse, ngakhale yokhudza thanzi lathu. (Salmo 55:22; Afilipi 4:6, 7) Koma Baibulo silinena kuti kuyamba kukonda kwambiri zinthu zauzimu pakokha kungatithetsere matenda amene timadwala masiku anoŵa.

Motero, Akristu ozindikira amapeŵa kunena mawu osonyeza kuti anthu odwala matendaŵa amakhala ndi vutoli chifukwa cha zochita zawo. Mawu otero si othandiza ndipo ali ngati mawu a anzake a Yobu amene ankangonamizira kuti akumulimbikitsa. (Yobu 8:1-6) Chifukwatu nthaŵi zambiri, anthu odwala matenda a maganizo sapeza bwino pokhapokha alandire mankhwala. Zimatero makamaka munthuyo akakhala kuti matendaŵa am’tengetsetsa kwambiri, mwinanso n’kufika pomaganiza zodzipha. Zikatero, m’pofunika kukaonana ndi dokotala.

Komabe Akristu anzawo angathandize m’njira zambiri. N’zoona kuti m’pofunika kuleza mtima. Mwachitsanzo, zochita zina pa utumiki wachikristu zingakhale zovutirapo kwambiri kwa anthu amene ali ndi matenda a maganizo. Diane, yemwe amadwala matenda a maganizo ochititsa munthu kusinthasintha zochitika anati: “Ndimavutika kuchita nawo utumiki. Zimandivuta kuuza ena uthenga wabwino ndiponso wosangalatsa wa m’Baibulo pamene ine mwini sindikumva bwino mumtima mwanga ndiponso sindikusangalala.”

Kuti mukhale munthu wothandiza kwa anthu odwala matendaŵa, yesetsani kuchita zinthu mowaganizira. (1 Akorinto 10:24; Afilipi 2:4) Yesetsani kuganizira mmene wodwalayo akumvera osati mmene inuyo mukuonera ayi. Musamuvutitse ndi zinthu zimene sangazikwanitse. Carl, amene akudwala matenda a maganizo ochititsa munthu kungokhala woipidwa anati: “Anthu akayamba kundimvetsa mmene ndilili, mumtimamu ndimamva kuti ndayambiranso kukondedwa. Pothandizidwa moleza mtima ndi anzanga angapo achikulire, ndinayamba kukonda kwambiri Mulungu ndipo ndimasangalala kwambiri chifukwa ndathandizanso ena kuchita chimodzimodzi.”

Anthu amene akudwala akamalimbikitsidwa akhoza kumaiwala mavuto awo. Taganizirani chitsanzo cha mayi wina wachikristu dzina lake Brenda, amenenso amadwala matenda a maganizo ochititsa munthu kusinthasintha zochitika. Iye anati: “Anzanga a ku mpingo akhala akundithandiza ndiponso kundimvetsa kwambiri panthaŵi imene zinthu zakhala zisakundiyendera bwino, ndipo sankandinena kuti ndikufooka mwauzimu. Nthaŵi zina akhala akunditenga mu utumiki kuti ndizikangomvetsera ndiponso nthaŵi zina akhala akundisungira mpando mu Nyumba ya Ufumu kuti ndikaloŵe anthu onse atakhalakhala kale.”

Cherie, amene tam’tchula m’nkhani yam’mbuyo ija, yemwe amadwala matenda a maganizo ochititsa munthu kungokhala woipidwa anathandizidwa kwambiri ndi akulu a mumpingo omwe n’ngachifundo ndiponso n’ngachikondi. Iye anati: “Akulu akamandiuza kuti Yehova amandikonda, akamandiŵerengera Mawu a Mulungu, Baibulo, ndi kundiuza za cholinga cha Yehova chodzabweretsa paradaiso wamtendere amene anthu azidzakhala mosangalala, ndipo akamapemphera nane, ngakhale patakhala patelefoni, ndimangomva kuti vuto langa layamba kuchepa. Ndimadziŵa kuti Yehova kapenanso abale anga sanandisiye, ndipo zimenezi zimandilimbikitsa kwambiri.”

Palibe kukayikira kulikonse pankhani yakuti achibale, ndiponso anzawo akamachita zinthu zolimbikitsa, odwalawo angathe kuthandizidwa kwambiri kuti apezeko bwino. Lucia anati: “Ndikuona kuti panopo ndikutha kuwongolera zina ndi zina pa moyo mwanga. Ine ndi mwamuna wanga tayesetsa kwambiri kulimbana ndi vuto langali, ndipo panopo zinthu zikutiyendera bwino kusiyana ndi kale.”

Anthu ambiri amene pakali pano amalimbana ndi matenda a maganizo amazindikira kuti kulimbana ndi matenda ameneŵa sikutherapo. Komano, Baibulo limatilonjeza kuti m’dziko latsopano la Mulungu, “wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.” (Yesaya 33:24) Matenda osautsa amene akuvutitsa anthu ambiri masiku anoŵa adzatha. Ndithu n’zolimbikitsa kwambiri kuganizira lonjezo la Mulungu lonena za dziko latsopano mmene matenda alionse, ndi matenda a maganizo omwe, adzathe kwamuyaya. Baibulo limanena kuti panthaŵi imeneyo, sikudzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena zowawa.—Chivumbulutso 21:4.

[Mawu Otsindika patsamba 12]

Yesu anavomereza kuti anthu amene ali ndi matenda m’thupi mwawo amafunikira dokotala.—MATEYU 9:12

[Mawu Otsindika patsamba 13]

Baibulo limatilonjeza kuti m’dziko latsopano la Mulungu, “wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.”—YESAYA 33:24