Nkhani Yabwino kwa Odwala Matendaŵa
Nkhani Yabwino kwa Odwala Matendaŵa
M’MBUYOMU, anthu ankakonda kupewa anthu odwala matenda a maganizo. Motero ambiri odwala matendaŵa ankakhala opanda anzawo ocheza nawo. Ena anali kuwasala m’zintchito. Ena, ngakhale anthu a m’banja mwawo momwe sankawafuna. Nthaŵi zambiri zimenezi zinkangowonjezera vutolo ndipo zinkalepheretsa odwalawo kupeza chithandizo.
Komabe m’zaka makumi angapo m’mbuyomu anthu adziŵa zinthu zambiri zokhudza matenda a maganizo ochititsa munthu kungokhala woipidwa ndiponso ochititsa munthu kusinthasintha zochitika. Masiku ano anthu ambiri amadziŵa kuti matenda ameneŵa n’ngochiritsika. Komano si kuti nthaŵi zonse chithandizo cha matendaŵa chimapezeka mosavuta. N’chifukwa chiyani zili choncho?
Kuzindikira Zizindikiro Zake
Matenda a maganizo sangawapeze poyeza magazi kapena mwa kuunika wodwalayo. Koma kuti awapeze amakhala akuonetsetsa khalidwe, kaganizidwe, ndiponso kachitidwe ka zinthu ka wodwalayo kwa nthaŵi yaitali ndithu. Payenera kukhala zizindikiro zingapo kuti atsimikizire kuti munthuyo alidi ndi matendaŵa. Koma vuto n’lakuti nthaŵi zina achibale ndi anzake sazindikira kuti khalidwe limene munthuyo akuonetsa likusonyeza kuti ali ndi matenda a maganizo. Dr. David J. Miklowitz analemba kuti: “Ngakhale onse atakhala kuti akuonadi kuti zochitika za munthuyo zikuoneka kuti sali bwino penapake, angathe kusiyana maganizo kwambiri pa nkhani yakuti n’chiyani chikumuchititsa zimenezo.”
Komanso ngakhale achibale atamaona kuti vutolo n’lalikuludi, zingakhale zovuta kuti wodwalayo akhulupiriredi kuti akufunika kupita kuchipatala. Ndipo ngati muli inuyo amene mukudwala n’kutheka kuti simukufuna n’komwe kuti akuthandizeni. Dr. Mark S. Gold analemba kuti: “Mwina mumakhulupiriradi maganizo amene amakubwererani m’mutu matendaŵa akakugwirani, kuti ndinu wachabechabe, motero mumangoti nanga n’kuvutikiranji kupeza chithandizo pamene muli kale munthu wopanda ntchito. N’kutheka kuti mukufuna mutakambirana ndi munthu wina za vutoli koma mumaganiza kuti ndi vuto lochititsa manyazi, kuti munalakwitsa nokha zinthu . . . . N’kutheka kuti simukudziŵa kuti zimenezi zikukuchitikirani chifukwa choti mukudwala matenda a
maganizo.” Komabe, anthu amene amadwala matenda aakulu a maganizo amafunika kwambiri kupeza chithandizo cha mankhwala.N’zoona kuti aliyense amavutika m’maganizo nthaŵi zinazake, ndipo si kuti nthaŵi zonse zikatero ndiye kuti munthuyo ali ndi matenda a maganizo. Koma bwanji ngati zikuoneka kuti kusasangalala koteroko kwachita kunyanyira? Ndipo bwanji ngati zitapitirira kwa nthaŵi yaitali ndithu, mwina milungu iŵiri kapena kuposa pamenepo? Komanso, bwanji ngati maganizo oterowo akukulepheretsani kuchita zinthu bwinobwino, kaya ndi kuntchito, kusukulu, kapena mukakhala pakati pa anthu ena? Ngati zili choncho, n’kwanzeru kuonana ndi dokotala wodziŵa bwino matendaŵa amene angathe kuzindikira komanso kupereka chithandizo cha matenda a maganizo.
Ngati pali zinthu zinazake zimene sizikuyenda bwino m’thupi mwa wodwalayo, mwina amatha kum’patsa mankhwala. Nthaŵi zina, amatha kumuuza kuti azikaonana ndi katswiri wolangiza wodwalayo mmene angalimbanirane ndi vuto lakelo. Nthaŵi zina, kugwiritsira ntchito njira ziŵiri zonsezi pamodzi kwathandiza kwambiri. * Chofunika n’kuchitapo kanthu kuti muthandizidwe. Lenore, wodwala matendaŵa yemwe tam’tchula m’nkhani yam’mbuyo ija anati: “Nthaŵi zambiri odwala amachita mantha ndiponso amachita manyazi ndi matenda awo. Komatu choyenera kuchita nacho manyazi ndicho kumangokhala osapeza chithandizo chimene mukufunikira pamene mukuona ndithu kuti muli ndi matenda.”
Lenore ananena mawu otsatiraŵa malingana ndi zimene zinam’chitikira: “Pafupifupi kwa chaka chonse ndinkangokhalira kugona. Kenaka tsiku lina ndikumvako bwino, ndinaganiza zoimba foni kuti ndilinganize zokaonana ndi dokotala.” Kenaka Lenore atamuyeza anam’peza ndi matenda a maganizo ochititsa munthu kusinthasintha zochitika, ndipo anam’lembera mankhwala. Izi zinasintha moyo wake. Lenore anati: “Ndikamwa mankhwala ndimapeza bwino, ngakhale kuti ndimafunika kuchita kukumbukira nthawi zonse kuti ndikangosiya kumwa mankhwalawo, matendawo andiyambanso.”
N’chimodzimodzinso ndi Brandon, yemwe ali ndi matenda a maganizo ochititsa munthu kungokhala woipidwa. Iye anati: “Ndisanakwanitse zaka 20, nthaŵi zambiri ndinkaganiza zongodzipha chifukwa choti ndinkangokhalira kuganiza zoti ndine wachabechabe. Matendaŵa sindinapite nawo kuchipatala mpaka pamene ndinakwanitsa zaka 30.” Monga Lenore, nayenso Brandon amamwa mankhwala a matenda akeŵa, koma palinso zinthu zina zimene zimam’thandiza. Iye anati: “Kuti ndikhale ndi moyo wabwino, ndimaonetsetsa kuti ndikuganiza zinthu zabwino ndiponso kuti ndikusamalira thupi langa. Ndimapuma mokwanira komanso ndimakhala wosamala kwambiri ndi zinthu zimene ndimadya. Chinanso, ndimayesetsa kuti m’maganizo mwanga ndi mumtima
mwanga muzikhala zinthu zabwino zochokera m’Baibulo.”Komabe Brandon anati matenda a maganizo ochititsa munthu kungokhala woipidwa ndi matenda ofunika kuchipatala osati chithandizo chauzimu. Kudziŵa zimenezi n’kofunika kwambiri kuti wodwala apeze bwino. Brandon anati: “Nthaŵi ina Mkristu mnzanga yemwe ankafuna kundithandiza anandiuza kuti, chifukwa chakuti Agalatiya 5:22, 23 amati chimwemwe ndi chipatso cha mzimu woyera wa Mulungu, ineyo ndikuvutika maganizo chifukwa choti ndachita chinthu chinachake chimene chikuletsa mzimu umenewo. Zimenezi zinawonjezera kuti ndizidziona kukhala munthu wolakwa ndiponso woipidwa kwambiri. Koma nditayamba kuthandizidwa kuchipatala, maganizo anga anayamba kukhazikika. Ndinayamba kupeza bwino kwambiri! Ndipo ndinayamba kuona kuti ndimangochedwa kulandira chithandizochi.”
Kuthana Nawo Matendaŵa
Ngakhale atakhala kuti munthuyo amupeza ndi matendawo ndipo wayamba kulandira mankhwala, matendaŵa angavutitsebe wodwalayo. Kelly, amene akuvutika ndi matenda aakulu a maganizo, amayamikira chithandizo chimene akum’patsa madokotala odziŵa bwino za matenda akeŵa. Komabe kuphatikiza pamenepo, iye anaonanso kuti kulimbikitsidwa ndi anthu ena n’kofunika kwambiri. Poyamba, Kelly sankakhala womasuka kupempha thandizo kwa anthu ena chifukwa ankaopa kuti azimuona ngati munthu wovuta. Iye anati: “Ndinayenera kuphunzira kupempha thandizo komanso kulola kuthandizidwa. Pamene ndinayamba kuuza ena za mavuto anga m’pamene ndinayambira kupeza bwino.”
Kelly ndi wa Mboni za Yehova, motero amasonkhana ndi a Mboni anzake ku Nyumba ya Ufumu. Koma nthaŵi zina, ngakhale misonkhano yosangalatsayi imamuika pamavuto ena. Iye anati: “Nthaŵi zambiri, ndimasoŵa mtendere kwabasi chifukwa cha kuwala kwa magetsi, piringupiringu wa anthu, ndiponso phokoso. Kenaka ndimayamba kudziona kuti ndikulakwa, ndipo zikatero matenda aja amawonjezeka chifukwa ndimangoona ngati kuti ndili ndi matendaŵa chifukwa cha kufooka kwanga mwauzimu.” Kodi Kelly amathana nalo bwanji vutoli? Iye anati: “Ndaphunzira kuti matenda a maganizo n’ngofunika kulimbana nawo mwakhama. Si kuti ndi muyezo wosonyeza mmene ndimakondera Mulungu kapena Akristu anzanga ayi. Sasonyeza mmene moyo wanga wauzimu ulilidi.”
Lucia, amene tam’tchulapo kale m’nkhani ina m’mbuyomu,
anayamikira chithandizo chabwino kwambiri chimene walandira kuchipatala. Iye anati: “Kuonana ndi dokotala wa za maganizo kwandithandiza kwambiri kuti ndidziŵe mmene ndingalimbanirane ndiponso kuthanirana ndi kusinthasintha kwa maganizo anga chifukwa cha matendaŵa. Lucia anagogomezeranso kufunika kwa kupuma. Iye anati: “Kugona n’kofunika mukakhala ndi vuto lomasangalala monyanyira. Ndikamagona mopereŵera, vuto langa limakula kwambiri. Ngakhale tulo tikamapanda kubwera, ndinadzizoloŵeza kuti ndizingokhalabe chogona n’kumapuma, m’malo modzuka.”Sheila, amenenso tam’tchulapo kale, amaona kuti n’zothandiza kukhala ndi buku lolembamo mmene akumvera tsiku ndi tsiku. Iye anaona kuti zinthu zikusintha ndithu m’maganizo mwake. Komabe amakumana ndi mavuto. Sheila anati: “Nthaŵi zina ndimangotoperatu mwakuti ndimangozindikira kuti ndayamba kuganiza zinthu zosathandiza n’komwe. Komabe panopa ndimadziŵa mmene ndingachepetsere maganizo ameneŵa.”
Kulimbikitsidwa ndi Mawu a Mulungu
Baibulo limalimbikitsa anthu onse amene akuvutika chifukwa cha “zolingalira” zawo. (Salmo 94:17-19, 22) Mwachitsanzo, Cherie anaona kuti lemba la Salmo 72:12, 13 n’lolimbikitsa kwambiri. Ponena za Yesu Kristu, yemwe ndi Mfumu yosankhidwa ndi Mulungu, pa lembali wamasalmo ananena kuti: “Adzapulumutsa waumphaŵi wofuulayo; ndi wozunzika amene alibe mthandizi. Adzachitira nsoni wosauka ndi waumphaŵi, nadzapulumutsa moyo wa aumphaŵi.” Cherie analimbikitsidwanso ndi mawu a mtumwi Paulo olembedwa pa Aroma 8:38, 39, akuti: “Ndakopeka mtima kuti ngakhale imfa, ngakhale moyo, ngakhale angelo, ngakhale maufumu, ngakhale zinthu zilipo, ngakhale zinthu zilinkudza, ngakhale zimphamvu, ngakhale utali, ngakhale kuya, ngakhale cholengedwa china chilichonse, sichingadzakhoze kutisiyanitsa ife ndi chikondi cha Mulungu.”
Elaine, yemwe amadwala matenda a maganizo ochititsa munthu kusinthasintha zochitika, amaona kuti ubwenzi wake ndi Mulungu umam’thandiza kwambiri. Iye amalimbikitsidwa kwambiri ndi mawu aŵa a wamasalmo: “Inu, Mulungu, simudzaupeputsa mtima wosweka.” (Salmo 51:17) Iye anati: “Ndalimbikitsidwa kwambiri podziŵa kuti atate wathu wachikondi wakumwamba, Yehova, amamvetsa. Ndalimbikitsidwa kwambiri popemphera kwa iye, makamaka panthaŵi zimene ndakhala ndikuda nkhaŵa kwambiri ndiponso kusautsika maganizo.”
Monga mmene taonera, kukhala ndi matenda a maganizo n’kovuta kwambiri. Komabe, Cherie ndi Elaine anaona kuti kudalira Mulungu popemphera limodzi ndi kulandira chithandizo choyenerera kunawathandiza kuti moyo aziumvako bwino. Komabe, kodi anthu amene amadwala matenda a maganizo ochititsa munthu kusinthasintha zochitika kapenanso ochititsa munthu kungokhala woipidwa angathandizidwe bwanji ndi achibale komanso anzawo?
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 8 Galamukani! silangiza anthu kuti atsatire njira yakutiyakuti ya chithandizo. Akristu ayenera kuonetsetsa kuti chithandizo chilichonse chimene akutsatira sichikutsutsana ndi mfundo za m’Baibulo.
[Mawu Otsindika patsamba 10]
“Nditayamba kuthandizidwa, maganizo anga anayamba kukhazikika. Ndinayamba kupeza bwino kwambiri!” Anatero BRANDON
[Bokosi patsamba 9]
Zimene Mwamuna Wina Anazindikira pa Matenda a Mkazi Wake
“Lucia asanayambe kudwala anathandiza anthu ambiri chifukwa cha nzeru zake. Ngakhale panopa, zikuoneka kuti mkazi wanga akamapezako bwino, anthu odzam’chezera amasangalala chifukwa cha kuchezeka kwake. Chinthu chimene anthu ambiri sazindikira n’chakuti Lucia amati pena kusangalala mochita kunyanyira pena n’kungokhala woipidwa. Umu ndi mmene amakhalira matenda a maganizo ochititsa munthu kusinthasintha zochitika, omwe Lucia wakhala nawo kwa zaka zinayi.
“Panthaŵi imene amakhala wosangalala monyanyira, si zachilendo kwa Lucia kukhala asanagone mpakana m’ma wani koloko, thu koloko, ngakhale fili koloko usiku, koma n’kumaganizabe bwinobwino zochita zinazake. Mphamvu zimachita kumuyabwa m’thupi. Amatha kuthamanga magazi ndi nkhani zazing’ono kwambiri ndipo amangosakaza ndalama mosayenerera. Amatha kupita pa malo oopsa kwambiri, podziona kuti iyeyo m’patali ndipo palibe choopsa chilichonse chimene chingam’chitikire, kaya chomuwonongera khalidwe, chomuvulaza kapena china chilichonsecho. Kuwonjezera pa zimenezi, amafuna kudzipha. Nthaŵi zonse akangoleka kusangalala konyanyira kuja amayamba kukhala woipidwa mochita kunyanyiranso.
“Moyo wanga wasintha kwambiri. Ngakhale kuti Lucia akulandira chithandizo, zinthu zimene iyeyo ndi ine tingakwanitse kuchita panopa n’zosiyana kwambiri ndi zimene tikanatha kukwanitsa m’mbuyomo kapena zimene tingadzathe kukwanitsa m’tsogolo. Zimene tingachite zimangodalira mmene zinthu zilili panthaŵi imeneyo. Panopa ndinangozoloŵera moyo wotha kusintha mwamsanga malingana ndi mmene zinthu zilili ndipo kale sindinkaganizako kuti ndingathe kutero.” Anafotokoza zimenezi ndi Mario.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 11]
Akakulemberani Mankhwala
Anthu ena amaona ngati kuti si chamuna kumwa mankhwala chifukwa cha matenda ameneŵa. Koma taionani nkhaniyi motere: Munthu wodwala matenda a shuga ayenera kumalandira chithandizo, ndipo nthaŵi zina amapatsidwa jakisoni wa matenda a shuga. Kodi kutero n’kusonyeza kulephera? Ayi ndithu! Iyi ndi njira yothandiza kuti thupi la wodwalayo lizigwiritsira ntchito bwino zakudya kuti iyeyo akhale wathanzi.
N’chimodzimodzinso kumwa mankhwala mukakhala ndi matenda a maganizo ochititsa munthu kungokhala woipidwa kapena ochititsa munthu kusinthasintha zochitika. Ngakhale kuti anthu ambiri athandizidwa popatsidwa malangizo akuti amvetsetse matenda awo, ndibwino kusamala. Munthu akamadwala matendaŵa chifukwa cha kusokonekera kwa thupi lake, sangachire pongomulimbikitsa basi. Steven, yemwe amadwala matenda a maganizo ochititsa munthu kusinthasintha zochitika analongosola kuti: “Dokotala amene anandithandiza analongosola nkhaniyi motere: Ngakhale munthu mutamuphunzitsa luso lonse loyendetsera galimoto, maphunziro onsewo sangakhale opindulitsa ngati mutam’patsa galimoto yopanda chiwongolero ndi mabuleki kuti ayendetse. N’chimodzimodzinso ndi matendaŵa, malangizo paokha sangapindulire munthu wodwala matenda a maganizo. Chinthu choyambirira chimene chimafunika kwambiri ndicho kumupatsa mankhwala othandiza kuti zinthu ziyambe kuyenda bwino m’mutu mwake.”
[Chithunzi patsamba 10]
Baibulo limalimbikitsa anthu onse amene amasautsika ndi maganizo