Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Khalidwe Lanu Limayendera Gulu la Magazi Anu?

Kodi Khalidwe Lanu Limayendera Gulu la Magazi Anu?

Lingaliro la Baibulo

Kodi Khalidwe Lanu Limayendera Gulu la Magazi Anu?

M’MAYIKO ena, n’chinthu chofala kuyesa kudziŵa khalidwe la munthu poona gulu la magazi ake. Mwachitsanzo, ku Japan si zachilendo kumva anthu akulonjerana pofunsana funso lakuti, “Kodi magazi anu ndi a gulu liti?” Anthu amene amakhulupirira zimenezi amanena kuti anthu a magazi a gulu la A ndi ofatsa, n’ngodalirika pa zinthu, ndipo n’ngokonda kukayikira ena; ndipo anthu amene magazi awo ali m’gulu la B ndi owona mtima, ndi owoloŵa manja, amakhumudwakhumudwa komanso sachedwa kupusitsidwa. Ndipotu pa magulu ena onse a magazi amanenaponso zinthu zangati zimenezi. Amanenanso kuti munthu wokhala ndi magazi a m’gulu linalake zingamuvute kapena sizingamuvute kugwirizana ndi munthu wina amene magazi ake ali m’gulu lakutilakuti.

Motero anthu ena amaona kuti kudziŵa gulu la magazi n’kofunika poika ana asukulu m’magulu, posankha mabwana m’makampani, ngakhalenso posankha munthu woti mukwatirane naye. Kodi pali umboni uliwonse wosonyeza kuti gulu la magazi athu ndilo limatipangitsa kuti tikhale anthu a khalidwe linalake? Kodi pali ziphunzitso zilizonse za m’Baibulo zimene zimakhudzapo pa nkhani imeneyi?

Kodi Gulu la Magazi N’chiyani?

Buku lotchedwa The World Book Multimedia Encyclopedia limalongosola kuti: “Makungu a maselo ofiira a m’magazi amakhala ndi mapuloteni otchedwa ma antigen. Pali mitundu 300 yodziŵika ya ma antigen ameneŵa.” Anthu ena ali ndi mitundu inayake ya mapuloteni ameneŵa ndipo ena alibe ndipo pali mitundu ina imene munthu sangakhale nayo panthaŵi imodzimodziyo. Motero bukulo limanenanso kuti, “asayansi anagaŵa magazi a anthu m’magulu osiyanasiyana oyendera kupezeka kapena kusapezeka kwa mitundu inayake ya ma antigen.”

Njira yotchuka kwambiri ya magulu a magazi ndi yotchedwa ABO, imene amagaŵira magazi a anthu m’magulu anayi otchedwa A, B, AB, ndi O. Kuphatikiza apo, njira ina yotchedwa Rh n’njofalanso kwambiri. Kwenikweni pali njira 20 zogaŵa magazi m’magulumagulu. Motero n’zachionekere kuti magazi n’ngovuta kuwafotokoza bwinobwino. Buku la Encyclopædia Britannica limati: “Pakuti m’magazi muli ma antigen ambiri a maselo ofiira amitundu yosiyanasiyana m’povuta kwambiri kuti anthu akhale ndi magazi ofanana pokhapokha ngati anthuwo ali mapasa ofanana ndendende.”

Zimenezi zikusonyeza kuti kunena mwatchutchu, munthu aliyense ali ndi “gulu la magazi” lakelake. Motero mfundo yakuti anthu amene magazi awo ali m’gulu lakutilakuti amafanana zochitika n’njopanda umboni. Zikuoneka kuti pali zinthu zosiyanasiyana zimene zimatichititsa anthufe kukhala ndi khalidwe limene tili nalo.

Kodi Khalidwe Lathu Timalitengera Kuti?

“Akati khalidwe la munthu amatanthauza zochitika za munthu, kaya n’zobadwa nazo ngakhalenso zochita kutengera, zimene zimasiyanitsa munthu aliyense ndi wina,” linalongosola motero buku la Encyclopædia Britannica. Inde, kuphatikiza pa zinthu zochita kubadwa nazo, palinso zinthu zina zimene zimakhudza khalidwe lathu monga zochitika za m’banja mwathu, maphunziro athu, anzathu ocheza nawo, komanso zinthu zabwino kapena zoipa zimene takumanapo nazo. Motero, sikuti khalidwe lathu limangodalira pa zinthu zokhudza magazi zokha ayi. Ngakhale mapasa ofanana ndendende, amene magazi awo amakhala ofanana, nthaŵi zambiri amakhala ndi khalidwe losiyana.

Mfundo ina yofunika n’njakuti munthu angathe kusintha khalidwe. Mtumwi Paulo anagogomezera kuti ziphunzitso zachikristu zili ndi mphamvu yaikulu kwambiri yosintha anthu. Iye analemba kuti: ‘Vulani munthu wakale pamodzi ndi ntchito zake, ndipo valani watsopano, amene alikukonzeka watsopano, kuti akhale nacho chizindikiritso, monga mwa chifaniziro cha Iye amene anam’lenga iye.’ (Akolose 3:9, 10) Akristu amazindikira kuti ndi ochimwa ndiponso kuti anatengera kukonda kuchita zochimwa. Motero ayenera kusintha khalidwe lawo kuti Mulungu ayambe kuwayanja.

Kodi n’chiyani chimawathandiza kuchita zimenezi? Ndicho mphamvu ya mawu a Mulungu, kapena kuti uthenga wake. Pankhani ya mphamvu ya mawu a Mulungu, amene tsopano ali m’Baibulo, Paulo analemba kuti: “Mawu a Mulungu ali amoyo, ndi ochitachita, ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse, napyoza kufikira kugaŵira moyo ndi mzimu, ndi zimfundo ndi mafuta a m’mafupa, nazindikiritsa zolingirira ndi zitsimikizo za mtima.” (Ahebri 4:12) Munthu akalola kuti mzimu wa Mulungu uzimulamulira ndi kuyesetsa kutsatira khalidwe labwino limene limalongosoledwa m’Baibulo, pang’ono ndi pang’ono khalidwe lake lingasinthe. Khalidwe lachikristu, lomwe munthu amakhala nalo m’njira imeneyi limadziŵika ndi zinthu monga “mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, [ndi] kuleza mtima.”—Akolose 3:12.

Mkristu Azichita Zinthu Moganizira

Inde, m’Baibulo mulibe mfundo imene imaletsa kuphunzira za magulu a magazi. Koma zogwirizanitsa maguluŵa ndi khalidwe la anthu, iyo ndiye ndi nkhani ina. Monga mmene timachitira ndi nkhani zonse zokhudza moyo wathu, pankhani imeneyi, tiyenera kulola kuti Mawu a Mulungu atitsogolere. (Salmo 119:105) Komanso m’pofunika kuchita zinthu moganizira.—Afilipi 4:5.

Munthu akamalephera dala kusintha khalidwe lake ponamizira kuti vuto ndi gulu la magazi ake ndiye kuti sakuganiza bwino. Zilibe kanthu kuti ali ndi magazi otani, Akristu ayenera kupitiriza kusintha khalidwe lawo kuti likhale lofanana kwambiri ndi makhalidwe a Yehova ndi a Yesu.—Aefeso 5:1.

Kuphatikiza apo, Akristu amayesetsa kuona ena mmene Yehova amawaonera. “Mulungu alibe tsankhu.” (Machitidwe 10:34, 35) Yehova amasangalala ndi anthu osiyanasiyana. Motero kupeŵa anthu enaake chifukwa cha gulu la magazi awo n’kusaganizira ndiponso n’kosagwirizana ndi mfundo zachikristu. N’chimodzimodzinso ngati munthu amacheza ndi anthu okhawo amene amati amagwirizana nawo gulu la magazi. Baibulo limatilangiza kuti: “Ngati musamala maonekedwe [“ngati mumakondera,” NW], muchita uchimo.”—Yakobo 2:9.

Sayansi ndi umisiri zikum’kabe patsogolo, motero pali zinthu zambiri zomwe zatulukiridwa zokhudza thupi la munthu ndiponso pali mfundo zina zambiri zomwe akungoziganizira. N’zosadabwitsa kuti anthufe timachita nazo chidwi zinthu zoterezi. Komabe n’kwanzeru kwa Akristu kulola kuti Baibulo ndilo liziwathandiza pa maganizo awo, osati mfundo zosatsimikizirika za anthu. Pa zochitika zonse m’moyo, Akristu ayenera ‘kuyesa kaye zinthu zonse’ ndi ‘kusungapo chimene chili chokoma.’—1 Atesalonika 5:21.

Ngati mukufuna kudziŵa zambiri kapena kuti wina aziphunzira nanu Baibulo panyumba panu kwaulere, lemberani Mboni za Yehova, Box 30749, Lilongwe 3, Malawi, kapena ku adiresi yoyenera pa maadiresi osonyezedwa patsamba 5.