Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Nthaŵi Yochita Homuweki Ndingaipeze Kuti?

Kodi Nthaŵi Yochita Homuweki Ndingaipeze Kuti?

Achinyamata Akufunsa Kuti . . .

Kodi Nthaŵi Yochita Homuweki Ndingaipeze Kuti?

‘Ndili m’kalasi lomaliza ku sekondale ndipo ndapanikizika modetsa nkhaŵa. . . . Zoti ndichite zangoti mbwee, osati mwamaseŵera ayi. Ndilibe nthaŵi yoti ndizichite,’ anatero mtsikana wina wa zaka 18.

KODI mumaona kuti mukupanikizika ndi homuweki yambiri imene amakupatsani kusukulu kuti mukachitire kunyumba madzulo alionse? Ngati ndi choncho, si inu nokha amene mumatero. Lipoti lina la atolankhani ku United States linati: “Pamene sukulu m’dziko muno zikuyesetsa kulimbikitsa zoti pakhale njira zabwino ndiponso kuti ana azikhoza bwino pa mayeso a boma, sukuluzo zikuunjikira homuweki anawo. Ana a sukulu za sekondale m’madera ena akunena kuti amathera maola oposa atatu usiku uliwonse kuchita homuweki. Kafukufuku wina amene a yunivesite ya Michigan anachita anasonyeza kuti masiku ano, ana aang’ono akuchita homuweki yoŵirikiza katatu kuposa mmene ana ankachitira zaka 20 zapitazo.”

Si ku United States kokha kumene ana asukulu akupatsidwa homuweki yambiri. Mwachitsanzo, pamene kumeneko ana pafupifupi 30 mwa ana 100 alionse a zaka 13 anati amathera maola oposa aŵiri akuchita homuweki tsiku lililonse, ku Taiwan ndi ku Korea, ana 40 mwa ana 100 alionse anati amatero, ndipo ku France, ana oposa 50 mwa ana 100 alionse amatero. Katie, yemwe amaphunzira pa yunivesite ina ku United States anadandaula kuti: “Nthaŵi zambiri ndimapanikizika kwambiri homuweki yanga ikachulukitsitsa.” Marilyn ndi Belinda, amene amaphunzira ku Marseilles, ku France, ananenanso zofanana ndi zimenezi. Marilyn anati: “Nthaŵi zambiri timathera maola aŵiri kapena oposa pamenepo usiku uliwonse tikuchita homuweki. Ukakhala ndi ntchito zinanso zoti uchite, zimakhala zovuta kwambiri kuti upeze nthaŵi yochitira zimenezo.”

Kodi Nthaŵi Ndingaipeze Kuti?

Kodi sizikanakhala bwino ngati mukanati muzitha kungowonjezera maola angapo patsiku nthaŵi imene mwawafuna kuti mumalize homuweki yanu ndi kuchita zina zilizonse zimene mukufunikira kuchita? Komatu, mungathe kuchita zofanana ndi zimenezi ngati muphunzira mfundo ya m’Baibulo imene ili pa Aefeso 5:15, 16, yakuti: “Penyani bwino umo muyendera, si monga opanda nzeru, koma monga anzeru; akuchita machawi [“oombola nthaŵi,” NW].” Ngakhale kuti wolemba Baibuloyo sanali kunena za homuweki polemba mawu amenewo, mfundo ya lembali ingagwiritsidwe ntchito pa moyo wa tsiku ndi tsiku. Mukamaombola chinachake, mumafunika kulolera kusiya chinthu china kuti mupeze chimene mukufunacho. Mfundo yake apa ndi yoti kuti mupeze nthaŵi yoŵerenga, mudzafunika kusiya zinthu zina. Koma kodi ndi zinthu ziti zimene mungasiye?

Mtsikana wina dzina lake Jillian analangiza kuti: “Konzani ndandanda ya zinthu zimene mukufuna kuyambirira kuzichita.” M’mawu ena, onani kuti ndi zinthu ziti zimene zili zofunika kwambiri. Misonkhano yachikristu ndiponso zinthu zina zauzimu ziyenera kukhala poyambirira. Komanso, musaiwale ntchito zimene mufunika kuchita panyumba, pamodzinso ndi homuweki.

Kenako, yesani kulemba mmene mukugwiritsiradi ntchito nthaŵi yanu kwa mlungu umodzi kapena kuyandikira mlungu ngakhalenso kuposa pamenepo. Mwina mungadabwe ndi zimene mungapeze. Kodi mumatha nthaŵi yochuluka motani mukuonera TV? kugwiritsa ntchito intaneti? kukaonerera mafilimu? kulankhula patelefoni? kukacheza ndi anzanu? Pamene mwachita zimenezi, kodi mukuona kusiyana kotani pakati pa nthaŵi imene mwathera mukuchita zimenezi ndi nthaŵi imene mumachita zinthu zofunika kwambiri zimene munaika pa ndandanda zija? Mwina mungafunike kungoona nthaŵi imene mumathera kuonerera TV, kuimba foni, kapena kugwiritsa ntchito intaneti kuti mupeze mbali zimene mungaomboleko nthaŵi ina yochulukirapo.

Zinthu Zofunika Kwambiri Zikhale pa Malo Oyamba

Zimenezi sizikutanthauza kuti musamaonerere TV kapena kudzipatula kwa anthu ena. Mwina mungafunike kukhazikitsa mfundo yakuti, “Zinthu zofunika kwambiri zikhale pa malo oyamba.” Lemba la m’Baibulo limene mungatsatire limati: “Mutsimikizire [kuchita] zinthu zofunika kwambiri.” (Afilipi 1:10, NW) Mwachitsanzo, popeza sukulu ndi yofunika kwambiri, mungadzikhazikitsire lamulo loti simuyatsa TV mpaka mutamaliza kugwira ntchito zapakhomo, kuphunzira kokonzekera misonkhano yachikristu, ndiponso kumaliza homuweki yanu. N’zoona kuti zingakhale zokhumudwitsa kusaonerera pulogalamu ya pa TV imene mumaikonda kwambiri. Koma kunena mwachilungamo, kodi ndi kangati pamene munafuna kuti muonere pulogalamu yokhayo imene mumaikonda komano n’kupezeka kuti mukuonerabe TV nthaŵi yonse ya madzulo, n’kulephera kuchita china chilichonse?

Komanso, mufunika kukumbukira kuti kupezeka pa misonkhano yachikristu n’kofunika kwambiri. Mwachitsanzo, ngati mukudziwa kuti mudzalemba mayeso kapena kuchita homuweki yofunika kwambiri m’tsogolo, mungayesere kuchitiratu zimenezo kuti zisasokoneze kupezeka kwanu pa misonkhano. Mwina mungayeserenso kulankhula ndi aphunzitsi anu mmene zinthu zilili, kuwadziŵitsa kuti mungayamikire kwambiri ngati atakudziŵitsani pasadakhale za homuweki iliyonse imene mwina mungafunike kuichita madzulo a tsiku limene mumakhala ndi misonkhano. Aphunzitsi ena angakhale okonzeka kukuthandizani.

Mfundo ina yothandiza ndi imene Baibulo limaphunzitsa pankhani ya mnzake wa Yesu dzina lake Marita. Iye anali mkazi wodziŵa kutakataka, koma sanaike zinthu zofunika kwambiri pa malo oyamba. Nthaŵi ina, anadzilemetsa pokonzera Yesu chakudya chimene chiyenera kuti chinali chapamwamba, pamene mchemwali wake, Mariya anali kumvetsera zimene Yesu ankanena m’malo momuthandiza. Marita atadandaula chifukwa cha zimenezi, Yesu anamuyankha kuti: “Marita, Marita, uda nkhaŵa nuvutika ndi zinthu zambiri; koma chisoŵeka chinthu chimodzi, pakuti Mariya anasankha dera lokoma limene silidzachotsedwa kwa iye.”—Luka 10:41, 42.

Tikuphunzirapo chiyani pamenepa? Tikuphunzira kuti tisamavutike ndi zambiri. Kodi mungatsatire bwanji mfundo imeneyi pa moyo wanu? Kodi ‘mukuda nkhaŵa ndi kuvutika ndi zinthu zambiri,’ mwina kuyesa kuchita homuweki komanso panthaŵi yomweyo mukugwira ganyu? Ngati mukugwira ganyu, kodi anthu a m’banja mwanu akufunikiradi ndalamazo moti sangachitire mwina? Kapena kodi mukungofuna kukhala ndi ndalama zina zapadera zogulira zinthu zimene mukufuna koma zomwe mukhoza kukhala bwinobwino popanda zimenezo?

Mwachitsanzo, m’mayiko ena achinyamata amafunitsitsa kugula magalimoto awoawo. Mlangizi wina wa sukulu ya sekondale, Karen Turner, anafotokoza kuti “achinyamata masiku ano amaumirizika kwambiri kuchita zinthu zoti apeze ndalama chifukwa kusamalira galimoto kumafuna ndalama zambiri.” Komabe, Turner anamaliza kuti: “Zimakhala zosokoneza kwambiri ngati munthu amayesa kuchita zinthu zambiri monga zochitika zina zakusukulu zimene amachita atatuluka m’kalasi, n’kuphatikizapo kugwira ntchito, pamodzinso ndi homuweki yambiri. Choncho zochita zimamuchulukira wophunzirayo.” Muzichulukitsiranji zochita ngati palibe chifukwa chenicheni chochitira zimenezo? Ngati mukulephera kuchita homuweki yanu, mwina mungamagwire ntchitoyo kwa maola ochepa mwinanso kungoisiya kumene.

‘Ombolani’ Nthaŵi Kusukulu

Kuwonjezera pa kupeza maola ena pa zinthu zimene mumachita mutaŵeruka kusukulu, ganizirani mmene mungagwiritsire ntchito bwino nthaŵi yanu muli kusukulu komweko. Josue anati: “Ndimayesetsa kuchita homuweki yambiri mmene ndingathere panthaŵi yoŵerenga kusukulu. Mwakuchita zimenezi, ndimakhala ndi mpata wofunsa aphunzitsi pakakhala mfundo ina imene sindinamvetse pamene tinali kuphunzira tsiku limenelo.”

Chinthu china chimene mungaganizire kuchita chingakhale kuchepetsa maphunziro omwe mukutenga amene mumakhala ndi ufulu wosankha. Mwina mungafunikenso kusiya zochita zina zimene mumachita mukatuluka m’kalasi. Mwa kusintha zina ndi zina m’mbali zimenezi, mungapeze nthaŵi yochuluka yoti muziŵerenga.

Kugwiritsa Ntchito Bwino Nthaŵi

Chabwino, tinene kuti mwasiya zinthu zina zosafunika kwenikweni ndiponso mwasintha zina ndi zina ndipo motero mwapeza nthaŵi yochulukirapo yoti mungachite homuweki. Kodi mudzaigwiritsa ntchito bwino motani nthaŵi imeneyo? Ngati mungathe kuchita ntchito yochulukirapo kuposa imene munkachita m’nthaŵi imeneyo, kodi zimenezo sizikufanana ndi kuwonjezera nthaŵi ina yochulukirapo pa nthaŵi imene munali nayoyo? Choncho naŵa malingaliro amene angakuthandizeni kuti muzigwiritsa ntchito bwino nthaŵi yanu.

Konzani zochita. Musanayambe homuweki yanu, ganizirani kaye zinthu ngati izi: Kodi ndi phunziro liti limene mufunika kuliyambirira? Kodi homuwekiyo iyenera kutenga nthaŵi yochuluka motani? Kodi ndi zinthu ziti zimene mudzafunika kugwiritsa ntchito pochita homuweki yanuyo, kaya ndi mabuku, mapepala, zolembera, kapena makakyuleta?

Pezani malo oŵerengera. Ngati n’kotheka, ayenera kukhala malo oti alibe zododometsa. Mtsikana wina dzina lake Elyse ananena kuti: ‘Ngati muli ndi desiki, igwiritseni ntchito. Mukakhala tsonga zimathandiza kuti muike maganizo kwambiri pa zimene mukuchitazo m’malo mochita zimenezo mutagona.’ Ngati mulibe chipinda chanokha, mwina azichimwene kapena ang’ono anu ndi azichemwali anu angakhale okonzeka kukupatsani mpata panthaŵi imene mumaŵerengayo. Kapena mwina mungakaŵerengere ku paki inayake kapena ku laibulale imene aliyense wofuna angaŵerengereko. Ngati muli ndi chipinda chanokha, musasokoneze zimene mukufuna kuchita poyatsa TV kapena kumvetsera nyimbo zomwe zingakudodometseni pamene mukuŵerenga.

Muzipumapuma. Mukaona kuti mukukanika kuika maganizo kwambiri pa zimene mukuchitazo pakapita nthaŵi, kupuma pang’ono kungakuthandizeni kuyambanso kuika maganizo pa zimene mukuchitazo.

Musazengereze! Katie, amene tamutchula cha kumayambiriro kwa nkhani ino anati: “Ndimazengereza nthaŵi zonse. Sindiyamba kuchita homuweki imene ndapatsidwa mpaka nthaŵi imene ndikufunika kukapereka itatsala pang’ono.” Peŵani kuchita zinthu mozengereza mwa kukhala ndi ndandanda yotsimikizika yochitira homuweki yanu ndipo itsatireni nthaŵi zonse.

Za kusukulu ndi zofunika kwambiri, koma monga mmene Yesu ananenera kwa Marita, zinthu zauzimu, zomwe zili “dera lokoma,” ndizo zofunika koposa. Onetsetsani kuti homuweki sikudodometsa zinthu zofunika kwambiri monga kuŵerenga Baibulo, kuchita nawo utumiki, ndi kupezeka pa misonkhano yachikristu. Zimenezi ndi zinthu zimene zidzakupindulitsani m’moyo wanu kosatha!—Salmo 1:1, 2; Ahebri 10:24, 25.

[Zithunzi patsamba 15]

Kuchita zinthu zochulukitsitsa kungakuchititseni kuvutika kupeza nthaŵi yochitira homuweki

[Chithunzi patsamba 15]

Kukonza bwino zinthu kungakuthandizeni kupeza nthaŵi yochulukirapo yochitira homuweki