Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ku Namaqualand Kumachitika Zodabwitsa Chaka ndi Chaka

Ku Namaqualand Kumachitika Zodabwitsa Chaka ndi Chaka

Ku Namaqualand Kumachitika Zodabwitsa Chaka ndi Chaka

YOLEMBEDWA NDI WOLEMBA GALAMUKANI! KU SOUTH AFRICA

Maluŵa a mitundumitundu amaoneka pa chidikha chachikulu kwambiri. Nthaŵi zambiri alendo akadzionera okha zimene zimachitika chaka ndi chaka ku Namaqualand salephera kutulutsa mawu osonyeza kuchita nazo chidwi. Mlendo wina atadabwa nazo ananena kuti: “Munthu ukakhala kuti ukuona zimenezi koyamba, maluŵawo amaoneka ngati ziphalaphala zotuluka pa ming’alu ya miyala, zomwe zimatuluka pang’onopang’ono n’kudzadza malo onsewo ndi mtundu wonkira ku chikasu wowala kwambiri.”

Komabe, kodi n’chiyani chimachititsa nyengo imene maluŵaŵa amatuluka kukhala yochititsa chidwi kwambiri? Dera la Namaqualand ndi chigawo chachikulu chouma chimene chili kumpoto chakumadzulo kwa dziko la South Africa. Cha kumpoto kwa derali kuli mapiri, ndipo kuseri kwa mapiriwo kuli mtsinje wa Orange womwe wapanga malire a chigawochi mbali imeneyo. Dera la Namaqualand lomwe ndi lokulirapo kuposa dziko la Switzerland (pafupifupi masikweya kilomita 50,000), ndi lalitali makilomita pafupifupi 200 kuchokera kumpoto kukafika kumwera, kungopitirira pang’ono theka la ulendo wofika ku Cape Town kuchokera kumeneko. Nthaŵi zambiri pachaka, ku dera limeneli lomwe ndi louma komanso la miyala, kumatentha kufika pa madigiri seshasi 40 masana ndipo usiku kumazizira kwambiri kufika pa madigiri seshasi −8. Popeza kulibe nyanja kapena mitsinje ndipo madzi amene amapezeka ndi a pansi panthaka ndipo amawawa mchere, dera la Namaqualand limaoneka ngati silosangalatsa mpaka itafikanso nthaŵi imene kumachitika zodabwitsa za pachakazi.

Chaka chilichonse, mvula ikangotha kuyambira kuchiyambi kwa mwezi wa August kudzafika m’kati mwa mwezi wa September, dera la chigwa la Namaqualand limene nthaŵi zambiri limakhala louma limatulutsa maluŵa ochuluka zedi. Dera lonselo limangooneka maluŵa achikasu, a pinki, oyera, ofiirira, ndi a bluu. Popeza maluŵaŵa amaoneka kwa milungu yochepa chabe pachaka, anthu amayembekezera mwachidwi pamene alendo ochokera madera osiyanasiyana padziko lonse amakonzekera kudzadyetsa maso awo poonerera maluŵa ochititsa chidwi ameneŵa.

Zimene zimachititsa kuti maluŵawo atuluke ndi kuoneka okongola motero ndi mvula yochuluka bwino ndiponso kuwala kwa dzuwa kokwanira bwino. Ndiyeno wina aliyense amalakalaka kuti mphepo yochokera kum’mawa isabwere, chifukwa ikayamba kuomba imachititsa kuti maluŵawo omwe ndi osalimba afote msanga ndipo mitundu yokongolayo imathera pomwepo.

Chinanso chimene chimachititsa kuti dera la Namaqualand likhale lochititsa chidwi n’chakuti derali limatulutsa mbewu za maluŵa zambirimbiri. Komabe, ambiri mwa maluŵawo samera chaka ndi chaka. Amaonetsa kukongola kwawo pa nyengo yapadera yoyenerana nawo. Ngakhale kuti mbewu zina zimamera patangotha chaka chimodzi chokha, zina zimangokhala osamera kwa nyengo zingapo, mpaka itafika nyengo yabwino kuti zimere. Mlendo wina anafotokoza kuti: “Chipangidwe cha mbewu zina n’chakuti zimatha zokha kudziteteza kuti zisamere nyengo yake isanafike. M’malo momera mvula ikangogwa kamodzi kokha pomwe kumakhala kukutentha, mbewu zoterozo zimamera pokhapokha kukazizira ndipo kuli chinyezi, zomwe zimakhala zofunika kwambiri kuti zikule ndi kukhalabe ndi moyo m’dera lotentha kwambiri limeneli.”

Chaka chilichonse kumakhala maluŵa osiyana ndi zaka zina, malinga ndi mmene mvula yagwera ndiponso ngati mphepo yowononga maluŵa siinaombe. Chifukwa cha zimenezi zaka zina kumatuluka maluŵa okongola kwambiri kuposa zaka zina. Buku lakuti Namaqualand—South African Wild Flower Guide, linafotokoza kuti: “Chifukwa chakuti maluŵa alionse amafuna katenthedwe kenakake kuti amere, ndipo mvumbi woyamba ungagwe kuyambira mu April mpaka mu July (miyezi yomwe katenthedwe kake n’kosiyana), chaka ndi chaka kumamera maluŵa osiyanasiyana, malinga ndi nthaŵi imene mvula yoyamba yagwera.”

Inde, kulidi maluŵa a mitundu yosiyanasiyana, yoposa 4,000, ndipo mtundu uliwonse uli ndi kakulidwe kake, kaonekedwe kake, ndiponso kameredwe kake. M’madera ena munthu angathe kuona maluŵa a mitundu yoyambira pa 10 kufika mpaka 20 pa kachigawo kongokwana sikweya mita imodzi. Kukongola kwa malowo kumachititsa kuti chithunzi chooneka bwino chimene katswiri wa zojambulajambula angajambule chioneke ngati n’chachabechabe. Ngakhale mawu owanena mochita kukomemeza kwadzaoneni amaoneka kuti sakwanira pofotokoza za kukongola kogometsa kwa dera la Namaqualand.

Komabe, akatswiri a zojambulajambula, olemba ndakatulo, ndi olemba mabuku salephera kunenapo kanthu pa za kukongola kochititsa chidwi kwa maluŵa ameneŵa. Wolemba ndakatulo wina wa ku South Africa, D. J. Opperman, mwa nthabwala anati: “Linali tsiku lalikulu lofesa mbewu pa dziko lapansili pamene. . . mbewu za maluŵa a mtengo wapatali zinatayikira thumba la mbewu za maluŵawo la Ambuye litabowoka.” Munthu wina amene anachita chidwi kwambiri ndi maloŵa analemba kuti: “Maluŵawo ankaoneka ngati utawaleza unali utadutsa pa malo a chipululu amenewo n’kusiyapo pakuoneka mitundu yosiyanasiyana.” Mlendo wina anati: “Kukongola kosatha kotereku kumachititsa munthu kuyamikira kuwoloŵa manja kwakukulu ndi nzeru zakuya za Mlengi wathu, Yehova.”

Ndiponso, kukongola kwa zodabwitsa za chaka ndi chaka za ku Namaqualand kukutitsimikizira kuti Mlengi angagwiritse ntchito zinthu zomera ngati zimenezi pobwezeretsa Paradaiso padziko lonse, kuti atumiki ake okhulupirika ndiponso oyamikira asangalale nazo kosatha. (Salmo 37:10, 11, 29) Ndiyeno, “chipululu chidzakondwa, ndipo maluŵa adzaphuka m’dziko losabala kanthu.”—Yesaya 35:1, Today’s English Version.

[Chithunzi pamasamba 16, 17]

Dera lonse, lomwe ndi lalikulu masikweya kilomita 50,000, limatulutsa maluŵa