Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuzindikira Matenda Atulo Aakulu

Kuzindikira Matenda Atulo Aakulu

Kuzindikira Matenda Atulo Aakulu

NTHAŴI zina zizindikiro zimene munthu angakhale nazo zingasonyeze kuti ali ndi matenda enaake aakulu okhudza tulo. Pali vuto lina lalikulu losoŵa tulo lomwe limatha kupitirira mwezi wathunthu lidakalipobe, nthaŵi zambiri limakhalapo chifukwa cha mavuto ena aakulu kuphatikizapo vuto losokonezeka maganizo. Nthaŵi zina vuto lalikulu losoŵa tuloli n’chizindikiro cha matenda ena aakulu.

Matenda Obanika Kutulo

Mario tulo tinkamuvuta kwambiri masana. Akamayendetsa galimoto yake, mkazi wake ankangokhalira kumuyang’anira, chifukwa nthaŵi ina iliyonse ankatha kugona, ndipo pambuyo pake sankatha kukumbukira n’komwe kuti anagona. Usiku uliwonse ankachita nkonono mosokosa komanso modukizadukiza ndipo nthaŵi zina ankatha kudzidzidzimutsa yekha n’kuyamba kupumira m’mwamba. *

Mario, anali ndi zizindikiro zoonekeratu za matenda obanika kutulo. Matenda obanika kutulo amam’banikitsa munthu kwa masekondi teni kapena mpaka kufika mphindi ziŵiri kapenanso zitatu. Nthaŵi zambiri munthuyo amangotembenukatembenuka chifukwa chobanika, kenaka amagonanso ndipo zimenezi zimamuchitikira nthaŵi zambirimbiri usiku wonsewo. Pali mitundu itatu ya matenda obanika kutulo.

Matenda obanika kutulo aubongo amayamba ngati mbali yaubongo yomwe imalamulira kapumidwe ikulephera kulamula kuti munthu azipuma bwinobwino. Matenda obanika kutulo akholingo amachitika chifukwa chakuti mbali ina yoloŵera mpweya kukhosiku imatsekeka, motero mpweya sutha kuloŵako. Matenda obanika kutulo ophatikiza amachitika ngati matenda aŵiri onseŵa aphatikizana ndipotu anthu ambiri amawapeza ndi matenda ophatikizaŵa. Wodwala mtundu uliwonse wa matenda obanika kutulo angafike pofanana ndi munthu amene sagona n’komwe tsiku lililonse usiku!

Anthu amene amadwala matenda obanika kutulo moyo wawo umakhala pachiswe, chifukwa amatha kugona ngakhale ali m’kati mogwira ntchito kapena moyendetsa galimoto. Angadwalenso matenda othamanga magazi, otupa mtima, ndiponso m’posavuta kuti adwale matenda a sitiloko kapena mtima wawo kusiya kugunda. Dr. William Dement wa ku yunivesite ya Stanford anati mwina anthu 38,000 a ku America amafa chaka chilichonse chifukwa cha matenda a mtima obwera chifukwa cha matenda obanika kutulo.

Ngakhale kuti matenda obanika kutulo amakonda amuna onenepa kwambiri opitirira zaka 40, matendaŵa amagwiranso anthu a zaka zina zilizonse, ngakhale ana aang’ono. Pali njira zingapo zothandiza pa matendaŵa, ndipo pa njira zonsezo pamafunika kuti pakhale dokotala wodziŵa bwino za matenda a tulo woti azikulangizani. Njira yothandiza kwambiri pa matendaŵa, yomwe n’njosalira opaleshoni ndi njira yogwiritsa ntchito makina omwe amathandiza kuti njira yoloŵera mpweya isamatsekeke. Usiku, wodwalayo amavala kumaso chipangizo chimene mumatulukira mpweya ndipo makinawo (amene dokotala amawachuna) amawatchera kuti azitulutsa mpweya wokwanira kuti wodwalayo asabanike akamagona. Zimenezi zikalephera kuthetsa vutolo, pali njira zingapo za opaleshoni, monga njira yogwiritsa ntchito moto wamagetsi kapena njira zina zamakono zomwe angagwiritse ntchito kuti apale bwinobwino pakhosipo.

Matenda Owodzera Masana

Matenda ena atulo ofunika kupita nawo kuchipatala ndiwo matenda owodzera masana. Matendaŵa n’ngamuubongo ndipo amachititsa munthu kuwodzera masana. Mwachitsanzo, Buck ankangokhalira kuwodzera. Ankatha kungogona mosadziŵika, ngakhale m’kati mwa misonkhano yofunika. Iye anayamba kunyamula makiyi m’manja mwake kuti akayamba kuwodzera, azidzidzimuka ndi phokoso la makiyiwo akagwa pansi. Kenaka anadwala matenda ofooketsa mawondo ake n’kumagwa nthaŵi iliyonse mtima wake ukakhala m’mwamba. Kenaka, akamagona ankachita ngati akudwala matenda ozizira ziwalo komanso nthaŵi zina ankaona zideruderu akangotsala pang’ono kugona.

Matenda owodzera masana nthaŵi zambiri amayamba munthu akakhala ndi zaka za pakati pa 10 ndi 30. Nthaŵi zina odwala matendaŵa amaoneka kuti akuchita zinthu bwinobwino koma amakhala asakuzindikira kuti patha nthaŵi yaitali bwanji akuchita zinthuzo. Vuto la nthenda imeneyi n’lakuti wodwalayo amatha kukhala nayo kwa zaka zambiri asanam’peze nayo ndipo anthu amamuona ngati waulesi, wopanda nzeru, kapena zochitika zake n’zachilendo. Pakalipano matendaŵa akuti sachiritsika, koma nthaŵi zina zimatheka ndithu kuchepetsa mphamvu yake polandira mankhwala komanso posintha zimene amachita pa moyo wake. *

Matenda Ena Atulo

Matenda ena aŵiri atulo, amene nthaŵi zina amabwerera pamodzi, amakhudza miyendo ndi manja, ndipo amachititsa kuti munthu adwale matenda aakulu osoŵa tulo. Oyamba pa matendaŵa ndi matenda ogwedezeka ziwalo, amene amachititsa kuti miyendo, ndiponso nthaŵi zina manja, zizigwedezeka munthu akamagona. Chitsanzo pankhani imeneyi ndi Michael. Iyeyu anam’peza ndi vuto loti miyendo yake inkagwedezeka usiku moti inkamudzutsa nthaŵi 350 usiku uliwonse!

Palinso matenda ena ochititsa munthu kumangofuna kusunthasuntha miyendo ndiponso kupinda mawondo ake, * motero amalephera kugona. Ngakhale kuti nthaŵi zina vuto limeneli akuti limabwera ngati munthu sachita zinthu zolimbitsa thupi ndiponso ngati magazi ake sayenda bwinobwino m’thupi, anthu ena akhalapo ndi vuto limeneli chifukwa chomwa zakumwa monga khofi. Zikuonekanso kuti nthaŵi zina moŵa umawonjezera vutoli.

Ndiye palinso vuto lokukuta mano munthu akamagona. Vutoli likamapitirira lingathe kuchititsa kuti mano apereseke ndiponso kuti nsagwada zizipweteka, motero munthuyo angamavutike kwambiri kupeza tulo. Pali njira zosiyanasiyana zothandizira anthu okhala ndi vutoli, malingana ndi kukula kwa vuto lawo. Nthaŵi zina amawachita opaleshoni m’kamwa kapena amatha kuwaveka chinthu chotchinjiriza mano awo usiku akamagona.

Matenda osoŵetsa anthu tulo ochepa chabe amene taonaŵa akusonyezeratu kuti kusachitapo kanthu pa matenda otero kungakhale ndi zotsatirapo zoopsa. Pena chithandizo chake chingakhale chosavuta koma pena chingakhale chovuta kwambiri, koma nthaŵi zambiri chimakhalabe chofunika ndithu. Ngati inuyo kapena munthu wina amene mumam’konda amavutika ndi matenda osoŵa tulo kapena ngati akuoneka kuti akudwala matenda enaake aakulu atulo, n’chinthu chanzeru kupita kuchipatala mosazengereza. Ngakhale atakalephera kuchiritsiratu matendawo, wodwalayo angapeze bwino ndithu motero nonsenu zingakupepukireniko. Ndipo m’tsogolo, malonjezo a m’Baibulo akadzakwaniritsidwa, “wokhalamo sadzanena Ine ndidwala.” Matenda onse adzachotsedweratu kwinaku Mulungu akusandutsa zinthu “zonse [kuti] zikhale zatsopano.”—Yesaya 33:24; Chivumbulutso 21:3-5.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Nkonono wodukizadukiza komanso wosokosa wa matenda obanika kutulo n’ngosiyana ndi nkonono umene anthu ambiri amachita mwa apo ndi apo, umene umangomvekera chapansipansi, womwe kuipa kwake n’koti ngati muli anthu ena m’chipindamo amalephera kugona.

^ ndime 11 Kuti mudziŵe zina zokhudza matenda owodzera masanaŵa, onani Galamukani! yachingerezi ya April 8, 1991, masamba 19 mpaka 21.

^ ndime 14 Onani Galamukani! yachingerezi ya November 22, 2000 kuti mudziŵe zina zokhudza vutoli.

[Chithunzi patsamba 28]

Chithandizo cha matenda atulo chiyenera kuperekedwa ndi dokotala

[Chithunzi patsamba 28]

Nkonono ungasonyeze kuti munthu ali ndi matenda obanika kutulo

[Chithunzi patsamba 29]

Nthaŵi zambiri munthu amadwala matenda owodzera masana anthu amamuona ngati waulesi

[Chithunzi patsamba 30]

Makina amene amapopera mpweya kuupititsa kukhosi angathandize pa matenda obanika kutulo