Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mmene Mungadziŵire Dzina la Mulungu

Mmene Mungadziŵire Dzina la Mulungu

Mmene Mungadziŵire Dzina la Mulungu

MZIMAYI wina wolemba nkhani m’nyuzipepala analandira kalata kuchokera kwa munthu wina amene amaŵerenga nyuzipepalayo, ndipo kalatayo inati: “Kwa moyo wanga wonse ndakhala ndikuvutika maganizo pofuna kudziŵa yankho la funso limene ndikukhulupirira kuti mundiyankha. Funso lake n’lakuti, Kodi dzina la Mulungu ndani? Ayuda amati dzina lake lenileni linaiwalika kalekale. Akristu amamutchula kuti ndi Yesu. Asilamu amati ndi Allah. . . . Ndiye dzina lake ndani kwenikweni?” Nyuzipepalayo inafalitsa funsolo pamodzi ndi yankho lakuti: “Malinga ndi ziphunzitso zakale za Ahebri, Mulungu ndi wamphamvuyonse, choncho sangakhale ndi dzina limodzi. Ndikukutsimikizirani kuti Iye akhoza kuvomera dzina lililonse limene mungamutchule mwaulemu.”

Mawu ongonena mosaganizira bwino pokamba za dzina la Mulungu ngati amenewo si achilendo kwenikweni masiku ano. Ngakhale kuti anthu amakonda zopembedza, ambiri amene amakhulupirira Baibulo saganizirapo kwambiri za nkhani yokhudza dzina la Mulungu. Koma kodi Mulungu amaiona bwanji nkhani imeneyi? Kodi amaiona kuti ndi nkhani yaing’ono?

Si Nkhani Yaing’ono

Tangoganizirani zakuti Baibulo limatchula dzina la Mulungu lakuti Yehova maulendo masauzande ndithu. M’Baibulo la New World Translation of the Holy Scriptures, dzinalo limapezeka maulendo 7,210! * Mulungu yemweyo ndiye anauzira olemba Baibulo kuti azilitchulatchula dzina lakelo. Mmodzi mwa olembawo ndi wamasalmo Asafu, yemwe analemba kuti: “Inu nokha, dzina lanu ndinu Yehova, ndinu Wam’mwambamwamba pa dziko lonse lapansi.” (Salmo 83:18) Nayenso Davide analemba pa salmo lina kuti: “Ife tidzatchula dzina la Yehova Mulungu wathu.”—Salmo 20:7.

Baibulo limasonyeza kuti Yehova Mulungu amaunika m’mitima mwathu kuti aone mmene timaonera dzina lake. Wamasalmo anati: “Tikadaiwala dzina la Mulungu wathu, . . . [Mulungu] sakadasanthula ichi kodi? Pakuti adziŵa zinsinsi za mtima.” (Salmo 44:20, 21) Mneneri Yesaya analemba kuti: “Muyamikire Yehova, bukitsani dzina lake, mulalikire machitidwe ake mwa mitundu ya anthu, munene kuti dzina lake lakwezedwa.”—Yesaya 12:4.

Mulungu mwini wakeyo ananena kuti: “Adzadziŵa kuti dzina langa ndine Yehova.” (Yeremiya 16:21) Panthaŵi inanso analengeza kuti: “Ndidzazindikiritsa dzina langa lalikulu kuti liri loyera, limene laipitsidwa mwa amitundu, . . . ndipo amitundu adzadziŵa kuti Ine ndine Yehova.” (Ezekieli 36:23) Ena mwa mawu ameneŵa akukamba za nthaŵi imene Yehova adzasonyeza mkwiyo wake kwa anthu amene salemekeza dzina lake. Kwa Mulungu, nkhani yokhudza dzina lake si yaing’ono.

Yehova Mulungu Sali Kutali Nanu

Kodi dzina la Mulungu mungalidziŵe bwanji? Kodi kudziŵa dzina la Mulungu kumatanthauza chiyani? Baibulo likuyankha kuti: “Iwo akudziŵa dzina lanu adzakhulupirira Inu.” (Salmo 9:10) Apa n’zoonekeratu kuti kudziŵa dzina la Mulungu kukukhudza zambiri osangoti za dzina lake basi. Muyenera kumukhulupirira iye. Zimenezo zikutanthauza kudziŵa kuti Mulungu ndi wotani ndiponso kuphunzira za makhalidwe ake ndi mmene amaganizira. Zimenezi zikulimbikitsani kuti mum’khulupirire iye.

Kuŵerenga ndi kuphunzira Baibulo mosamala kwambiri ndiko kungakuzindikiritseni kuti Yehova ndi Mulungu wotani kwenikweni. Iye amalonjeza zoteteza anthu amene amamukonda ndiponso okonda dzina lake. Ponena za munthu amene amachita zimenezo, Mulungu akuti: “Popeza andikondadi ndidzam’pulumutsa; ndidzam’kweza m’mwamba, popeza adziŵa dzina langa. Adzandifuulira ine ndipo ndidzam’yankha; kunsautso ndidzakhala naye pamodzi; ndidzam’landitsa, ndi kum’chitira ulemu. Ndidzam’khutitsa ndi masiku ambiri, ndi kumuonetsera chipulumutso changa.”—Salmo 91:14-16.

Inde, pali ubwenzi weniweni pakati pa Yehova Mulungu ndi anthu amene amamudziŵa dzina! Inunso mukhoza kukhala naye paubwenzi woterowo. Pamene mukupemphera kuchokera pansi pa mtima, osauma pakamwa kutchula dzina lake. Adzakuyankhani, chifukwa Baibulo limati iye “sakhala patali ndi yense wa ife.”—Machitidwe 17:27.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Baibulo la New World Translation of the Holy Scriptures, limene limafalitsidwa ndi Mboni za Yehova, ndi Baibulo limene linamasuliridwa mwamakono ndiponso mawu ake amagwirizana ndi mmene anthu amayankhulira panopo. Chinthu chofunika kwambiri m’Baibulo limeneli n’chakuti linabwezeretsa dzina la Mulungu pena paliponse pamene linayenera kukhalapo m’Malemba a Baibulo. Panopa, mabaibulo ameneŵa, athunthu kapena mbali yake yokha, oposa 122 miliyoni asindikizidwa m’zinenero zokwanira 45.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 11]

Mulungu Amakudziŵani Dzina

Mulungu anauza Mose kuti: “Ndikudziŵa dzina lako.” (Eksodo 33:12) Timatsimikizira kuti zimenezi zinalidi zoona kuchokera pankhani yodziŵika bwino ya chitsamba chimene chinali kuyaka moto. Baibulo limati Mulungu “ali m’kati mwa chitsamba anamuitana, nati, Mose, Mose.” (Eksodo 3:4) Chimenechi ndi chitsanzo chimodzi chabe mwa nthaŵi zambirimbiri zimene Mulungu anatchula anthu ake mayina awo. Zikuonekeratu kuti Mlengi wa chilengedwe chonse ameneyu amachita nafe chidwi aliyense payekha.

Baibulo limati mwa mabiliyoni ambirimbiri a nyenyezi zimene zilipo, Mulungu amadziŵa dzina la nyenyezi ina iliyonseyo. (Yesaya 40:26) Ngati zili choncho, kuli bwanji ndi anthu amene amamupembedza? Mtumwi Paulo analemba kuti “Ambuye [Yehova] azindikira iwo amene ali ake.” (2 Timoteo 2:19) Zimenezi zikusonyeza kuti si nkhani yongoloŵeza mayina awo basi. Mulungu amawadziŵa bwino kwambiri anthu amene amamulambira. Nafenso, tiyenera kumudziŵa Mulungu dzina lake ndi kuyamba kudziŵa kwambiri makhalidwe ake.

Buku lomalizira la m’Baibulo limafotokoza mophiphiritsira za buku limene Mulungu amalembamo mayina a anthu amene akhala akumulambira kuyambira kale kwambiri. Buku limeneli amalitchula kuti “buku la moyo” chifukwa chakuti Yehova Mulungu adzapereka moyo wosatha kwa anthu amene mayina awo analembedwa m’bukulo. (Chivumbulutso 17:8) Ichi ndi chiyembekezo chosangalatsa kwambiri kwa anthu amene amamudziŵa Mulungu dzina lake.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 12]

Analalikira Dzina la Mulungu

● Nyimbo ya Mose Aisrayeli atangotsala pang’ono kuti aloŵe m’Dziko Lolonjezedwa: “Ndidzalalika dzina la Yehova.”Deuteronomo 32:3.

● Mawu amene Davide anauza Goliati: “Ine ndafika kwa iwe m’dzina la Yehova wa makamu.”1 Samueli 17:45.

● Mawu a Yobu katundu wake yense atawonongekeratu ndiponso ana ake onse atamwalira mwadzidzidzi: “Lidalitsike dzina la Yehova.”Yobu 1:21.

● Mtumwi Petro akuyankhula zomwe zinalembedwa m’Malemba Achihebri: “Yense amene akaitana pa dzina la Ambuye [Yehova] adzapulumutsidwa.”Machitidwe 2:21.

● Mneneri Yesaya: “Muyamikire Yehova, bukitsani dzina lake, . . . munene kuti dzina lake lakwezedwa.”Yesaya 12:4.

● Yesu Kristu akuphunzitsa ophunzira ake kupemphera: “Chifukwa chake pempherani inu chomwechi: Atate wathu wa Kumwamba, Dzina lanu liyeretsedwe.”Mateyu 6:9, 10.

● Yesu Kristu akupemphera kwa Mulungu: “Ndalionetsera dzina lanu.”Yohane 17:6.

● Mulungu akuyankhula ndi anthu ake: “Ine ndine Yehova; dzina langa ndi lomweli; ndipo ulemerero wanga Ine sindidzapereka kwa wina.”Yesaya 42:8.