Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Kumwa Mowa Mwauchidakwa N’koipadi?

Kodi Kumwa Mowa Mwauchidakwa N’koipadi?

Lingaliro la Baibulo

Kodi Kumwa Mowa Mwauchidakwa N’koipadi?

KWA zaka zambiri, m’zisudzo ndiponso m’mafilimu akhala akuyerekezera chidakwa chochita zinthu zoseketsa anthu. Ngakhale kuti asangalatsi amachita zimenezi mongoseŵera chabe, nthabwala zawozo zimasonyeza kuti anthu ambiri sasangalala nalo khalidwe lauchidakwa, ndipo amaona kuti ndi khalidwe lopeputsa munthu komabe losavulaza m’njira iliyonse.

Komatu uchidakwa weniweni si nkhani yongoitengera mwanthabwala ayi. Bungwe loona zaumoyo padziko lonse la World Health Organization linaika uchidakwa m’gulu la zinthu zowononga thanzi kwambiri padziko lonse. Akuti kupatulako fodya, uchidakwa ukupha ndi kudwalitsa anthu ambiri kuposa chinthu chilichonse chovuta kusiya, ndipo umachititsa kuti dziko la United States lokha liwononge ndalama zokwana mabiliyoni 184 pachaka.

Ngakhale kuti pali zoopsa zotere, anthu ambiri uchidakwa sauona ngati chinthu choopsa. Inde, amavomereza kuti pakapita nthaŵi yaitali munthu amatha kuvulala nawo, koma saona kuti pali vuto kuledzera kwambiri mwa apo ndi apo. Kwa achinyamata a m’madera ena a padziko lonse, kumwa mowa mwauchidakwa amakuona ngati chizindikiro cha kukula. Ndipo ngakhale kuti mabungwe a zaumoyo akhala akuchenjezapo mwamphamvu, khalidwe longogugudiza mowa mwina wokwana mabotolo asanu kapena kuposa, likukula kwambiri pakati pa anthu a misinkhu yonse. Motero m’pomveka kuti anthu ambiri amakayikira ngati kumwa mowa kwambiri kuli koipadi. Kodi Baibulo limanenapo chiyani pankhaniyi?

Vinyo Komanso Mitundu Ina ya Mowa Ndi Mphatso Zochokera kwa Mulungu

M’Baibulo muli malo ambiri omwe mumatchulidwa za vinyo ndi mitundu ina ya mowa. Mfumu Solomo analemba kuti: “Tiye, idya zakudya zako mokondwa, numwe vinyo wako mosekera mtima; pakuti Mulungu wavomerezeratu zochita zako.” (Mlaliki 9:7) Wamasalmo anavomereza kuti Yehova Mulungu ndiye amapereka “vinyo wokondweretsa mtima wa munthu.” (Salmo 104:14, 15) N’zachiwonekere kuti vinyo ndi imodzi mwa mphatso zimene Yehova anapatsa anthu.

N’zachidziŵikire kuti Yesu sankaletsa anthu kumwa vinyo. Pajatu chozizwitsa chake choyamba chinali kusandutsa madzi kukhala vinyo wabwino kwambiri pa phwando la ukwati. (Yohane 2:3-10) Anagwiritsiranso ntchito vinyo m’njira yoyenerera kwambiri kuphiphiritsira mwazi wake pamene ankakhazikitsa Mgonero wa Ambuye. (Mateyu 26:27-29) Baibulo limanenaponso zakuti vinyo amachiritsa matenda ena, chifukwa mtumwi Paulo analimbikitsa Timoteo pomuuza kuti: “Uchite naye vinyo pang’ono, chifukwa cha mimba yako.”—1 Timoteo 5:23; Luka 10:34.

Nkhani Yagona pa Kumwa Mosapambanitsa

Onani kuti Paulo anati ndi bwino kumwa “vinyo pang’ono.” N’zochita kuonekeratu apa kuti Baibulo limaletsa kumwa mowa mopanda malire. Ansembe achiyuda ankaloledwa kumwa mosapambanitsa akakhala kuti sakutumikira kukachisi. Komabe ankawaletsa kumwa chakumwa chilichonse choledzeretsa panthaŵi imene akuchita ntchito zawo zaunsembe. (Levitiko 10:8-11) Patatha zaka zambiri, Akristu a m’zaka 100 zoyambirira anachenjezedwa kuti oledzera “sadzaloŵa Ufumu wa Mulungu.”—1 Akorinto 6:9, 10.

Kuphatikizanso apo, pomulangiza Timoteo, Paulo anati anthu onse otsogolera mumpingo sayenera kukhala ‘oledzera’ kapena ‘omwetsa vinyo.’ * (1 Timoteo 3:3, 8) Kwenikweni Baibulo limalamula kuti oledzera amene sakulapa ayenera kuchotsedwa mumpingo wachikristu. (1 Akorinto 5:11-13) Malemba amanena mosapita m’mbali kuti ‘vinyo achititsa chiphwete.’ (Miyambo 20:1) Kumwa mowa mwauchidakwa kungachititse munthu kutayirira komanso kuchita zinthu mosaganiza bwino.

Chifukwa Chimene Mawu a Mulungu Amaletsera Kumwa Mowa Kwambiri

Yehova, ‘amene amatiphunzitsa kupindula,’ amadziŵa kuti chinthu chilichonse, kuchichita mopanda malire, chingathe kutipweteka ngakhalenso kupweteketsa anthu ena. (Yesaya 48:17, 18) Kumwa zakumwa zoledzeretsa kuli m’gulu la zinthu zotere. Mawu a Mulungu amafunsa kuti: “Ndani ali ndi chisoni? Ndani asauka? Ndani ali ndi makangano? Ndani ang’ung’udza? Ndani alasidwa chabe? Ndani afiira maso?” Mawu a Mulungu omwewo amayankha kuti: “Ndi amene achedwa pali vinyo, napita kukafunafuna vinyo wosanganizidwa.”—Miyambo 23:29, 30.

Chifukwa chomwa kwambiri mowa, anthu ena achita zinthu ngati oduka mutu ndiponso zoopsa: mwina kuyendetsa galimoto mowa uli m’mutu n’kuyika pangozi moyo wawo ndiponso wa ena, mwina kuchita zinthu zozoloŵerana mopitirira muyeso ndi mkazi wa mwini mapeto ake n’kuyambana kwambiri ndi anzawo, mwina kuyankhula kapena kuchita zinthu zopusa kapena zochititsa anthu kuuma thupi. (Miyambo 23:33) Anthu ena amati kumwa mowa mwauchidakwa ndi chimodzi mwa zinthu zosokoneza kwambiri moyo wa anthu ndipo izi n’zoona. Mpake kuti Mulungu amatilimbikitsa kuti: “Usakhale mwa akumwaimwa vinyo”!—Miyambo 23:20.

Pa Agalatiya 5:19-21, Paulo anaika kuledzera m’gulu la “ntchito za thupi” zosemphana ndi zipatso za mzimu wa Mulungu. Kumwa mowa mwauchidakwa kungasokoneze ubwenzi wa munthu ndi Mulungu. Motero n’zachidziŵikire kuti Akristu ayenera kupeŵa kumwa mowa mopambanitsa.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 11 Popeza kuti abale oyang’anira ayenera kupereka chitsanzo chabwino kwa nkhosa pa kaganizidwe ndi kakhalidwe kawo potsanzira kwambiri khalidwe lapamwamba la Yehova, Akristu ena ayeneranso kuchita chimodzimodzi.