Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Nkhondo ya Nyukiliya Anthu Akuiopabe?

Kodi Nkhondo ya Nyukiliya Anthu Akuiopabe?

Kodi Nkhondo ya Nyukiliya Anthu Akuiopabe?

Yolembedwa ndi wolemba Galamukani! ku Japan

“Munthu aliyense woganiza bwino amaopa nkhondo ya zida za nyukiliya, ndipo dziko lililonse lotsogola limakonzekera nkhondo imeneyi. Ngakhale kuti aliyense amadziŵa kuti kuchita nkhondo yotereyi n’kupenga kwenikweni, dziko lililonse lili ndi kachifukwa kake kodzikhululukira,” anatero katswiri wa sayansi ya zakuthambo, Carl Sagan.

PA AUGUST 6, 1945, ndege yankhondo ya ku America inaponya bomba la nyukiliya pamzinda wa Hiroshima, ku Japan ndipo anthu ambirimbiri anafa komanso katundu wochuluka anawonongekeratu m’nthaŵi yochepa chabe. Ili linali bomba loyamba la nyukiliya kuphulitsidwa pankhondo. Bombalo linaseseratu dera lalikulu masikweya kilomita 13 mumzindawo, lomwe linali ndi anthu okwana 343,000. Zinthu zambiri mumzinda wonsewo zinaphwasukiratu, ndipo anthu osachepera 70,000 anafa ndipo enanso 69,000 anavulala. Patangotha masiku atatu anaponyanso bomba lina la nyukiliya, komano ili analiponya mumzinda wa Nagasaki; ndipo linapha anthu 39,000 n’kuvulaza anthu 25,000. Pafupifupi theka la zinthu mumzindawu zinaphwasukiratu kapena zinangowonongeka. Zida zoopsa choncho zinali zisanagwiritsidweko ntchito n’kale lonse, m’mbiri yonse ya anthu. Apatu dziko linasintha. Linasintha chifukwa linaloŵa m’nyengo ya zida za nyukiliya. Pasanathe zaka zambiri, mayiko a United States, dziko lomwe kale linali Soviet Union, Great Britain, France, ndi China anali atakonza mabomba a nyukiliya oopsa kuposa oyamba aja.

Chidani chapakati pa mayiko a ndale zachikomyunizimu ndi mayiko odana ndi ndale zotere chinachititsa kuti apange zida za nyukiliya zoopsa kwambiri ndiponso njira zotsogola zoponyera zidazo. Padziko lonse anthu anachita mantha pamene kunapangidwa mabomba otha kufika kutsidya la nyanja zamchere, omwe m’timphindi tochepa chabe, angathe kukafika kumayiko otalikirana ndi mtunda wopitirira mwina makilomita 5,600. Sitima zoyenda pansi pamadzi anazikonza kuti zizitha kunyamula zida za nyukiliya zokwanira kuphulitsa malo 192 osiyanasiyana. Panthaŵi inayake akuti kunali zida za nyukiliya zokwana mpaka 50,000! Panthaŵi ya chidani chapakati pa mayiko a ndale zachikomyunizimu ndi mayiko odana ndi ndalezi, anthu anangotsala pang’ono kuwonongeratu dziko lonse ndi nkhondo imene anthu ena ankanena kuti idzakhala Armagedo ya nyukiliya, nkhondo yopanda wopambana.

Chidanicho Chitatha

Buku la Encyclopædia Britannica linalongosola kuti cha m’ma 1970, chidani chapakati pa mayiko a ndale zachikomyunizimu ndi mayiko odana ndi ndale zotere chinachepa “malingana ndi mfundo zimene anagwirizana pa Makambirano Ochepetsako Zida Zoopsa omwe anachitika kaŵiri. Panthaŵiyi mayiko a America ndi Soviet Union anapatsana malire a kuchuluka kwa mabomba a nyukiliya ndi mabomba ena okhala ndi mphamvu ya nyukiliya amene akanayenera kusunga. Kenaka kumapeto kwa m’ma 1980 chidanichi chinachepa n’kutheratu.

Lipoti la bungwe la Carnegie Endowment for International Peace linati: “Kutha kwa chidanichi kunachititsa anthu kuyamba kuganiza kuti mpikisano wa mayiko okhala ndi zida za nyukiliya ndiponso chidani cha pakati pa dziko la United States ndi dziko la Russia zikupita kokutha.” Zida zambirimbiri za nyukiliya zaphwasulidwa m’zaka zaposachedwapa chifukwa cha ntchito yochepetsa zida za nyukiliya. M’chaka cha 1991 mayiko a Soviet Union ndi United States anasayinirana Pangano Lochepetsa ndi Kuletsa Zida Zoopsa, lomwe linali pangano loyamba m’mbiri yonse lochititsa kuti mayiko aŵiriŵa achepetse zida zawo zoopsa zomwe akuzisunga komanso zomwe anazitchera, kuti dziko lililonse likhale ndi zida 6,000 zokha. Kumapeto kwa chaka cha 2001, mayiko aŵiriŵa analengeza kuti atsatira mfundo zonse za m’panganolo pochepetsa zida zawo zoopsa. Kenaka m’chaka cha 2002 anavomerezanso Pangano la ku Moscow, pomwe mayikoŵa anagwirizana kuti pakutha kwa zaka khumi zikubwerazi akhale atachepetsako zida zawozo kuti zikhalepo 1,700 apo ayi zisapititirire 2,200.

Ngakhale zili choncho, Mlembi Wamkulu wa bungwe la United Nations, Kofi Annan anati: “Ino si nthaŵi yoiwalako zakuti nkhondo ya zida za nyukiliya ingathe kuchitika.” Iyeyu anawonjezera kuti: “Kumayambiriro kwa zaka za m’ma 2000 zino nkhondo yoopsa ya zida za nyukiliya ikhoza kuchitika ndithu.” N’zoopsa kuganizira kuti ngakhale panopa, nkhondo yoopsa ya nyukiliya yoposa yomwe inachitika pamene anaponya mabomba a nyukiliya ku Hiroshima ndi ku Nagasaki ikhoza kuchitika. Kodi ndani amene akuoneka kuti angachititse nkhondo yoopsa motere? Komanso funso lofunika kwambiri n’lakuti, kodi ingathe kupeŵedwa?