Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Nkhondo ya Nyukiliya Anthu Angaipeŵe?

Kodi Nkhondo ya Nyukiliya Anthu Angaipeŵe?

Kodi Nkhondo ya Nyukiliya Anthu Angaipeŵe?

“Adzadya nadzagona pansi, [ndipo sipadzakhala] wakuwaopsa.”—Zefaniya 3:13.

ALIYENSE amalakalaka atamakhala padziko pano mosaopa nkhondo ya nyukiliya. Komabe poona mmene zinthu zilili m’dzikoli, anthu ambiri akuda nkhaŵa. Nyuzipepala ya The Guardian Weekly inati: “Dziko la United States ndiponso mayiko ena sakuganiziranso kwenikweni zoletsa ndi kuchepetsa kapenanso kuthetseratu zida za nyukiliya padziko lonse.”

Komabe, ena amanena kuti mayiko achitapo kanthu ndithu pa nkhaniyi. Mwachitsanzo, akuti dziko la United States lokha linagwiritsira ntchito ndalama zokwana madola 2.2 biliyoni chaka chimodzi chokha pofuna kupeŵa nkhondo ya nyukiliya. Ndithu, izi si ndalama zochepa ayi. Komano anthu ambiri zimawapweteka mtima kudziŵa kuti chaka chilichonse, dziko lomweli limawononganso ndalama zokwana madola 27 biliyoni pokonzekera kumenya nkhondo ya nyukiliya.

Nanga bwanji za mapangano a mtendere? Kodi mapangano otere angathe kutilimbitsa mtima?

Mapangano Ochepetsa Zida za Nyukiliya

Kuchokera pamene mabomba a nyukiliya anayamba kupangidwa, mayiko alembapo mapangano angapo oyesa kuchepetsa zida za nyukiliya. Ena mwa mapanganoŵa ndi monga Pangano Loletsa Kuti Zida za Nyukiliya Zisafale, Pangano Lochepetsako Zida Zoopsa, ndi Pangano Loletsa Kuyesa Mitundu Yambiri ya Zida za Nyukiliya. Kodi mapanganoŵa sanathandize kuti nkhondo ya nyukiliya isachitike?

Pangano lililonse limadalira kuti opanganawo asunge lonjezo lawo. Mwachitsanzo, Pangano Loletsa Kuti Zida za Nyukiliya Zisafale, lomwe analikhazikitsa mu 1970 ndipo linali litavomerezedwa ndi mayiko 187 pofika m’mwezi wa December 2000, limadalira kukhulupirika kwa mayiko okhala ndi zida za nyukiliya ndi omwe alibe amene anasayina panganoli. Ngakhale kuti panganoli limaletsa mayiko opanda zida za nyukiliya kupanga kapena kupeza zidazi, limafunanso kuti mayiko okhala ndi zida zotere ayesetse kuwononga zida zawozo. Kodi zimenezi zathandizadi? Carey Sublette analemba m’chikalata chotchedwa “Mafunso Ofunsidwafunsidwa pa Nkhani ya Zida za Nyukiliya” kuti: “Ngakhale kuti panganoli si loti mayiko angalephere kuliphwanya mwachibisila, lathandiza ndithu kuti mayiko asayambe kupanga zida za nyukiliya pogwiritsira ntchito mafakitale wamba amene amawayendera nthaŵi ndi nthaŵi mogwirizana ndi panganoli.”

Ngakhale kuti panganoli lathandizako ndithu, Sublette anati, “lalephera . . . kusintha mayiko angapo kuti asiye zofuna kupeza zida zotere, moti mpaka ena azipeza ndithu.” Komabe iye anati mayikoŵa akukonza zida zimenezi mochita kubisa komanso akuzikonzera ku malo amene sawayendera mogwirizana ndi panganolo. Kuti pangano lililonse ligwire ntchito, pamafunika kuti opanganawo azikhulupirika. Kodi tiyenera kungokhulupirira zilizonse zimene anthu amalonjeza? Yankho la funsoli n’lachidziŵikire tikayang’ana zimene anthu achita m’mbuyomu.

Motero kodi n’kuti kumene tingapeze thandizo?

Kuganizira Njira Ina

M’mwezi wa December 2001, anthu okwana 110 amene analandirapo mphoto yapamwamba ya Nobel anavomereza ndiponso anasayinira mfundo yakuti: “Chinthu chimodzi chokha chothandiza kuti tsogolo la dziko lino likhale labwino n’chakuti mayiko onse achite zinthu mogwirizana, potsatira mfundo za demokalase. . . . Kuti tikhale bwinobwino m’dziko limene talisinthali, tiyenera kuyamba kuganizira njira ina.” Komano kodi ndi kuganizira mwa ‘njira inanso’ kuti kumene kukufunikira? Kodi n’kwanzeru kukhulupirira kuti anthu amene akuchititsa kuti zamtendere zizikayikitsa padziko pano chifukwa cha zida zawo za nyukiliya angayambe kuganizira njira ina?

Baibulo limatilangiza kuti: “Musamakhulupirira zinduna, kapena mwana wa munthu, amene mulibe chipulumutso mwa iye.” (Salmo 146:3) N’chifukwa chiyani sitiyenera kutero? Baibulolo limayankha kuti: “Njira ya munthu sili mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.” (Yeremiya 10:23) Inde, chifukwa chachikulu n’chakuti anthu sanalengedwe mwakuti angathe kulamulira dziko mwamtendere. Baibulo limanena kuti, “wina apweteka mnzake pom’lamulira.”—Mlaliki 8:9.

Ngati anthu sangathe kulamulira dziko, kodi ndani angathe kutero? Baibulo limalonjeza kuti padzakhala mtendere boma lodalirika ndiponso lodziŵadi kulamulira likadzayamba kulamulira. Ulamuliro umenewu m’Baibulo umatchulidwa kuti Ufumu wa Mulungu, ndipo mosadziŵa, anthu ambiri akhala akupempha kuti ufumuwu udze akamanena Pemphero la Ambuye n’kumati: “Atate wathu wa Kumwamba, . . . Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga kumwamba chomwecho pansi pano.” (Mateyu 6:9, 10) Ufumu umenewu Mfumu yake ndi Yesu Kristu, Kalonga Wamtendere. Polongosola ulamuliro wa kalongayu Baibulo limati: “Za kuyenjezera ulamuliro wake, ndi za mtendere sizidzatha.”—Yesaya 9:6, 7.

Ngakhale “zinduna,” kapena kuti andale, ndiponso maboma a anthu atapanda kuphunzira za ufumu umenewu, inuyo mungathe kutero. Mboni za Yehova zathandiza anthu ambiri zedi kuphunzira uthenga wolimbitsa mtima wa m’Baibulo powaphunzitsa Baibulo kwaulere. Ngati mukufuna kudziŵa zambiri, chonde lemberani kalata kwa ofalitsa magazini ino, kapena mungathe kupita ku Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova ya m’dera limene mukukhala.

[Chithunzi pamasamba 8, 9]

Mu ulamuliro wa boma la Mulungu lolamulidwa ndi mfumu, padziko pano anthu sadzaopanso nkhondo ya nyukiliya