Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Muli Nkhani Zothandiza Kwambiri’

‘Muli Nkhani Zothandiza Kwambiri’

‘Muli Nkhani Zothandiza Kwambiri’

Izi ndi zimene mkulu woyang’anira malo osamalira anthu odwala kwambiri ku Illinois, m’dziko la United States, ananena ataŵerenga kabuku kakuti Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira. Wa Mboni za Yehova wina ndi amene anamutumizira buloshalo pamodzi ndi Galamukani! chifukwa chakuti wa Mboniyo anaŵerengapo mu Galamukani! kuti anthu achikulire ndiwo amakonda kwambiri kudzipha. Mkulu woyang’anira malowo atalandira bulosha ndi magaziniyo, analemba kalata mofulumira.

Ataona kuti m’bulosha lakuti Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira muli nkhani zothandiza kwambiri, m’kuluyo analemba kuti: “Ndingakonde kugaŵira buloshali . . . kwa mabanja amene angalimbikitsidwe chifukwa cha nzeru zake zothandizadi pamodzi ndi malemba komanso nkhani zake za m’Baibulo.”

Wa Mboniyo anamuimbira telefoni mkuluyo nthaŵi yomweyo n’kugwirizana zoti akakumane naye. Mkuluyo anaitanitsa mabulosha 20 ndipo anapemphanso kuti wa Mboniyo azipitako pa miyezi iŵiri kapena itatu iliyonse kuti azikasiya mabulosha ndi magazini ena.

Mwina inuyo kapena enaake amene mukuwadziŵa angalimbikitsidwe ataŵerenga bulosha lamasamba 32 limeneli. Mungaitanitse bulosha lanu polemba zofunika m’kabokosi kali pamunsika ndi kutumiza ku adiresi imene ili pomwepoyo kapena ku adiresi yoyenera imene ili patsamba 5 la magazini ino.

□ Ndikupempha kuti munditumizire bulosha lakuti Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira.

□ Chonde nditumizireni munthu kuti ayambe kuchita nane phunziro la Baibulo lapanyumba laulere.