Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zinyama Zidzasangalatsa Anthu Mpaka Kalekale

Zinyama Zidzasangalatsa Anthu Mpaka Kalekale

Zinyama Zidzasangalatsa Anthu Mpaka Kalekale

PALIDI mitundu yambiri ya zinyama, ndipo zonse zimaoneka kuti zili ndi chikhalidwe chawochawo. Kukonda zinyama ndi kuzichitira chifundo kungachititse munthu kuyandikira kwa Mlengi. Zimenezi n’zimene zinachitikira Maria.

Pafupifupi zaka zitatu zapitazo, pamene Maria ankakhala ku Lisbon, Portugal, galu wake wokondedwa anasoŵa, ndipo analengeza zimenezi pa wailesi. Wa Mboni za Yehova wina, amene anali wotsimikiza kuti anaona galu wofanana ndi amene anamufotokoza pa wailesiyo, anamudziŵitsa Maria. Pamene aŵiriwo anakumana, anam’peza galuyo, ndipo Mboniyo inanena kuti popeza Maria anali munthu wokonda zinyama chotero, ndiye kuti angasangalaledi kukhala m’dziko latsopano limene Mulungu walonjeza. Mboniyo inafotokoza kuti pa nthaŵi imeneyo, anthu adzakhala pamtendere ndi zinyama zonse.

Maria anavomera pempho loti apite ku msonkhano wa Mboni. Zimene anamva ndi kuona kumeneko zinadzutsa chidwi chake moti mpaka anafuna kuphunzitsidwa Baibulo payekha. Pamene phunzirolo limapita patsogolo, Maria anakhudzidwa mtima kwambiri ndi zimene anaphunzira zokhudza Yehova Mulungu ndi lonjezo lake la moyo wosatha padziko lapansi latsopano lachilungamo. (Salmo 37:29; Yohane 17:3) Pamapeto pake, pa February 16, 2002, anasonyeza poyera kudzipatulira kwake kwa Yehova mwa kubatizidwa m’madzi.

Cholinga cha Mulungu Pachiyambi

Mofanana ndi Maria, anthu ambiri akhudzidwa mtima ndi umboni wa m’Baibulo wakuti cholinga cha Mulungu pachiyambi chakuti anthu adzakhale kosatha m’paradaiso padziko lapansi ndi kusamalira zinyama zake zonse, chidzakwaniritsidwa. (Genesis 1:28) Baibulo limati Mulungu “sanalilenga [dziko lapansi] mwachabe” koma “analiumba akhalemo anthu.” Malinga ndi zimenezi, anthu anali oti adzasangalale ndi moyo pa dziko lapansi limodzi ndi zinyama zake mpaka kalekale.—Yesaya 45:18.

Baibulo limatsindikanso kuti Mulungu akufuna kukwaniritsa cholinga chake chimene anali nacho pachiyambi choti dziko lapansi likhale paradaiso. Iye anati: “Ndanena,” ndipo anawonjezera kuti: “Ndidzachichitanso.” Yehova ananenanso kuti: “Momwemo adzakhala mawu anga amene atuluka m’kamwa mwanga, sadzabwerera kwa Ine chabe, koma adzachita chimene ndifuna, ndipo adzakula mmene ndinawatumizira.”—Yesaya 46:11; 55:11.

N’zachiwonekere kuti cholinga cha Mulungu pachiyambi chinali choti anthu asangalale ndi moyo m’paradaiso padziko lapansi kosatha. Tikhoza kukhulupirira ndi mtima wonse kuti cholinga chimenecho chidzakwaniritsidwa. Tiyeni tione zimene Baibulo limatisonyeza za mmene moyo udzakhalire m’dziko latsopano la Mulungu. Tiona kuti, n’zoonadi kuti zinyama zonse, zoweta ndi zakuthengo zomwe, zidzakhala pamtendere ndi zinzake komanso ndi anthu.—Yesaya 65:17, 21-25; 2 Petro 3:13.

Ziweto M’dziko Latsopano la Mulungu

M’dziko latsopano la Yehova, anthu adzatha kugwira ubweya wa mkango, kusisita ubweya wa nyalugwe, ndi kugona m’nkhalango popanda kuopa kuti nyama iliyonse iwapweteka. Taonani lonjezo lotsatirali la Mulungu: “Ndidzapangana nazo pangano la mtendere, ndi kuleketsa zilombo zoipa m’dzikomo; ndipo [anthu a]dzakhala mosatekeseka m’chipululu, ndi kugona kunkhalango.”—Ezekieli 34:25; Hoseya 2:18.

Indedi, pa nthaŵi imeneyo zinyama zakuthengo zidzakhala zomvera, ngakhale kwa ana ang’onoang’ono. Baibulo limati: “Mmbulu udzakhala pamodzi ndi mwana wa nkhosa, ndipo nyalungwe adzagona pansi ndi mwana wa mbuzi; ndipo mwana wa ng’ombe ndi mwana wa mkango ndi choweta chonenepa pamodzi; ndipo mwana wamng’ono adzazitsogolera.”

Koma si zokhazo ayi! Lembalo likupitiriza kuti: “Ng’ombe yaikazi ndi chilombo zidzadya pamodzi; ndipo ana awo ang’ono adzagona pansi; ndipo mkango udzadya udzu ngati ng’ombe. Ndipo mwana wakuyamwa adzaseŵera pa una wa mamba, ndi mwana woleka kuyamwa adzaika dzanja lake m’funkha la mphiri. Sizidzaipitsa, sizidzasakaza m’phiri langa lonse loyera, chifukwa kuti dziko lapansi lidzadzala ndi odziŵa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.”—Yesaya 11:6-9.

M’dziko latsopano la Yehova, simudzakhala vuto la kuthithikana kwa anthu m’mizinda ikuluikulu imene imakhala yovuta kuti iwo ndi ziweto zawo akhalemo. Zoona, ngakhale masiku ano anthu ambiri amasangalala ndi zinyama zawo, ndipo ambiri amaziona moyenera ndi kuzisamalira bwino. Koma tangoganizani za lonjezo losangalatsa kwambiri loti anthu adzasangalala ndi ziweto mpaka kalekale m’dziko latsopano lachilungamo! Kuzisamalira mwachikondi kumene anthu azidzachita, kudzapangitsa kuti Mlengi Wamkulu wa zamoyo zonse alemekezedwe.

Ngati simunaphunzire za zolinga za Mulungu zochititsa chidwi, monga mmene Maria yemwe amakonda zinyama analili asanaphunzire mpaka chaposachedwapa, tikukupemphani kuti mudziŵitse ofalitsa magazini ino kapena wina wa Mboni za Yehova, ndipo adzakhala wokondwa kukuthandizani kuphunzira zolinga za Mulungu.

[Chithunzi patsamba 18]

M’dziko latsopano la Mulungu, anthu adzasangalala ndi zinyama mpaka kalekale