Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ziweto Tifunika Kuziona Moyenera

Ziweto Tifunika Kuziona Moyenera

Ziweto Tifunika Kuziona Moyenera

MONGA tafotokozera m’nkhani yapitayi, anthu anapatsidwa udindo wosamalira dziko lapansi ndi zinyama zonse zimene zili m’dzikoli. Baibulo limati: “[Mulungu] mudagonjetsa zonse pansi pa mapazi ake; nkhosa ndi ng’ombe, zonsezo, ndi nyama za kuthengo zomwe; mbalame za m’mlengalenga, ndi nsomba za m’nyanja.”—Salmo 8:6-8; 115:16.

Mmene anthu amakwaniritsira udindo wawo wosamalira zinyama ndi nkhani yofunika kwambiri. Mawu a Mulungu amati: “Wolungama asamalira moyo wa choweta chake.” (Miyambo 12:10) Ndipotu, malamulo a Mulungu kwa Aisrayeli nthaŵi zambiri anatsindika kufunika kochitira chifundo zinyama. (Deuteronomo 22:4, 10; 25:4) Pofuna kukwaniritsa udindo umenewu, anthu nthaŵi zambiri aweta ziweto zapakhomo, ndipo awetanso ngakhale zinyama zakuthengo.—Genesis 1:24.

Komabe, m’pofunika kukumbukira kuti Baibulo limatsindika kusiyana kwa anthu ndi zinyama. Anthu ndi amene anapangidwa ‘m’chifanizo ndi chikhalidwe cha Mulungu,’ osati zinyama. (Genesis 1:26) Ndipo zinyama anazilenga kuti zikhale ndi moyo wokhala ndi polekezera, pamene anthu anawalenga ndi mwayi wotha kukhala ndi moyo kosatha padziko lapansi. (Genesis 3:22, 23; Salmo 37:29) Yesu Kristu anati, kuti tikhale ndi “moyo wosatha,” tiyenera kusonyeza chikhulupiriro ndi kuphunzira za Mulungu, zinthu zimene zinyama sizingathe kuchita. (Yohane 3:36; 17:3) Kuwonjezera apo, Baibulo limayerekezera anthu osayenerera kuukitsidwa ndi “zamoyo zopanda nzeru, nyama zobadwa kuti zikodwe ndi kuwonongedwa.”—2 Petro 2:9-12.

Anazilenga Kuti Zithandize Anthu

Mulungu analenga zinyama kuti zithandize anthu. Zinyama zingathandize anthu kugwira ntchito yawo komanso zingakhale mabwenzi awo. Zimathandizanso kusonyeza chikondi ndi nzeru za Mulungu. Inde, zimasangalatsa kwambiri kuona kukongola kwa zinyama ndi kudziŵa zambiri za Mlengi mwa kuphunzira za nzeru zawo zachibadwa zochititsa chidwi. (Salmo 104:24; Miyambo 30:24-28; Aroma 1:20) Chitsanzo chimodzi mwa zitsanzo zambiri za nzeru zoterozo timachiona mwa tizilombo. Njira imene njuchi zimalankhulirana ndi kutsatira malangizo oti zikapeze zakudya ndi yochititsa chidwi kwambiri. N’zochititsanso chidwi kwambiri kuona mmene zimamangira zisa zawo mwaluso.

Zinyama zingathandize anthu powapatsa chakudya. Poyambirira, Mulungu anapatsa anthu zomera zokha, monga therere laliwisi, kuti azidya. Koma patapita zaka zoposa 1600, chigumula cha m’tsiku la Nowa chitachitika, Mulungu anati: “Zoyenda zonse zamoyo zidzakhala zakudya zanu; monga therere laliwisi ndakupatsani inu zonsezo.” (Genesis 1:29; 9:3) Choncho, Mulungu analola kuti anthu azidya zinyama. Mwachiwonekere, zimenezi zinali zothandiza kwa anthu, ngakhale kuti poyambirira Mulungu sanaphatikizepo nyama pa zakudya za anthu.

Kusunga Ziweto Kuli ndi Mavuto Ake Masiku Ano

Zikuoneka kuti m’mbiri yonse ya anthu, ziweto nthaŵi zambiri sankazisunga m’nyumba, ndipo zimenezi zikuchitikabe m’madera ambiri pa dziko lapansi. Koma posachedwapa, pamene anthu asamukira ku mizinda n’kuyamba kukhala moyo wotukuka, ziweto zapanyumba zayamba kuchuluka. Zimenezi zabweretsa mavuto ena m’mayiko otukuka.

Pa ziweto zonse za padziko lapansi zimene akuziyerekezera kuti n’zokwana 500 miliyoni, ziweto pafupifupi 200 miliyoni zimapezeka ku United States. Kumeneko kuli agalu pafupifupi 59 miliyoni ndi amphaka 75 miliyoni. Komabe, ku London ndi ku Paris, ziweto zimene khomo lililonse lili nazo n’zochuluka kuposa ku New York City!

Zaka zingapo zapitazo ku Paris anachita lendi njinga zamoto zokwana 70 zochotsa ndowe za agalu kuti ziyeretse njira zoyenda anthu za m’mbali mwa misewu. Anayerekezera kuti agalu pafupifupi 250,000 ku Paris amatulutsa ndowe zokwana matani 25 tsiku lililonse, ndipo zosakwana theka la zimenezi n’zimene zimachotsedwa ndi njinga zamoto zochotsa ndowezo. Anthu ambirimbiri chaka chilichonse akuti amavulala n’kugonekedwa m’zipatala ataterereka pa ndowe za agaluzo.

Kuwonjezera apo, palinso vuto la phokoso. Eni agalu ena amalola agalu awo kuchita zinthu zimene sangalole kuti anthu achite. Nkhani ya pa intaneti yonena za ziweto yotchedwa The Pet Care Forum inati: “Zikuoneka kuti eni ake a agalu owuwa kwambiri amaphunzira kunyalanyaza phokosolo.” Mwachitsanzo, ena sachita chilichonse kuti aletse agalu awo kuwuwa, ngakhale pamene phokosolo likuwalepheretsa kulankhulana bwino ndi munthu wina pa nkhani yofunikira.

Komanso, galu akhoza kukhala phee ndiponso mwamtendere akakhala ndi mbuye wake koma mbuye wakeyo akachoka, akhoza kusoŵetsa mtendere kwambiri anthu ena okhala pafupi. N’zoona kuti eni ake a ziweto akhoza kukonda zinyama zawozo ngakhale zili ndi mavuto oterowo, koma munthu amene amagwira ntchito ya mashifiti amene amakhala naye pafupi kapena mayi wa khomo lina amene akufuna kugoneka mwana wake sangamve chimodzimodzi. Kuwonjezera apo, zinyama zimene zikusowa chochita zingayambe kusonyeza khalidwe lowononga zinthu, n’kuyamba kusokonezeka maganizo, ngakhale kuvulaza anthu kumene.

Vuto limene makamaka likupezeka m’mizinda ndilo kuswana kwambiri kwa ziweto. Akuyerekezera kuti agalu 17 miliyoni ndi amphaka 30 miliyoni amabadwa ku United States chaka chilichonse. Zambiri mwa zinyama zimenezi amakazisiya ku malo osungirako zinyama zotayika kapena zosafunidwa, kumene chaka chilichonse m’dziko limenelo lokha akuyerekezera kuti zinyama pafupifupi 4 miliyoni mpaka 6 miliyoni amazipha.

N’chifukwa chiyani zinyama zambirimbiri amazitumiza ku malo ameneŵa? Nthaŵi zambiri n’chifukwa chakuti chikondi cha anthu pa ziweto chingakhale cha nthaŵi yochepa chabe. Kagalu kosangalatsa kapena kamphaka kokongola kamene anali kukakonda kamakula n’kusanduka nyama yaikulu yofunika kuisamalira. Koma mwina m’nyumbamo mungakhale mulibe munthu amene ali ndi nthaŵi kapena kuleza mtima kofunika kuti aziseŵera kapena kuphunzitsa chiwetocho. Dr. Jonica Newby, wolemba mabuku komanso katswiri wa zinyama anati: “Mosiyana ndi zimene anthu ambiri amakhulupirira, kafukufuku amene anachitika pa dziko lonse wasonyeza nthaŵi zonse kuti theka la agalu amene amakasiyidwa ku malo osungirako zinyama zotayika kapena zosafunidwa sikuti amakhala otayidwa, m’malo mwake amakasiyidwa kumeneko ndi ambuye awo amene sangathenso kupirira ndi kuwuwa, kuwononga, kapena kuchuluka kwa mphamvu za ziwetozo.”

Nkhani ina yonena za kuchuluka kwa ziweto inafotokoza mwachidule zimenezi kuti: “Zamoyo zasanduka zinthu zoti tikhoza kutaya, zomwe tingazikumbatire zikakhala zazing’ono n’kuzitaya zikayamba kusoŵetsa mtendere. Kusaganizira moyo wa zinyama koteroko kukuchuluka ndipo kukuwononga chikhalidwe chathu.”

Mfundo Zofunika Kuziganizira

Kusunga chiweto, makamaka mu mzinda, ndi nkhani yofunika kuiganizira bwino. Ziweto zamphamvu zimafuna kuchita zinthu zolimbitsa thupi tsiku lililonse kuti zikhale ndi thanzi labwino. Kafukufuku wotchedwa “National People and Pets Survey” ku Australia anati: “Kuyenda ndiponso kuchita ntchito zina zolimbitsa thupi n’kofunikira polimbitsa thanzi la galuyo komanso kumuthandiza kukhala ndi maganizo abwino. Agalu amene sachita zinthu zolimbitsa thupi zokwanira akhoza kuyamba kukhala ovuta kuwayang’anira.” Komabe, anthu ambiri amene ali ndi agalu amakhala otopa kwambiri madzulo akaŵeruka ku ntchito ndipo satha kupita ndi galu wawoyo kokawongola miyendo kuti akaphwetseko mphamvu zake zimene wakhala akuzisunga tsiku lonse.

Choncho, anthu amene akufuna kuweta ziweto ayenera kudzifunsa mafunso aŵa: ‘Kodi ndidzatha kusamala chiwetocho? Kodi zimene ndimachita pa moyo wanga zidzachititsa kuti chiwetocho chizidzakhala chokha nthaŵi yaitali? Kodi ndidzakhala ndi nthaŵi yopita kokayenda ndi chiweto changacho kapena kuseŵera nacho? Ngati galu wanga akufunika kuphunzitsidwa, kodi ndili wokonzeka kum’phunzitsa kapena kumupititsa ku sukulu yophunzitsa agalu kumvera? Kodi kukhala ndi chiweto kudzandithera nthaŵi imene ndikanamachita zinthu zina zofunika?’

Mfundo inanso yofunika kuiganizira ndi yoti kusunga chiweto kukhoza kukutherani ndalama zambiri. Kafukufuku amene anachitika ku United States wa anthu amene ali ndi ziweto anapeza kuti pa avareji ndalama zofunika kulipira ku vetenale pachaka ngati munthu akuweta galu ndi madola 196, pamene mphaka ndi madola 104. Koma ndalama zimenezo sizikuphatikizapo zogulira chakudya ndi zofunika zina za tsiku ndi tsiku. Kuwonjezera pamenepo, m’madera mwina pamafunika ndalama zolembetsera chiwetocho ku boma.

N’kovuta Kuti Anthu Aone Ziweto Moyenera

Mlengi wathu ayenera kuti amakondwera tikamasangalala ndi zinyama zimene analenga ndi kuzisamalira mwachikondi. Choncho, kodi simungavomereze kuti sichingakhale chinthu chabwino kuzunza zinyama? Komabe, pofuna kusangalala, anthu nthaŵi zambiri amalola zinyama, monga n’gombe, agalu, ndi nkhuku, kuti zizipwetekedwa mwankhaza ndi kuphedwa pa maseŵera omenyana. N’zomvetsa chisoni kuti zinthu zimene anthu amachitira zinyama nthaŵi zambiri n’zosagwirizana ndi zimene Mulungu ankafuna pachiyambi.

Komabe, anthu ena amadera nkhaŵa kwambiri ziweto kuposa mmene amachitira ndi zinthu zofunika kwenikweni. Ndipo ngati kukonda zinyama kwafika ponyanyira, moyo wa ziweto ungaoneke ngati wofunika kuposa wa anthu. Mwachitsanzo, pamene moto unabuka m’chipatala china cha zinyama ndipo eni ake a ziwetozo anasonkhana panja, ena akuti “analimbana ndi ozimitsa moto amene anatchinga malowo kuti munthu asalowe, ndipo anthuwo anali kufuula kuti akufuna kufera limodzi ndi zinyama zawo zokondedwazo.”

N’zoona kuti zingakhale zomvetsa chisoni kwambiri kuona chiweto chokondedwa chikufa. Koma ngakhale pa mfundo imeneyi, pamafunika kuona zinthu moyenera. Monga taonera poyamba, zinyama sizinalengedwe m’chifanizo cha Mulungu, ndipo sizinalengedwe kuti zidzakhale ndi moyo kosatha, monga mmene anthu analengedwera. Pofotokoza mmene Mulungu analengera anthu, Baibulo limati: “Waika [u]muyaya m’mitima yawo.” Koma silinanene zilizonse zofanana ndi zimenezi pankhani ya zinyama.—Mlaliki 3:11.

Choncho, Baibulo silinena kuti n’kulakwa kupha zinyama. Ndipo pakali pano nyama ndi chakudya cha anthu ambirimbiri. Koma bwanji za kupha chiweto, mwachitsanzo chiweto chimene chikudwala ndi kuvutika? Zimenezo zingakhale zovuta kuchita komanso zopweteka! Komabe, mwini chiweto angaganize zoti kungakhale bwino kuchita zimenezo mwamsanga ndiponso m’njira yoti chiwetocho chisamve kupweteka, m’malo mopatsa chiweto chake chokhulupirikacho mankhwala okwera mtengo amene angangotalikitsa kuvutika kwake, ndiponso ngakhale kuwonongetsa ndalama za banja lake.

Mulungu amakonda kwambiri anthu amene anawalenga. Kodi ifenso sitiyenera kusamala ndi kukonda zinyama zimene watipatsa udindo wozisamalira ndi kuziyang’anira? Anthu amene ali ndi chikondi choterocho nthaŵi zambiri akopeka poganizira nthaŵi imene adzasangalala ndi zinyama m’njira imene Mlengi anafunira poyambirira. Nkhani yomaliza mu nkhani zotsatizanazi ifotokoza mbali imeneyi.

[Chithunzi patsamba 15]

N’chifukwa chiyani ziweto zambiri ku malo osungirako zinyama zotayika zimaphedwa chaka chilichonse?

[Mawu a Chithunzi]

© Hulton-Deutsch Collection/CORBIS

[Zithunzi pamasamba 16, 17]

Makamaka kwa anthu a m’mizinda, chiweto chingafune zambiri kuposa zimene ambiri amaganiza

[Chithunzi patsamba 17]

Mlengi wathu amasangalala tikamakomera mtima zinyama