Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Anapulumuka Madzi Atasefukira!

Anapulumuka Madzi Atasefukira!

Anapulumuka Madzi Atasefukira!

Yolembedwa ndi wolemba Galamukani! ku Switzerland

MU October 2000, kunamveka kuti madzi asefukira m’madera osiyanasiyana a padziko lonse. Mvula yamphamvu inagwa m’mapiri, moti madzi ake okhala ndi miyala ndi chithope anakokolola zinthu zosiyanasiyana ngakhale mitengo yathunthu!

M’dera la Valais lomwe lili kummwera kwa dziko la Switzerland munagwa tsoka lotereli. Pakati penipeni pa dera limeneli, mulitali mwake, panadutsa mtsinje wa Rhône womwe umaloŵera cha kumadzulo kuchokera ku chigawo chokhala ndi madzi oundana chotchedwanso kuti Rhône chomwe chili m’chigawo chapakati cha mapiri a Alps ndipo mtsinjewu umakafika ku nyanja ya Geneva, ulendo wautali makilomita 170. Mapiri amene ali ku matsidya onse aŵiri a mtsinjewu amachititsa kuti madzi amvula azikafika mumtsinjemo kudzera m’timakwawa tambirimbiri tatikulu mosiyanasiyana. Kayendedwe ka madzika sikabweretsa vuto lililonse zinthu zikakhala bwinobwino. Koma madzi a mvula akadzaza dera lonselo, nthaŵi zambiri zinthu zimasokonekera.

Zimenezi ndi zomwe zinachitika ku Gondo, kumalire a dziko la Italy. Mbali yaikulu ya tauni yam’mapiri imeneyi, yomwe mumakhala anthu 150 inawonongeka chifukwa cha madzi osefukira okhala ndi matope ndiponso miyala. Posakhalitsa madzi osefukira chifukwa cha mvula ya mphamvuyo anafikanso m’madera ena a ku Valais. Misewu ndiponso njanji zinatsekeka, ndipo nyumba zinayamba kudzaza ndi matope ndiponso miyala. M’malo ena munkadzaza matope moti ankafika mamita anayi kutalika kwake kuchokera pansi. Mayi wina anaona chithope chotalika mamita 30 kuchoka pansi chikukokolola zimiyala zikuluzikulu ndiponso mitengo yomera n’kumaloŵera ku tauni imene ankakhala!

Markus ndi mkazi wake Tabitha, ankakhala ku Mörel mmene zoopsazi zinkachitika. Markus anati: “Tinadzidzimuka nthaŵi itangokwana sikisi koloko m’maŵa titamva chimkokomo cha madzi ndiponso kugwedezeka.” Ndinatuluka panja tochi ili m’manja kuti ndikaone chimene chikuchitika ndipo zimene ndinaonazo zinandiopsa kwambiri. Nyumba ndiponso milatho inaphwasuka chifukwa cha miyala yosaneneka, ndipo panali galimoto ina imene inamenyetseka kunyumba yoyandikana nafe. Chakumunsi pang’ono, munthu wina woyandikana nafe pamodzi ndi mkazi wake yemwe, ankalephera kutuluka m’nyumba mwawo. Ndinawathandiza kutulukira pawindo. Nditabwerera kunyumba kwanga, ineyo ndi mkazi wanga Tabitha tinali ndi nthaŵi yokwanira kungonyamula zinthu zathu zingapo chabe basi.”

Markus ndi Tabitha ndi a Mboni za Yehova, ndipo anakapeza anzawo a Mboni okhala nawo m’dera lomwe kunalibe zoopsazi. Markus anati: “Ngakhale kuti tinapulumuka, zoopsazi zinam’sokoneza maganizo Tabitha kwa masiku ambiri.” Koma kodi n’chiyani chinam’thandiza kuti asiye kuganizira kwambiri zoopsazo? Tabitha anati: “Kukhala ndiponso kulimbikitsidwa ndi abale ndi alongo a chikhulupiriro changa,” ndipo anawonjezera kuti: “Komanso anthu ambiri m’dera lathu anasonyeza mtima woganizira kwambiri anzawo.”

Zimenezi zinakumbutsa Markus ndi Tabitha lemba la Miyambo 18:24 lomwe limati “lilipo bwenzi lipambana ndi mbale kuumirira.” Panthaŵi ya mavuto anzathu otereŵa amafunikadi kwambiri!

[Mapu patsamba 18]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Dera lokhudzidwa

Gondo

[Chithunzi patsamba 18]

Markus ndi Tabitha

[Mawu a Chithunzi patsamba 18]

Mise à disposition par www.crealp.ch