Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Tsiku Lofunika Kulikumbukira Lamlungu pa April 4, 2004

Tsiku Lofunika Kulikumbukira Lamlungu pa April 4, 2004

Tsiku Lofunika Kulikumbukira Lamlungu pa April 4, 2004

USIKU, patsiku limene anaphedwa, Yesu Kristu anakhazikitsa Chikumbutso cha imfa yake. Yesu anagwiritsira ntchito vinyo ndi mkate wopanda chotupitsa m’njira yophiphiritsira, ali ndi atumwi ake pamgonero wosakhala n’zakudya zambirimbiri, ndipo anati: “Chitani ichi chikumbukiro changa.”—Luka 22:19.

A Mboni za Yehova, akukuitanani ndi mtima wonse kuti mukasonkhane nawo pa Chikumbutso chimenechi chomwe chimachitika chaka chilichonse . Chaka chino Chikumbutsochi chidzachitika Lamlungu madzulo, pa April 4. Detili ndi limene pa kalendala ya m’Baibulo yoyendera mwezi lili deti la Nisani 14. Yesetsani kufunsa a Mboni za Yehova kwanuko kuti akuuzeni malo ndi nthaŵi yeniyeni ya mwambowu.