Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Banja Liyesedwa Chikhulupiriro

Banja Liyesedwa Chikhulupiriro

Banja Liyesedwa Chikhulupiriro

INDIA, ndi mtsikana wokongola wazaka naini yemwe amakhala ku Wisconsin, m’dziko la United States, ndipotu iye akudziŵa bwino mmene matenda amakhalira. India wachitidwapo kale maopaleshoni atatu akuluakulu pamodzinso ndi kulandira chithandizo m’njira zina zambirimbiri. Mayi ake, a Lori anati: “Kwa zaka sikisi, moyo wa India unali wongokhalira kupita ndiponso kugona kuchipatala komanso kuonana ndi madokotala.”

Zonsezi zinayamba India ali ndi chaka chimodzi ndi theka. Iye anayamba kuonetsa zizindikiro zodabwitsa, monga kutsegula m’mimba kosalekeza, kutentha thupi kwambiri, kutupa mimba, ndi kuwonda modetsa nkhaŵa. Ankamvanso kuwawa m’mimba. Kwa zaka ziŵiri, usiku uliwonse, kamwanaka kankadzuka kaŵirikaŵiri n’kuyamba kulira, kudandaula, ndiponso nthaŵi zambiri kankakuŵa kwambiri chifukwa cha ululu.

India anavutika mosaneneka kwinaku madokotala akuyesa umu ndi umu pofuna kudziŵa kuti vuto lake n’chiyani. Lori anati: “Mwana wathu anali kufa ndi njala.” Mark, yemwe ndi bambo wake wa India anati: “Chaka chinatha mwana wathu akungowonda ifeyo n’kumangoyang’ana chifukwa chosoŵa pogwira. Ndikukumbukira tsiku lina usiku, nditathedwa nzeru kwambiri, ndiye tinkakambirana ndi mkazi wanga Lori zimene tichite India akamwalira, chifukwa panthaŵiyi zakuti akhala moyo tinali titaiwalako.”

Patapita nthaŵi, India anam’peza ndi matenda a zilonda za m’mimba. Komanso anali ndi matenda otupa mitsempha ya ndulu yodutsa m’chiŵindi. Matenda ameneŵa anali ochiritsika. Komano anafunika opaleshoni, ndipo anafunikanso kumwa mankhwala ochiritsa matenda ake a zilonda za m’mimba aja. Matenda onseŵa amafunika kuti wodwalayo aziyang’aniridwa ndiponso kusamalidwa kwambiri.

Tsopano patha zaka seveni kuchokera pamene India anayambira kudwala. Panopo akupezako bwino, chifukwa chosamalidwa bwino ndi madokotala. Mark ndi Lori ndi a Mboni za Yehova ndipo amaona kuti chifukwa chokhulupirira Mawu a Mulungu, makamaka zimene amanena pa nkhani ya matenda, imfa, ndi chiyembekezo chakuti akufa adzauka, zawathandiza kuti apirire. N’chimodzimodzinso ndi India. Lori anati: “Kuyambira kale, India wakhala akuuza anthu momasuka za chiyembekezo chakuti akufa adzauka chimene chimatchulidwa m’Baibulo. Sakayikira ngakhale pang’ono zakuti akufa adzaukadi.”

Nthaŵi ina India anali m’chipinda choseŵereramo pachipatala chinachake, ndipo anakumana ndi kamtsikana kanzake kamene kanali ndi mng’ono wake wodwala matenda a kansa ya m’magazi. Mayi a India analongosola motere zimene zinachitika: “Mtsikanayo anamuuza India kuti akuona kuti mng’ono wake amwalira. Motero India anamulongosolera mtsikanayu zimene Baibulo limanena pa nkhani ya imfa ndi kuti iyeyo saopa kufa. Tsiku lotsatira, mayi ake a mtsikanayo anandipeza n’kuyamba kundifunsa mafunso. Anadabwa kuona kuti India analimba mtima kukamba za imfa momasuka choncho.”

Mark ndi Lori aona kuti mapemphero a okhulupirira anzawo awathandiza kwambiri. Mark anati: “M’mbuyomo, ndikamauza anthu kuti ndikakukumbukirani m’mapemphero anga kapena ndikamapemphera nawo, ndinkaona ngati kuti sindikuwathandiza kwenikweni powapempherera chabe. Koma tsopano ndazindikira kufunikira kopempherera pamodzi ndi ena ndiponso kufunikira kopempherera ena. Chinthu chimene chinatithandiza kwambiri m’vuto lathu ndicho mapemphero a ena. Komatu tili ndi abale auzimu otikonda kwambiri!”

Mark amaonanso kuti matenda a India awathandiza kuti aganizepo mofatsa pa zinthu zimene amaona kuti n’zofunika kwambiri m’moyo wawo. Iye anati: “Panopo chuma sitikuchionanso monga mmene tinkachionera poyamba. Mwana wanu akamadwala chuma sichioneka ngati chinthu chofunika n’komwe! Zinthu zofunikadi m’moyo ndizo ubwenzi wathu ndi Yehova Mulungu ndiponso ubale wathu wachikondi.”

Mark, Lori ndiponso India ndi abale ake amalakalaka zimene zidzachitike m’dzikoli m’tsogolo malingana ndi mmene mneneri Yesaya ananenera kuti “wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.”—Yesaya 33:24; Chivumbulutso 21:4.

[Chithunzi patsamba 30]

Uyu ndi India Erickson

[Chithunzi patsamba 31]

Chipatala cha San Diego Children’s Hospital

[Chithunzi patsamba 31]

India ndi anthu a m’banja mwake