Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Timafuniranji Chiyembekezo?

Kodi Timafuniranji Chiyembekezo?

Kodi Timafuniranji Chiyembekezo?

KODI Daniel, yemwe ankadwala matenda a kansa, amene tam’tchula m’nkhani yam’mbuyo uja, akanati asatayebe mtima zinthu zikanamuyendera bwanji? Kodi akanachira matenda a kansawo? Kodi bwenzi ali moyobe panopo? Ngakhale anthu ogogomezera kwambiri ubwino wa chiyembekezo sanganene kuti akanatero. Ndipotu pamenepa pagona mfundo yofunika kwambiri; mfundo yakuti sitiyenera kukokomeza ubwino wa chiyembekezo. Chiyembekezo si mankhwala ochiritsa vuto lililonse.

Poyankha mafunso omwe a bungwe lofalitsa nkhani la Columbia Broadcasting System anali kumufunsa, Dr. Nathan Cherney anachenjeza kuti kukokomeza ubwino wa chiyembekezo kungathe kupweteketsa odwala amene matenda awapezeketsa kwambiri. Iye anati: “Taonapo amuna akunena akazi awo kuti akufulumira kutaya mtima.” Dr. Cherney anapitiriza kuti: “Maganizo ameneŵa achititsa anthu kumaona kuti matenda awo angathe kuchepa ngati sakutaya mtima, ndiyeno matendawo akamaipiraipira ena amaganiza kuti ndiye kuti odwalawo akufulumira kutaya mtima, komatu uku n’kulakwa.”

Zoona zake n’zakuti anthu amene akudwala matenda akayakaya amasauka nawo kwambiri matendawo. Motero si bwino kuti pamwamba pa zimenezi, ife owakondafe tiwachititse kuti azidziimba mlandu. Komano kodi tingati chiyembekezo chilibe kanthu?

Ayi sitingatero. Mwachitsanzo, dokotala tam’tchula uja, ndi katswiri wa chithandizo chosalimbana ndi nthenda kapena kutalikitsa moyo wa wodwala, koma chongothandiza kuti moyo wake ukhale wofeŵerapo panthaŵi yonse yomwe akudwalayo. Madokotala otereŵa amaona kuti chithandizo chokhazikitsa pansi maganizo a wodwala, ngakhale amene matenda awapezeketsa kwambiri, n’chothandiza kwabasi. Pali umboni wochuluka wosonyeza kuti chiyembekezo n’chothandiza m’njira imeneyi komanso m’njira zina zambiri.

Kuthandiza Kwake kwa Chiyembekezo

Mtolankhani wina amene amalemba nkhani za matenda, dzina lake Dr. W. Gifford-Jones anati: “Chiyembekezo ndi mankhwala amphamvu kwambiri.” Iyeyu anaŵerenga akafukufuku osiyanasiyana omwe anachitidwa pofuna kudziŵa ubwino wolimbikitsa anthu amene akudwala mwakayakaya. Akuti zimenezi zimawathandiza kuti asamataye mtima. Atafufuza m’chaka cha 1989 anapeza kuti odwala amene anathandizidwa m’njira imeneyi ankakhala ndi moyo wautaliko, komano atafufuza posachedwapa sanapeze mfundo iliyonse yotsimikizira zimenezi. Komabe zina zimene akhala akufufuza zatsimikizira kuti odwala amene amalimbikitsidwa savutika maganizo ndiponso samva kuwawa monga odwala ena.

Taganiziraninso za kafukufuku wina wofuna kudziŵa kuti kutaya mtima ndiponso kusataya mtima kumakhudzana bwanji ndi matenda a mitsempha ya kumtima. Amuna okwana 1,300 anawaonetsetsa kwa nyengo yaitali kuti adziŵe ngati anali okonda kutaya mtima msanga kapena ayi. Patatha zaka teni anadzapeza kuti amuna opitirira 12 pa 100 aliwonse pa gululi anadzadwala matenda a mitsempha ya kumtima. Ndipo pa gulu la odwalawo, amuna amene ankataya mtima msanga anali ochuluka moŵirikiza poyerekezera ndi amene sankataya mtima msanga. Laura Kubzansky, yemwe ndi pulofesa wothandizira wa zaumoyo ndi makhalidwe a anthu ku Harvard School of Public Health anati: “Umboni wambiri wotsimikizira kuti ‘kusataya mtima’ kumathandiza pa thanzi la munthu n’ngosatsimikizirika ndi sayansi. Komano pa kafukufuku amene tachitayu, kwa nthaŵi yoyamba, tapeza umboni weniweni wa sayansi wotsimikizira kuti kusataya mtima n’kothandiza munthu akamadwala matenda a mitsempha ya kumtima.”

Ofufuza ena anapeza kuti anthu amene amadziona kuti alibe thanzi labwino sachira mwamsanga pambuyo powachita opaleshoni kusiyana ndi anthu amene amadziona kuti ali ndi thanzi labwino. Akuti zikuoneka kuti kusataya mtima msanga kumathandizanso kuti munthu akhale ndi moyo wautali. Pa kafukufuku wina anafuna kudziŵa mmene kuona ukalamba ngati chinthu chabwino kapena choipa kumakhudzira anthu achikulire. Anthu ena achikulire atawachititsa kuti aziona mawu ongoonekera kwa kanthaŵi kochepa osonyeza kuti kukalamba kumasonyeza nzeru ndi kukhwima maganizo, achikulirewo anapezeka kuti ayamba kuyenda mwamphamvu. Mphamvu anapezazo n’zofanana ndi zimene akanapeza akanati azichita maseŵera olimbitsa thupi kwa milungu 12!

Kodi n’chifukwa chiyani zinthu ngati chiyembekezo, kusataya mtima, ndiponso maganizo abwino zimaoneka kuti zimatipatsa thanzi labwino? N’kutheka kuti asayansi ndiponso madokotala sangatiuze yankho lotsimikizika la funsoli chifukwa samvetsa bwinobwino mmene maganizo ndiponso thupi la munthu limayendera. Komabe akatswiri otere, amene amafufuza nkhaniyi angathe kunenapo malingaliro awo monga anthu oti akuidziŵa bwino nkhaniyi. Mwachitsanzo, pulofesa wina wa zaubongo anati n’kutheka kuti n’chifukwa choti: “Timamva bwino m’thupimu tikakhala osangalala ndiponso osataya mtima. Tikamamva choncho sitikhala ndi nkhaŵa iliyonse ndipo thupi lathu limasangalala. Chimodzi mwa zinthu zina zimene anthu angachite kuti akhale athanzi n’chimenechi.”

Madokotala, akatswiri a maganizo a anthu, ndiponso asayansi ena zimenezi angazione ngati nzeru zatsopano, komatu izi si zatsopano kwa anthu ophunzira Baibulo. Kwa zaka pafupifupi 3,000 zapitazo, mfumu yanzeru Solomo inauziridwa kulemba mawu aŵa: “Mtima wosekerera uchiritsa bwino; koma mzimu wosweka uphwetsa mafupa.” (Miyambo 17:22) Onani kuti lembali silikukokomeza nkhaniyi. Silikunena kuti mtima wosekerera ungathe kuchiritsa nthenda ina iliyonse koma langoti “uchiritsa bwino.”

Ndipotu, sikungakhale kulakwa kufunsa kuti kodi chiyembekezo chikanakhala kuti ndi mankhwala, alipo dokotala amene akanapanda kulembera odwala ake mankhwalaŵa? Komansotu chiyembekezo chimathandiza m’njira ina yofunika kwambiri kuposa thanzi chabe.

Mmene Kusataya Mtima Ndiponso Kutaya Mtima Kumakhudzira Moyo Wanu

Ofufuza anapeza kuti anthu osakonda kutaya mtima amapindula kwambiri chifukwa cha maganizo otere. Nthaŵi zambiri amachita bwino kusukulu, kuntchito ngakhalenso pa zamaseŵera. Mwachitsanzo, anachita kafukufuku pa timu ina ya atsikana yochita maseŵera osiyanasiyana. Makochi a timuyo anafotokoza zonse zokhudza maluso a atsikanawo pa maseŵerawo. Komanso, mtsikana aliyense anam’funsa bwinobwino payekha n’kudziŵa kuti ali ndi chiyembekezo chachikulu motani. Kunapezeka kuti chinthu chothandiza kwambiri kuti atsikanawo aziseŵera bwino chinali chiyembekezo chawo osati maluso ena onse amene makochi awo anatchula. Kodi n’chifukwa chiyani chiyembekezo chimathandiza kwambiri chonchi?

Pali zambiri zimene zadziŵika pofufuza zimene zimachitika tikataya mtima. Atafufuza nkhaniyi cha m’ma 1960, anatulukira zodabwitsa pa khalidwe la nyama, zomwe zinachititsa kuti pabwere mawu akuti “kutaya mtima kochita kuphunzira.” Kenaka anapeza kuti anthu angathenso kukhala ndi vutoli. Mwachitsanzo, pofuna kutsimikiza zimenezi anatenga anthu n’kuwaika pa malo aphokoso loboola mkutu atawauza kuti angathe kuzimitsa phokosolo podina mabatani enaake. Anthuwo anakwanitsa kuzimitsa phokosolo.

Gulu lina la anthu linauzidwa kuchita chimodzimodzi, komano anthuwo akadina mabataniwo palibe chimene chinkachitika. N’zosadabwitsa kuti ambiri pa gululi anafika pongotaya mtima kuti phokosolo silisiya. Kenaka atawayesanso anthuwo anachita mphwayi moti sanayese n’komwe kuzimitsa phokosolo. Iwowo anali ataona kuti palibe chilichonse chimene angachitepo kuti phokosolo lileke. Koma ngakhale m’gulu lachiŵirili, anthu osataya mtima sanalefuke maganizo n’kusiya kuyesayesa.

Dr. Martin Seligman, amene anathandiza kukonza njira zofufuzira pa akafukufuku ena oyamba aja anakhudzidwa mtima kwambiri ndi zimene anapeza pa ntchito yofufuza mmene kutaya mtima ndiponso kusataya mtima kumakhudzira anthu moti anaisandutsa ntchito yake yeniyeni. Iyeyu anafufuza mosamala za mmene anthu amene ankakonda kudziona ngati olephera amaganizira. Iye anapeza kuti kutaya mtima motere kumasokoneza anthu kuchita zinthu zambiri m’moyo mwinanso kuwalepheretseratu kuchita zinthu bwinobwino. Ponenapo mwachidule za kutaya mtimaku Seligman anati: “Nditafufuza nkhaniyi kwa zaka 25 ndatsimikiza kuti ngati nthaŵi zambiri maganizo athu ali ofanana ndi maganizo a anthu osachedwa kutaya mtima, pomaganiza kuti zinthu zikangolakwika ndiye kuti olakwa ndi ifeyo, komanso kuti zipitirirabe kutero, ndipo kuti zingathe kusokoneza zochita zathu zonse, chimachitika n’chakuti timakumanadi ndi zovuta zambiri kusiyana ndi zimene tikanakumana nazo.”

Kwa ena, izinso zingaoneke ngati zatsopano, komatu si zachilendo kwenikweni kwa anthu ophunzira Baibulo. Taonani mwambi uwu: “Ukalefuka tsiku la tsoka mphamvu yako ichepa.” (Miyambo 24:10) Inde, Baibulo limalongosola momveka bwino kuti mukafooka chifukwa cha maganizo, mumalefuka. Ndiyeno kodi mungatani kuti musamataye mtima msanga koma muzikhala ndi chiyembekezo chachikulu?

[Chithunzi pamasamba 12, 13]

Chiyembekezo chingakuthandizeni kwambiri