Kodi Zimatani Kuti Ayambe Kuwavutitsa
Kodi Zimatani Kuti Ayambe Kuwavutitsa
Monika atangomaliza sukulu anayamba kugwira ntchito ya ukalaliki wokhudzana ndi zamalamulo. Iye ankaganiza kuti moyo wapantchito auzoloŵera mosavuta.
Horst anali dokotala wa zaka za m’ma 35. Anali ndi mkazi ndi ana, ndipo zimaoneka kuti adzakhala munthu wodziŵika ndiponso wandalama.
Monika ndiponso Horst ankavutitsidwa kuntchito zawo.
NKHANI ya Monika ndi Horst imatiphunzitsa mfundo yofunika kwambiri yakuti: N’zovuta kudziŵa kuti anthu amene angavutitsidwe amakhala anthu otani. Inde, aliyense angathe kuvutitsidwa, zilibe kanthu kuti akugwira ntchito yotani. Ndiyeno kodi mungadziteteze m’njira yotani? Njira imodzi ndiyo kudziŵa mmene mungakhalire
mwamtendere kuntchito, ngakhale anthu amene mumagwira nawo ntchito atakhala ovuta.Kugwirizana ndi Amene Mumagwira Nawo Ntchito
Ntchito zimene ambiri amagwira zimafuna kugwirira pamodzi monga gulu n’kumathandizana mogwirizana. Ngati anthu a m’gululo akugwirizana, ntchito imayenda bwino. Ngati sakugwirizana, ntchito imasokonezeka ndipo m’posavuta kuti wina ayambe kuvutitsidwa.
Kodi n’zifukwa zotani zimene zingachititse kuti gulu lotere lisayendetse bwino ntchito yawo? Chimodzi ndicho kusinthasintha anthu ogwira nawo ntchito. Anthu akamasinthasintha chonchi, m’povuta kugwirizana. Komanso, anthu atsopano sadziŵa bwinobwino mmene ntchito imayendera, motero amachedwetsa anzawo onse m’gululo. Ntchito ikamakula, nthaŵi zambiri gululo limapanikizika.
Komanso ngati gululo lilibe cholinga chimodzi chomwe likufuna kukwaniritsa, n’zovuta kuti lingachite zinthu mogwirizana. Zimenezi zingachitike, mwachitsanzo, ngati bwana woopa kulandidwa udindo akutaya nthaŵi yake yambiri polimbana ndi kuteteza udindo wakewo m’malo motsogolera anthu. Bwanayo angafike pomayambanitsa dala anthu antchitowo pofuna kupezerapo mpata woonetsa ubwana wake. Kuphatikiza apo, mwinanso gululo lingakhale lopanda dongosolo lenileni lochitira zinthu moti antchito ena sangadziŵe bwinobwino kuti udindo wawo umayambira ndiponso kuthera pati. Mwachitsanzo, pangabuke mikangano ngati anthu aŵiri ogwira ntchito akuganiza kuti onse ali ndi udindo wokhala munthu womaliza kusayinira malisiti enaake.
Zikatere, zimavuta kukambirana momasuka ndipo nthaŵi zambiri anthu amakhala ndi chakukhosi. Nsanje imasokoneza kagwiridwe ka ntchito, ndipo imachititsa antchito kumapikisana pofuna kuti azikondedwa ndi bwana. Wina akangosemphana nawo maganizo pang’ono, iwowo amaona kuti wawalakwira kwambiri. Kwenikweni kankhani kang’onong’ono kamatha kukula kwabasi. Apa m’pamene pamaloŵera khalidwe lovutitsa ena kuntchito.
Anthu Amene Amakonda Kuwavutitsa
Pakatha nthaŵi, pamadzapezeka munthu mmodzi amene ena amakonda kumuvutitsa. Kodi ndi munthu wotani amene angayambe kumuvutitsa motere? Amakhala makamaka munthu amene amaoneka kuti n’ngosiyana ndi ena. Mwachitsanzo, angathe kukhala mwamuna amene ali yekhayekha pagulu la akazi kapena mkazi amene ali yekhayekha pagulu la amuna. Amathanso kukhala munthu wosadzikayikira amene ena akumuona ngati wamavuvu, kapena munthu wofatsa amene ena akumuona ngati wachinyengo. Wovutitsidwayo angathenso kukhala wosiyana ndi ena, mwina chifukwa chokhala wamkulu kapena mwana kwambiri kapena chifukwa chokhala munthu woidziŵa kwambiri ntchitoyo.
Mulimonsemo, anzakewo “amamusautsa ndi kumusambula ndipo mavuto awo amawathetsera pa iyeyo pofuna kuti akhazike mitima yawo m’malo,” inatero magazini ya zachipatala ya ku Germany yotchedwa mta. Wovutitsidwayo akayesa kuthetsa vutoli, saphula kanthu ayi ndipo mwinanso amangoipitsiraipitsira zinthu. Kuvutitsidwaku kukapitirira, munthuyo amayamba kusoŵa mnzake. Zikafika pamenepa, ndiye kuti vutoli walephera kuthana nalo payekha.
Inde, kuyambira kale anthu ena akhala akuvutitsidwa kuntchito. Koma ambiri angathe kukumbukira kuti nthaŵi inayake anthu ankagwirizana ndithu kuntchito. Zoukira munthu mmodzi sizinkachitikachitika. Koma panopa zinthu zasintha n’kufika poti “anthu ambiri asiya kuchita zinthu mogwirizana ndiponso mwamanyazi,” monga mmene dokotala wina analongosolera. Masiku ano anthu saona ngati vuto kutengetsana ndi munthu wina poyerayera kuntchito.
Motero, m’pake kuti anthu onse amene ali pantchito akhudzidwe ndi yankho la mafunso akuti: Kodi n’zotheka kupeŵa kuvutitsidwa kuntchito? Kodi mungapeze bwanji mtendere kuntchito?
[Zithunzi patsamba 6]
Cholinga chovutitsa ena ndicho kuwapangitsa kuti aziona kuti palibe amawafuna kuntchitoko