Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Ukwati Tiyenera Kuuona Kuti N’ngopatulika?

N’chifukwa Chiyani Ukwati Tiyenera Kuuona Kuti N’ngopatulika?

Lingaliro la Baibulo

N’chifukwa Chiyani Ukwati Tiyenera Kuuona Kuti N’ngopatulika?

ANTHU ambiri masiku ano anganene kuti amakhulupirira kuti ukwati n’ngopatulika. Nangano n’chifukwa chiyani maukwati ambiri amathera n’kusudzulana? Ena ukwati amangouna ngati chinthu chimene umangolonjeza basi ndiponso ngati chinthu chongosayinirana papepala. Komatu anthu malonjezo sawaona ngati kanthu. Anthu amene ukwati amauona motere, siziwavuta kuthetsa ukwatiwo akaona kuti zinthu sizikuwayendera.

Kodi Mulungu amauona bwanji ukwati? Yankho la funsoli limapezeka m’Mawu ake, Baibulo, pa Ahebri 13:4, pomwe pamati: “Ukwati uchitidwe ulemu ndi onse.” Mawu a Chigiriki amene anawamasulira kuti ‘kuchitiridwa ulemu’ amatanthauza kuti chinthucho n’chamtengo wapatali zedi ndipo n’chofunika kwambiri. Chinthu chimene timachiona kuti n’chofunika, timayesetsa kuchisunga bwino kuti chisatayike, ngakhale mwangozi. Ukwatinso tiziuona chimodzimodzi. Akristu ayenera kuona kuti ukwati n’ngopatulika, kuti n’chinthu chamtengo wapatali choyenera kuchiteteza.

N’zachidziŵikire kuti Yehova Mulungu anapanga ukwati kuti ukhale chinthu chopatulika pakati pa mkazi ndi mwamuna. Koma kodi tingasonyeze bwanji kuti ifenso ukwati timauona choncho?

Chikondi ndi Ulemu

Kuti anthu okwatira alemekeze ukwati amafunika kuti azilemekezana. (Aroma 12:10) Mtumwi Paulo analemba mawu otsatiraŵa kwa Akristu a zaka 100 zoyambirira: “Yense payekha, yense akonde mkazi wake wa iye yekha, monga adzikonda yekha; ndipo mkaziyo akumbukire kuti aziopa mwamuna.”—Aefeso 5:33.

N’zoona kuti nthaŵi zina mwamuna kapena mkazi wanu angapange zinthu zosati mungamukonde nazo kapenanso kum’patsa nazo ulemu. Koma, Akristu ayenera kusonyezabe chikondi ndi ulemu wotero. Paulo analemba za “kulolerana wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali nacho chifukwa pa mnzake; monganso Ambuye anakhululukira inu, teroni inunso.”—Akolose 3:13.

Kukhala ndi Nthaŵi Yosamalirana

Anthu okwatirana amene amaona ukwati wawo ngati chinthu chopatulika amayesetsa kusamalirana m’njira zosiyanasiyana zofunika kwa anthu okwatirana. Kugona malo amodzi monga mkazi ndi mwamuna ndi imodzi mwa njira zoterezi. Baibulo limati: “Mwamunayo apereke kwa mkazi mangawa ake; koma chimodzimodzinso mkazi kwa mwamuna.”—1 Akorinto 7:3.

Koma pali anthu ena okwatirana amene aona kuti m’pofunika kuti mwamuna apite kwina kwa kanthaŵi kuti akapezeko ndalama. Nthaŵi zina amakhalirana kutali choncho kwa nthaŵi yaitali kuposa mmene amaganizira. Nthaŵi zambiri kukhalirana kutali choncho kwasokoneza maukwati, mwakuti kwapangitsapo ena kuchita chigololo ndiponso kusudzulana. (1 Akorinto 7:2, 5) Pachifukwa chimenecho, Akristu ambiri okwatirana alolera kukhala popanda zinthu zinazake kusiyana n’kuwononga banja limene amaona kuti n’lopatulika.

Pakabuka Mavuto

Pakabuka mavuto, Akristu amene amalemekeza ukwati wawo samathamangira kupatukana kapena kusudzulana. (Malaki 2:16; 1 Akorinto 7:10, 11) Yesu anati: “Yense wakuchotsa mkazi wake, kosati chifukwa cha chigololo, am’chititsa chigololo: ndipo amene adzakwatira wochotsedwayo achita chigololo.” (Mateyu 5:32) Kusudzulana kapena kupatukana popanda zifukwa zogwirizana ndi Malemba n’kusalemekeza ukwati.

Malangizo amene timapereka kwa anthu amene ali ndi mavuto aakulu a m’banja amasonyezanso mmene ifeyo timaonera ukwati. Kodi timafulumira kuwauza kuti apatukane kapena kusudzulana? N’zoona kuti nthaŵi zina pamakhala zifukwa zoyenera zopatukana, mwachitsanzo ngati munthuyo akumuzunza kwambiri kapena kusamusamalira mwadala. * Komanso, monga mmene tanenera kale, Baibulo limalola kusudzulana ngati mwamuna kapena mkazi wachita chigololo. Ngakhale zili choncho, Akristu sayenera kuthamangira kuchititsa ena kusudzulana. Chifukwatu, pamapeto pake amene angadzavutike nazo patsogolo si wolangizayo ayi koma ndi mwini vutoyo.—Agalatiya 6:5, 7.

Ukwati Musautenge Ngati Masanje

M’madera ena anthu ambiri amakwatira kapena kukwatiwa pofuna kuloledwa kukhala m’dziko linalake. Nthaŵi zambiri anthu otere amagwirizana zolipira munthu amene ali nzika ya dzikolo kuti akwatirane naye. Nthaŵi zambiri mabanja otereŵa, ngakhale kuti amakhala okwatirana, amakhala kosiyana, ndipo mwina sakhala paubwenzi wina uliwonse. Ndiye winayo akangopeza chilolezo chokhala m’dzikolo, basi amasudzulana. Iwoŵa ukwati wawo amangouna ngati bizinesi basi.

Baibulo silivomereza masanje otereŵa ayi. Ngakhale zolinga zawo zitakhala zina, anthu amene aloŵa m’banja, amaloŵa m’chinthu chopatulika chimene Mulungu amaona kuti sichiyenera kutha. Mulungu amawaonabe anthu amene agwirizana chonchi kuti n’ngokwatirana, ndipo nawonso sangasudzulane pokhapokha patakhala zifukwa zimene Baibulo limaloleza anthu okwatirana kusudzulana n’kukwatiranso munthu wina.—Mateyu 19:5, 6, 9.

Monga mmene timachitira tikafuna kukwaniritsa chinthu china chilichonse chofunika, ukwatinso timafunika kuuchitira khama ndiponso kupirira nawo kuti uyende bwino. Anthu amene saona ukwati ngati chinthu chopatulika amathetsa mosavuta ukwati wawo. Apo ayi sayesa n’komwe kukonza banja lawo kuti likhale losangalatsa. Komano, anthu amene amazindikira kupatulika kwa ukwati amadziŵa kuti Mulungu amafuna kuti banja lawo lisadzathe. (Genesis 2:24) Amazindikiranso kuti poyendetsa bwino ukwati wawo, amalemekeza Mulunguyo poti ndiye Wopanga ukwati. (1 Akorinto 10:31) Kuona ukwati m’njira imeneyi, kumawapatsa mphamvu kuti apirire ndi kuyesetsa kuyendetsa bwino ukwati wawo.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 14 Onani Nsanja ya Olonda ya November 1, 1988, masamba 22-23.