Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

N’kuntchito Kapena N’kunkhondo?

N’kuntchito Kapena N’kunkhondo?

N’kuntchito Kapena N’kunkhondo?

YOLEMBEDWA NDI WOLEMBA GALAMUKANI! KU GERMANY

“Ndinafika pongotopa nazo. Apa n’kuti nditatha zaka zoposa 30 ndikugwira ntchito m’kampaniyi. Ndinali nditapatsidwa udindo woyang’anira ena. Kenaka panabwera bwana watsopano. Anali mnyamata wamphamvu zake ndiponso wanzeru zake. Iye ankaganiza kuti ineyo ndikuloŵetsa pansi kampaniyo motero anayamba kulimbana nane. Kwa miyezi yambiri anakhala akundikalipira, kundinamizira, ndiponso kundichititsa manyazi moti ndinafika potopa nazo. Kampani itandifunsa ngati ndingakonde kupuma pantchito atandipatsa ndalama zanga ndinavomera, ndipo ndinasiyana nayo kampaniyo.” Anasimba nkhaniyi ndi Peter. *

PETER ankavutitsidwa kuntchito. Kwawo ndi ku Germany, ndipo kumeneku akuti anthu opitirira 1 miliyoni amavutitsidwa kuntchito. Ku Netherlands, munthu mmodzi pa anthu anayi aliwonse adzavutitsidwapo kuntchito m’moyo wawo. Ndipo lipoti la bungwe la International Labour Organization linati vutoli likukula ku Australia, Austria, Britain, Denmark, Sweden, ndi ku United States. Koma kodi kuvutitsidwa kuntchito n’kutani makamaka?

“Nkhondo Yovutitsa Maganizo”

Malingana ndi nyuzipepala ya ku Germany yotchedwa Focus, kuvutitsidwa kumeneku “n’kuvutitsa munthu mwakaŵirikaŵiri, mochita kumupanganira.” Kumeneku si kusereulana kwabwinobwino kwa pantchito kuja, monga kulankhulana mwakachipongwe pang’ono, kunyozana modziŵana, kunenana mongocheza, kapena kupusitsana mongoseŵera. Koma ndi kuchita zinthu zosoŵetseratu munthu mtendere. Cholinga chake chimakhala chakuti ovutitsidwayo aziona kuti palibe akumufuna pantchitopo. *

Kuvutitsidwa kotere kumatha kukhala kuvutitsana kwangati kwa ana kapena kumatha kufika pochitirana zinthu zoswa lamulo. Munthuyo amamudya miseche, kumusambwadza, kumuchitira zinthu mwamtopola, kapena kumunyalanyaza. Anthu ena otere amawapatsa dala chintchito chambiri kapenanso amakonda kuwapatsa ntchito zosautsa zimene anthu ena onse azikana. Anzawo a pantchito angathe kuwalepheretsa kugwira ntchito bwino, mwina pobisa mwadala zinthu zofunika kuti adziŵe. Nthaŵi zina, anthu ovutitsa mnzawo kuntchito amaphulitsa matayala a galimoto yake kapena kumusokonezera zinthu mu kompyuta yake.

Anthu ena amavutitsidwa ndi munthu mmodzi. Koma ambiri amavutitsidwa ndi gulu la anzawo ogwira nawo ntchito.

Mwina chodabwitsa kwambiri n’chakuti nthaŵi zambiri vutoli limachitika movomerezedwa ndi bwana. Atafufuza m’mayiko ena a ku Ulaya, anapeza kuti pa theka la anthu ovutitsidwa, mabwana oyang’anira anthuwo anali m’gulu la anthu ovutitsawo, ndipo ambiri mwa ovutitsidwawo ankavutitsidwa ndi bwana wawo yekhayo basi. Zonsezi zimachititsa kuti kuntchito kukhale “nkhondo yosatherapo yovutitsa maganizo,” monga mmene inanenera nyuzipepala ya ku Germany yotchedwa Frankfurter Allgemeine Zeitung.

Sizithera Kuntchito

Nthaŵi zambiri, mavuto obwera chifukwa chovutitsidwa kuntchito amafika patali. Ambiri ovutitsidwa amadzadwala matenda aakulu chifukwa cha nkhanza zotere. Ena mwa matenda otere ndi matenda a kuvutika maganizo, kusoŵa tulo, ndiponso vuto la mantha aakulu. Nanga kodi Peter, amene tam’tchula kumayambiriro uja, zinamuyendera bwanji? Iye anayamba kudziona ngati munthu wopanda ntchito. Mayi wina dzina lake Margaret, yemwenso ndi wa ku Germany, atadwala dokotala anamulangiza kuti apite kuchipatala cha anthu a nthenda zokhudza maganizo. Kodi chinamudwalitsa n’chiyani? Kuvutitsidwa kuntchito. Kuvutitsidwa kuntchito kungasokonezenso kwambiri ukwati kapena moyo wa m’banja wa wovutitsidwayo.

Ku Germany, anthu ambiri akuvutitsidwa kuntchito moti kampani ina ya inshuwalansi ya zaumoyo inakhazikitsa gawo loti lizithandiza anthu ameneŵa patelefoni. Kampaniyi inapeza kuti pa anthu onse oimba foniwo, anthu opitirira theka ankajomba kuntchito mwina kwa milungu sikisi. Munthu mmodzi pa atatu aliwonse ankajomba kwa miyezi itatu, ndipo anthu opitirira 10 pa 100 alionse kwa miyezi yoposa itatu. Nyuzipepala ya zachipatala ya ku Germany inati pafupifupi “anthu 20 pa anthu 100 alionse odzipha okha amadzipha chifukwa chovutitsidwa kuntchito.”

N’zoonekeratu kuti kuvutitsidwa kuntchito kumachititsa kuti kuntchito kuzikhala koopsa. Kodi pali njira iliyonse yopeŵera vutoli? Kodi munthu angapeze bwanji mtendere kuntchito?

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Mayina onse m’nkhani zotsatizana zino tawasintha.

^ ndime 6 Zimene anapeza atafufuza zimaonetsa kuti ambiri mwa anthu amene amavutitsidwa kuntchito ndi akazi, komabe n’zotheka kuti mwina n’chifukwa choti akazi ndiwo amakonda kunena za vutoli ndiponso kufuna thandizo.

[Zithunzi patsamba 4]

Kuvutitsidwa kumachititsa kuti ntchito isanduke nkhondo yovutitsa munthu maganizo