Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Onani Dziko Lokoma’

‘Onani Dziko Lokoma’

‘Onani Dziko Lokoma’

Mayi wina ataŵerenga kabuku kotchewa ‘Onani Dziko Lokoma,’ komwe kafalitsidwa posachedwapa ndipo kali ndi mapu a m’Baibulo, analemba kuti: “Chinthu chotere n’chimene ndakhala ndikufuna. Malo ndi anthu komanso zochitika za m’Malemba tsopano ndimazimvetsa bwino kwambiri.”

Kabuku kamasamba 36 kameneka, komwe kali ndi zithunzi zoonetsa mtundu weniweni wa zojambulidwazo, kamathandiza anthu ophunzira Mawu a Mulungu kuti azitha kuzimvetsa mosavuta nkhani za m’Baibulo m’maganizo mwawo. Mayi uja anapitiriza kuti: “Kuona kuti dera limene panamangidwa kachisi linali lokwera poliyerekezera ndi dera lozungulira kachisiyu kumandithandiza kwambiri kumvetsa malemba amene amanena za ‘kulambira kokwezeka’ kwa Yehova. N’zothandiza kwambiri kuona bwinobwino mmene mizinda yopulumukirako anaiyalira, ndipo n’chimodzimodzinso ndi malo ena otchulidwa m’Malemba Achihebri ndi Achigiriki. Ndinayamba kugwiritsa ntchito kabuku kabwinoka pophunzira buku la m’Baibulo la Machitidwe.”

Mayiyu anamaliza kalata yakeyi ndi mawu akuti: “Nthaŵi zambiri ndikamaŵerenga Mawu a Mulungu ndizionamo zinan’zina m’kabukuka.”

Mungathe kuitanitsa kabukuka, komwe n’kotchedwa ‘Onani Dziko Lokoma,’ polemba zofunika m’kabokosi kali pamunsika ndi kukatumiza ku adiresi imene ili pomwepoyo kapena ku adiresi yoyenera imene ili patsamba 5 la magazini ino.

□ Ndikupempha kuti munditumizire kabuku kakuti ‘Onani Dziko Lokoma.’

□ Chonde nditumizireni munthu kuti ayambe kuchita nane phunziro la Baibulo lapanyumba laulere.

[Mawu a Chithunzi patsamba 32]

Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.