Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zosuta Fodya Ine Ayi!

Zosuta Fodya Ine Ayi!

Zosuta Fodya Ine Ayi!

MUTU umenewu anaupereka kwa ana a sukulu ambirimbiri amene anachita nawo mpikisano wolemba nkhani wa bungwe la Missouri State Medical Association (MSMA) omwe unali mpikisano wa boma lonse la Missouri ku United States. Ana a sukulu pafupifupi 675 ochokera m’masukulu 42 anatumiza nkhani zawo ku mpikisanowu. Amene anapata mphoto pampikisanowu anali mtsikana wa zaka 12 dzina lake Breanna, ndipo ndakatulo yake anaisindikiza m’magazini ya bungweli yotchedwa Missouri Medicine. Breanna analinso ndi mwayi woŵerenga ndakatuloyi kwa nthumwi zimene zinapezeka pa msonkhano wapachaka wa bungweli. Asanayambe kuŵerenga, Breanna ananena mawu otsatiraŵa kwa anthuwo:

“Ineyo ndine wa Mboni za Yehova, ndipo mfundo zonse zimene ndinalemba m’ndakatuloyi ndinazitenga m’magazini ya Galamukani! Kwenikweni mfundo imene inandithandiza kuti ndilembe mbali imene ndimaikonda kwambiri m’ndakatuloyi ndinaitenga pachikuto cha magazini iyi. Pachikutochi pali chigaza cha munthu chili ndi ndudu kukamwa kwake ndipo pali mawu akuti: ‘Imfa Yogulitsa.’ Kwa zaka zambiri, magazini ya Galamukani! yafalitsa nkhani zambiri zonena za kuopsa kwa fodya.”

A Mboni za Yehova, salola zosuta fodya. Iwo amakhulupirira kuti kuwononga thupi ndi china chilichonse n’kusalemekeza mphatso ya moyo komanso n’kusalemekeza Mlengi. (Machitidwe 17:24, 25) Motero iwo amatsatira malangizo a m’Malemba akuti: “Tidzikonzere tokha kuleka chodetsa chonse cha thupi ndi cha mzimu, ndi kutsiriza chiyero m’kuopa Mulungu.”—2 Akorinto 7:1.

Monga achinyamata anzake a Mboni za Yehova, Breanna amayesetsa kutsatira mfundo za m’Baibulo. Ndithu, achinyamata onse otere amasangalatsa mtima wa Mlengi wawo.—Miyambo 27:11.

[Chithunzi patsamba 10]

Breanna (tsopano ali ndi zaka 14) wanyamula chipepala chimene pali ndakatulo yake