Zoyenera Kuchita Kuti Mukhale Pamtendere Kuntchito
Zoyenera Kuchita Kuti Mukhale Pamtendere Kuntchito
N’CHIFUKWA chiyani anthu ena amavutitsa anzawo? Baibulo limatithandiza kumvetsa nkhaniyi. Limalongosola kuti tikukhala “m’masiku otsiriza” a nthaŵi ino ndiponso kuti n’chifukwa chake tikukumana ndi “nthaŵi zoŵaŵitsa.” Anthu ambiri ndi “odzikonda okha, okonda ndalama, odzitamandira, odzikuza, amwano, osamvera akuwabala, osayamika, osayera mtima, opanda chikondi chachibadwidwe, osayanjanitsika, akudyerekeza, osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino, achiwembu, aliuma olimbirira, otukumuka mtima.” (2 Timoteo 3:1-5) M’masiku ovutaŵa, makhalidwe otere n’ngofala ndipo ndiwo amachititsa kuti anthu ena azivutitsa anzawo kuntchito. Komano kodi mungakhale bwanji pamtendere kuntchito?
Kuthetsa Mikangano
Chimayambitsa khalidwe lovutitsa ena nthaŵi zambiri ndicho kusungirana chakukhosi ndi anthu ogwira nawo ntchito. Motero, thetsani mwamsanga kusamvana kulikonse kumene kukukhudza inuyo komano musaloŵerere m’nkhani za eni. Pofuna kuziziritsa ena mitima, chitani zinthu mozindikira ndiponso mwaulemu. Aliyense muzimuona ngati munthu wokhala ndi maganizo ayekha osati maganizo oimira gulu lonse. Ngati winawake akuoneka kuti ali nanu chifukwa, yesetsani kuthetsa nkhaniyo. Kumbukirani mawu a Yesu akuti: “Fulumira kuyanjana ndi mnzako wamlandu.”—Mateyu 5:25.
Chinanso n’chakuti aliyense kuntchitoko amapindula nazo ngati mukukhala omasukirana. Motero, yesetsani Miyambo 15:22.
kukhala womasuka polankhula ndi bwana wanu popanda kuchita zinthu ngati kuti mukungofuna kuti azikukondani. Komanso kumbukirani kuti, kulankhulana momasuka ndi anzanu ogwira nawo ntchito ndiponso anthu apansi panu n’kothandiza kuti musamavutike ndi maganizo. Mfumu Solomo analemba kuti: “Zolingalira zizimidwa popanda upo; koma pochuluka aphungu zikhazikika.”—Motero, yesetsani kugwirizana ndi anzanu akuntchito. Sikuti muyenera kuchita zinthu mofuna kungosangalatsa anthu, n’kumangovomereza zilizonse, chifukwa chofuna mtendere basi. Komano kuchita zinthu mwachikondi ndiponso mwaubwenzi kungathandize kuti muyambe kumasukirana. Samalani zimene mukulankhula ndiponso mmene mukuzilankhulira. Apanso Baibulo limapereka malangizo othandiza akuti: “Mayankhidwe ofatsa abweza mkwiyo.” (Miyambo 15:1) “Lilime [lofatsa, NW] ndilo mtengo wa moyo.” (Miyambo 15:4) “Chipiriro chipembedza mkulu” wankhondo. (Miyambo 25:15) “Mawu anu akhale m’chisomo, okoleretsa, kuti mukadziŵe inu mayankhidwe anu a kwa yense.”—Akolose 4:6.
“Kufatsa Kwanu Kuzindikirike ndi Anthu Onse”
Mtumwi Paulo analangiza Akristu ku Filipi kuti: “Kufatsa kwanu kuzindikirike ndi anthu onse.” (Afilipi 4:5) Potsatira mfundo imeneyi, yesetsani kumayendera mfundo za kakhalidwe kabwino. Peŵani kudzidalira kwambiri komanso kukhala wamanyazi kwambiri. Anzanu akamakusereulani, musamawabwezere. Kufanizira khalidwe loipa simungapindule nako ayi. Muzilemekeza ena, ndipo mukamatero nthaŵi zambiri nawonso amadzayamba kukulemekezani.
Samalani ndi zochitika zanu komanso zovala zanu. Dzifunseni kuti: ‘Kodi zovala zanga zimapatsa anthu maganizo otani? Kodi maonekedwe anga n’ngokopa amuna kapena akazi? Kodi maonekedwe anga ndi osadzisamala? Kodi ndingachite bwino nditasintha kavalidwe kanga kakuntchito?’
M’madera ambiri, anthu ogwira ntchito modzipereka ndiponso mosamala ntchito amalemekezedwa ndiponso amakhala ofunika kwambiri pantchitopo. Motero yesetsani kugwira ntchito mwaluso kuti muzilemekezedwa. Muzidalirika ndiponso muzikhulupirika. Koma sikuti muzilimbana n’zofuna kuchita ntchito iliyonse mosalakwitsako ngakhale pang’ono. Mayi wina amene anavutitsidwapo kuntchito, pambuyo pake anadzavomereza kuti penapake nayenso anali wolakwa ndithu. Iye anati: “Ndinkafuna kuchita chilichonse mwambambande.” Mayiyu anadzazindikira kuti n’zosatheka kuchita chilichonse mwambambande ponena kuti: “Inde, ntchito yanga ndimaidziŵa bwino, koma sikuti ndiyenera kuchita ntchito iliyonse mosalakwitsako.”
Musamakwiye ndi zilizonse. Sikuti munthu akangokunenani ndiye kuti akukuvutitsani. M’Baibulo, Mfumu Solomo analemba kuti: Mlaliki 7:9, 21, 22.
“Usakangaze mumtima mwako kukwiya . . . Mawu onsetu onenedwa usawalabadire . . . pakuti kaŵirikaŵiritu mtima wako udziŵa kuti nawenso unatemberera ena.”—Komano sikuti mukatsatira mfundo zabwino zimenezi ndiye kuti basi simudzavutitsidwanso kuntchito. Ngakhale mutayesetsa kwambiri, anzanu ena kuntchitoko angalimbane nanube. Ndiyeno kodi mungatani?
Funani Thandizo
Gregory anati: “Anzanga akuntchito atandinyalanyaza kwa miyezi ingapo, ndinasokonezeka maganizo kwambiri.” Monga Gregory, anthu ambiri ovutitsidwa kuntchito amasautsika maganizo m’njira zambiri. Amaipidwa nazo, amadziimba mlandu, amachita manyazi, amasoŵa pogwira, komanso amadziona ngati achabechabe. Ngakhale munthu wabwinobwino angafike potayiratu mtima chifukwa chovutitsidwa. Inde, Baibulo limanena kuti “nsautso iyalutsa wanzeru.” (Mlaliki 7:7) Choncho, kodi munthu angachitepo chiyani?
Zimene ofufuza anapeza zimasonyeza kuti ndi bwino kusalimbana ndi vutoli panokha. Kodi munthu wovutitsidwa angapeze kuti thandizo? Makampani ena aakulu akhazikitsa njira zothandizira antchito awo amene akuona kuti akuvutitsidwa. Makampani otere amadziŵa kuti kuthetsa vutoli kumapindulitsa kampani. Ofufuza ena anapeza kuti antchito amene amavutitsa anzawo amataya nthaŵi yambiri ndithu pantchito yawo pochita zimenezi. Wovutitsidwa angathe kupeza thandizo kulikonse kumene kuli njira yotere. Mlangizi wa m’kapampaniyo kapena wochoka kwina, yemwe saikira kumbuyo aliyense wa antchito osagwirizanawo, angathandize kuti antchitowo akambirane nkhaniyo n’kugwirizana za khalidwe loyenerera pantchitopo.
Palibe Njira Yothetseratu Vutoli
Komabe, dziŵani kuti palibe njira yothetseratu kuvutitsidwa kuntchito. Ngakhale amene angatsatire mfundo za m’Baibulo zimene zili m’nkhani ino angapezekebe kuti akuvutitsidwa. Otereŵa asakayike kuti Yehova Mulungu akuona kupirira kwawo ndiponso akuona kuti iwoŵa akuyesetsa kusonyeza makhalidwe a Yehova Mulungu ngakhale ali pamavuto.—2 Mbiri 16:9; Yeremiya 17:10.
Anthu ena ovutitsidwa kwambiri ndiponso mwapafupipafupi amangoyamba kufunafuna ntchito ina. Ena amasoŵa koloŵera, chifukwa cha kusoŵa kwa ntchito ndiponso chithandizo. Monika, amene tam’tchula m’nkhani yam’mbuyoyi, chinam’chitikira n’chakuti patatha nthaŵi, vuto lake linatha lokha chifukwa mmodzi wa anthu amene ankamuvutitsa anachoka pantchitopo. Motero, anthu anayamba kukhalako mwamtendere, ndipo Monika anamaliza kuphunzira ntchitoyo kenaka n’kuyamba kufuna ntchito kwina.
Peter, amene tam’tchula m’nkhani yoyamba ija, anathetsa vuto lake popuma pantchitoyo zaka zake zopumira pantchito zisakwane. Komanso, mkazi wake anali womvetsa zinthu moti anam’thandiza kwambiri panthaŵi imene anali kuvutitsidwa. Peter anati: “Iye ankadziŵa vuto limene ndinkakumana nalo ndipo ankandilimbikitsa kwambiri.” M’kati mwa mavuto awo, Monika ndi Peter analimbikitsidwa kwambiri ndi chikhulupiriro chawo monga Mboni za Yehova. Kuchita nawo utumiki wothandiza anthu kunawachititsa kuti akhalebe anthu odzipatsa ulemu, ndipo kusonkhana ndi okhulupirira anzawo kunalimbikitsa ubwenzi wawo ndi anzawo enieniŵa.
Kaya inuyo zinthu zikukuyenderani motani, yesetsani kukhala bwino ndi anzanu a kuntchito. Mukamavutitsidwa, yesetsani kutsatira malangizo a mtumwi Paulo akuti: “Musabwezere munthu aliyense choipa chosinthana ndi choipa. . . . Ngati n’kutheka, monga momwe mukhoza, khalani ndi mtendere ndi anthu onse. . . . Musagonje kwa choipa, koma ndi chabwino gonjetsani choipa.”—Aroma 12:17-21.
[Mawu Otsindika patsamba 8]
Kuchita zinthu mwaubwenzi kungathandize kuti muyambe kumasukirana
[Mawu Otsindika patsamba 9]
“Ngati n’kutheka, monga momwe mukhoza, khalani ndi mtendere ndi anthu onse.”—AROMA 12:18
[Chithunzi pamasamba 8, 9]
Thetsani mwamsanga kusamvana kulikonse pakati pa inuyo ndi munthu wina