Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Dziko Lopanda Matenda

Dziko Lopanda Matenda

Dziko Lopanda Matenda

“Mayiko onse ayenera kugwirizana ndi kuthandizana kuti aonetsetse kuti anthu onse azipeza chithandizo chofunika chamankhwala chifukwa chakuti anthu a m’dziko limodzi akakhala athanzi zimakhudza ndi kuthandiza mwachindunji mayiko ena onse.”—Chikalata Chotchedwa ALMA-ATA DECLARATION, SEPTEMBER 12, 1978

ZAKA 25 zapitazo, anthu ena ankaganiza kuti kuonetsetsa kuti munthu aliyense padziko lapansi azipeza chithandizo chofunika chamankhwala n’cholinga chotheka kukwanitsa. Nthumwi za ku msonkhano wotchedwa International Conference on Primary Health Care, umene unachitikira ku Alma-Ata, m’dziko limene panopa limatchedwa Kazakhstan, zinagwirizana kuti ziyesetsa kupatsa anthu onse katemera wa matenda akuluakulu opatsirana podzafika chaka cha 2000. Nthumwizo zinakhulupiriranso kuti podzafika chaka cha 2000, anthu onse padziko lapansi adzakhala aukhondo ndiponso adzakhala ndi madzi akumwa abwino. Mayiko onse amene ali m’bungwe la World Health Organization (WHO) anasaina chikalata chimenecho.

Cholinga chimenecho chinali chotamandika ndithu, koma zotsatirapo zake zakhala zokhumudwitsa. Si anthu onse amene akupeza chithandizo chofunika chamankhwala padziko lapansi, ndipo matenda opatsirana akuopsezabe miyoyo ya anthu mabiliyoni ambiri padziko lapansi. Chinanso, matenda akupha ameneŵa nthaŵi zambiri amapha ana komanso akuluakulu amene afika pamsinkhu woti angathe kugwira bwino ntchito.

Ngakhale matenda atatu oopsa a Edzi, TB, ndi malungo sanachititse mayiko “kugwirizana ndi kuthandizana.” Bungwe longopangidwa kumene lotchedwa Thumba Lapadziko Lonse Lolimbana ndi Edzi, TB ndi Malungo linapempha maboma kuti apereke madola 13 biliyoni oti athandize kuthetsa matenda ameneŵa. Koma pofika m’chilimwe cha 2002, anapereka madola ongopitirira pang’ono 2 biliyoni, pamene m’chaka chomwecho, ndalama zimene anawonongera pa zinthu zokhudzana ndi nkhondo zinakwana pafupifupi madola 700 biliyoni! N’zomvetsa chisoni kuti m’dziko lamasiku ano logaŵanikali, n’zinthu zoopsa zochepa chabe zimene zingathe kugwirizanitsa mayiko onse kuti achite zinthu zothandiza aliyense.

Ngakhale kuti amafunitsitsadi kuthandiza, mabungwe azaumoyo amakumana ndi zolepheretsa zambiri pankhondo yolimbana ndi matenda opatsirana. Nthaŵi zina maboma sapereka ndalama zimene zikufunika. Tizilombo toyambitsa matenda tayamba kusamva mankhwala ambiri, ndipo anthu nthaŵi zina amaumirira khalidwe limene limaika moyo wawo pachiswe. Kuwonjezera apo, mavuto aakulu amene ali kuderako, monga umphaŵi, nkhondo, ndi njala amathandizira kuti tizilombo toyambitsa matenda tithe kudwalitsa anthu mamiliyoni ambiri.

Mulungu Amafuna Kuti Tikhale ndi Thanzi Labwino

Njira yothetsera matenda ilipo. Tili ndi umboni woonekeratu wosonyeza kuti Yehova Mulungu amafunitsitsa kuti anthu akhale ndi thanzi labwino. Mphamvu ya thupi lathu yotiteteza ku matenda ndi umboni wabwino kwambiri wa zimenezi. Malamulo ambiri amene Yehova anapatsa Aisrayeli akale anasonyeza kuti iye anafunitsitsa kuti awateteze ku matenda opatsirana. *

Yesu Kristu, amene amasonyeza khalidwe lofanana ndi la Atate wake wakumwamba, nayenso amamvera chisoni anthu odwala. Uthenga Wabwino wa Marko umafotokoza zimene zinachitika pamene Yesu anakumana ndi mwamuna wina wakhate. “Ngati mufuna mukhoza kundikonza,” anatero wakhateyo. Yesu anadzazidwa ndi chifundo pamene anazindikira ululu umene mwamunayo anali kuvutika nawo. Yesu anayankha kuti: “Ndifuna; khala wokonzedwa.”—Marko 1:40, 41.

Yesu sanangochiritsa modabwitsa anthu ochepa okha. Wolemba Uthenga Wabwino Mateyu analemba kuti Yesu ‘anayendayenda m’Galileya monse, analikuphunzitsa . . . nalalikira uthenga wabwino wa Ufumu, nachiritsa nthenda zonse ndi kudwala konse mwa anthu.’ (Mateyu 4:23) Kuchiritsa kwake sikunangothandiza anthu odwala a ku Yudeya ndi Galileya okha basi. Kuchiritsa kumeneko kumatisonyeza mmene matenda onse adzathere, Ufumu wa Mulungu umene Yesu analalikira ukadzayamba kulamulira anthu mosatsutsidwa ndi aliyense.

N’zotheka Anthu Onse Padziko Lapansi Kukhala ndi Thanzi Labwino

Baibulo limatitsimikizira kuti n’zotheka anthu onse padziko lapansi kukhala ndi thanzi labwino. Mtumwi Yohane anaoneratu nthaŵi imene ‘chihema cha Mulungu chidzakhala mwa anthu.’ Chifukwa chakuti Mulungu adzachita zimenezi, “sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.” Kodi zimenezo zikumveka ngati nkhambakamwa chabe? M’vesi lotsatira, Mulungu mwiniwakeyo ananena kuti: “Mawu aŵa ali okhulupirika ndi oona.”—Chivumbulutso 21:3-5.

Komabe, kutha kwa matenda kudzafuna kuti umphaŵi, njala, ndi nkhondo, nazonso ziyambe zatha, chifukwa masoka ameneŵa ndi tizilombo toyambitsa matenda opatsirana zimayendera limodzi. Choncho, Yehova wasiya ntchito imeneyi m’manja mwa Ufumu wake, boma lakumwamba lolamulidwa ndi Kristu. Poyankha mapemphero a anthu ambiri ochokera pansi pa mtima, boma limenelo lidzabwera, ndipo lidzaonetsetsa kuti kufuna kwa Mulungu kuchitike padziko lapansi.—Mateyu 6:9, 10.

Kodi tingayembekezere kuti Ufumu wa Mulungu udzabwera liti? Poyankha funso limenelo, Yesu ananeneratu kuti anthu a padziko lapansi adzaona zinthu zofunika kwambiri zikuchitika zimene zidzakhale chizindikiro chosonyeza kuti Ufumuwo watsala pang’ono kuchitapo kanthu. Iye anati chimodzi mwa zizindikiro zimenezi chidzakhala kugwa kwa “miliri m’malo akutiakuti.” (Luka 21:10, 11; Mateyu 24:3, 7) Liwu lachigiriki limene analimasulira kuti “miliri” limatanthauza “nthenda iliyonse yakupha yopatsirana.” M’zaka za m’ma 1900 miliri yoipa kwambiri inagwadi m’madera ambiri, ngakhale kuti sayansi ya zamankhwala yapita patsogolo.—Onani bokosi lakuti “Anthu Omwalira ndi Miliri Chiyambire 1914.”

Ulosi umene uli m’buku la Chivumbulutso, umene umafanana ndi mawu a Yesu opezeka m’Mauthenga Abwino, umasonyeza anthu angapo okwera akavalo ali ndi Yesu Kristu pamene akuyamba kulamulira kumwamba. Munthu wachinayi anakwera “kavalo wotumbuluka,” ndipo anasiya “imfa” m’mbuyo mwake. (Chivumbulutso 6:2, 4, 5, 8) Tikaona anthu amene afa ndi matenda ena akuluakulu opatsirana chiyambire 1914 tingatsimikizedi kuti wokwera pakavalo wophiphiritsira ameneyu wakweradi kavaloyo. Kuvutika ndi “imfa” padziko lonse ndi umboni winanso wosonyeza kuti Ufumu wa Mulungu uli pafupi kubwera. *Marko 13:29.

Ngakhale kuti sayansi ya zamankhwala yachepetsa kufalikira kwa matenda opatsirana kwa zaka makumi angapo, pali matenda atsopano amene ayamba kutivutitsa. Mwachionekere, tikufunikira mphamvu zoposa za anthu kuti tithetseretu vuto limeneli. Mlengi wathu akulonjeza kuti adzachita zimenezo. Mneneri Yesaya akutilonjeza kuti mu Ufumu wa Mulungu, “wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.” Kuwonjezera apo, ‘[Mulungu] adzameza imfa ku nthaŵi yonse; ndipo Ambuye Mulungu adzapukuta misozi pa nkhope zonse.’ (Yesaya 25:8; 33:22, 24) Tsiku limenelo likadzafika, matenda adzagonjeratu mpaka kalekale.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 8 Chilamulo cha Mose chinali ndi malangizo okhudza katayidwe ka zonyansa, ukhondo, ndi kuika odwala kwaokha. Dr. H. O. Philips anafotokoza kuti “nkhani zokhudza kubereka, kutulukira matenda, kuchiza matenda, ndiponso khalidwe loteteza ku matenda zimene zili m’Baibulo n’zotsogola ndi zodalirika kwambiri kuposa zimene ankaphunzitsa Hippocrates.”

^ ndime 15 Kuti muone umboni wina wosonyeza kuti Ufumu wa Mulungu uli pafupi kubwera, onani chaputala 11 cha buku lakuti Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Bokosi patsamba 28]

Anthu Omwalira ndi Miliri Chiyambire 1914

Ziŵerengero zili m’munsizi n’zongoyerekezera. Komabe, zikusonyeza mmene miliri yavutitsira anthu chiyambire 1914.

Nthomba (pakati pa 300 miliyoni ndi 500 miliyoni) Palibe mankhwala ochiza nthomba amene anakonzedwapo. Katemera wapadziko lonse ndi amene pomalizira pake anathetsa nthendayi pofika mu 1980.

TB (pakati pa 100 miliyoni ndi 150 miliyoni) TB tsopano imapha anthu pafupifupi 2 miliyoni chaka chilichonse, ndipo pafupifupi munthu mmodzi mwa anthu atatu alionse ali ndi kachilombo koyambitsa TB m’thupi mwake.

Malungo (pakati pa 80 miliyoni ndi 120 miliyoni) M’zaka zoyambirira za m’ma 1900, anthu ofa ndi malungo anali pakati pa 2 miliyoni chaka chilichonse. Kum’mwera kwa Sahara ku Africa kuno n’kumene anthu amafa kwambiri ndi malungo, ndipo kudera limeneli malungo akuphabe anthu opitirira wani miliyoni chaka chilichonse.

Fuluwenza ya ku Spain (pakati pa 20 miliyoni ndi 30 miliyoni) Olemba mbiri ena akuganiza kuti anthu amene anafa ndi ambiri kuposa pamenepa. Mliri wakupha umenewu unavutitsa anthu padziko lonse mu 1918 ndi 1919, nkhondo yoyamba yapadziko lonse itangotha kumene. Buku lakuti Man and Microbes linati: “Ngakhale mliri wa makoswe sunaphe anthu ambiri choncho m’kanthaŵi kochepa kotero.”

Nthenda yofanana ndi tayifodi (pafupifupi 20 miliyoni) Miliri ya nthenda imeneyi nthaŵi zambiri inkagwa panthaŵi yankhondo, ndipo panthaŵi ya nkhondo yoyamba yapadziko lonse mliri wa nthenda imeneyi unavutitsa anthu m’mayiko a kum’maŵa kwa Ulaya.

Edzi (kupitirira 20 miliyoni) Mliri wamakonowu tsopano ukupha anthu 3 miliyoni chaka chilichonse. Ziwerengero zoyerekezera za bungwe la United Nations loona za Edzi zikusonyeza kuti “ngati sipakhala kuyesetsa kwakukulu kofuna kupeŵa ndi kuchiza nthendayi, anthu 68 miliyoni adzafa . . . m’zaka za pakati pa 2000 ndi 2020.”

[Zithunzi patsamba 27]

Mu Ufumu wa Mulungu, matenda ngati aŵa sadzaopsezanso anthu

Edzi

Malungo

TB

[Mawu a Chithunzi]

AIDS: CDC; malaria: CDC/Dr. Melvin; TB: © 2003 Dennis Kunkel Microscopy, Inc.

[Chithunzi patsamba 29]

Yesu anachiritsa nthenda za mitundu yonse