Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Kuda Nkhaŵa N’Kupanda Chikhulupiriro?

Kodi Kuda Nkhaŵa N’Kupanda Chikhulupiriro?

Lingaliro la Baibulo

Kodi Kuda Nkhaŵa N’Kupanda Chikhulupiriro?

“KUDA NKHAŴA N’KOLETSEDWA.” Pansi pa mutu umenewu, munthu wina amene anali mbusa kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1900 analemba kuti kuda nkhaŵa chifukwa cha zinthu zosoŵeka pamoyo n’kulakwa komanso ndi “tchimo lalikulu.” Chaposachedwapa, munthu wina amene anali kuthirirapo ndemanga pa nkhani yokhudza kuthana ndi nkhaŵa analemba kuti, “Kuda nkhaŵa kumasonyeza kuti sitikhulupirira Mulungu.”

M’nkhani ziŵiri zonsezi, olembawo anaganiza chonchi chifukwa cha Ulaliki wa Yesu wa pa Phiri, pamene ananena kuti: “Musadere nkhaŵa.” (Mateyu 6:25) Popeza anthu ambiri amada nkhaŵa masiku ano, tingafunse kuti: Kodi Mkristu ayenera kuganiza kuti akulakwa chifukwa akuda nkhaŵa? Kodi kuda nkhaŵa n’kupanda chikhulupiriro?

Mulungu Amamvetsa Kulephera Kwathu

Baibulo siliphunzitsa kuti kupanda chikhulupiriro n’kumene kumachititsa kuda nkhaŵa kwa mtundu wina uliwonse. Popeza tikukhala mu “nthaŵi zoŵaŵitsa,” n’zosatheka kukhaliratu osada nkhaŵa. (2 Timoteo 3:1) Akristu okhulupirika amalimbana ndi nkhaŵa za tsiku ndi tsiku zobwera chifukwa cha kudwala, kukalamba, mavuto a zachuma, mavuto a m’banja, upandu, ndi mavuto ena. Ngakhale mu nthaŵi zakale, atumiki a Mulungu ankakhalapo ndi mantha nthaŵi zina ndiponso ankada nkhaŵa.

Taganizirani nkhani ya m’Baibulo ya Loti. Mulungu anamuuza kuti athaŵire kumapiri kuti apulumuke mizinda ya Sodomu ndi Gomora ikamawonongedwa. Koma Loti anali ndi nkhaŵa. Iye anati: “Iyayitu, mfumu.” Mwamantha, iye anapitiriza kunena kuti: “Ine sindikhoza kuthaŵira kuphiri kuti chingandipeze ine choipacho ndingafe.” N’chifukwa chiyani Loti anaopa kupita kumapiri? Baibulo silitiuza chifukwa chake. Kaya chifukwa chake chinali chotani, Loti anali ndi mantha ndithu. Kodi Mulungu anachitapo chiyani? Kodi Loti analangidwa chifukwa chosakhulupirira Mulungu? Ayi. M’malo momulanga, Yehova anamuganizira, ndipo analola kuti Loti athaŵire kumzinda wina wapafupi.—Genesis 19:18-22.

M’Baibulo muli zitsanzo zina za olambira Mulungu okhulupirika amene anali ndi nkhaŵa yaikulu nthaŵi zina. Mneneri Eliya anachita mantha ndipo anathaŵa atamva kuti akufuna kumupha. (1 Mafumu 19:1-4) Mose, Hana, Davide, Habakuku, Paulo, ndi amuna ndi akazi ena amene anali ndi chikhulupiriro cholimba nawonso anafotokoza za nkhaŵa zawo. (Eksodo 4:10; 1 Samueli 1:6; Salmo 55:5; Habakuku 1:2, 3; 2 Akorinto 11:28) Komabe, Mulungu anawamvera chifundo ndipo anapitiriza kuwagwiritsa ntchito mu utumiki wake, ndipo mwa kuchita zimenezi Mulungu anasonyeza kuti anthu opanda ungwiro amawamvetsadi bwino.

“Tchimoli Limangotizinga”

Koma kuda nkhaŵa kosalekeza kungafooketse chikhulupiriro chathu n’kutichititsa kusiya kukhulupirira Mulungu. Mtumwi Paulo anafotokoza kuti kupanda chikhulupiriro ndilo “tchimoli limangotizinga.” (Ahebri 12:1) Mwa kuphatikizapo iye mwini, mtumwi Paulo mwachionekere anali kuvomereza vuto limene anali nalo loti nthaŵi zina ankakhala ndi chikhulupiriro chofooka kwa kanthaŵi.

Mwina zimenezi n’zimene zinachitikira Zekariya pamene sanakhulupirire mngelo amene anamuuza kuti mkazi wake adzakhala ndi pakati. Panthaŵi ina atumwi a Yesu analephera kuchiza munthu chifukwa chokhala ndi ‘chikhulupiriro chaching’ono.’ Komabe, anthu ameneŵa anakhalabe oyanjidwa ndi Mulungu.—Mateyu 17:18-20; Luka 1:18, 20, 67; Yohane 17:26.

Mosiyana ndi zimenezi, Baibulo lilinso ndi zitsanzo za anthu amene anasiya kukhulupirira Mulungu ndipo anakhala ndi zotsatirapo zoipa kwambiri. Mwachitsanzo, Aisrayeli ambiri amene anachoka ku Igupto sanaloledwe kuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa chifukwa cha kupanda chikhulupiriro. Panthaŵi inayake anafika mpaka polankhula motsutsana ndi Mulungu mwachindunji, mwa kunena kuti: “Mwatikwezeranji kutichotsa ku Aigupto kuti tifere m’chipululu? Pakuti mkate ndi madzi palibe.” Posonyeza mkwiyo wake, Mulungu anatumiza njoka zaululu kuti ziwalange.—Numeri 21:5, 6.

Anthu okhala m’tawuni ya kwawo kwa Yesu ya Nazarete anataya mwayi wapadera wotha kuona zodabwitsa zina zikuchitika m’dera lakwawo chifukwa chopanda chikhulupiriro. Kuwonjezera pamenepo, mbadwo woipa wa nthaŵi imeneyo unadzudzulidwa mwamphamvu ndi Yesu chifukwa cha kupanda chikhulupiriro. (Mateyu 13:58; 17:17; Ahebri 3:19) Mogwirizana ndi zimenezo, mtumwi Paulo anachenjeza kuti: “Tapenyani, abale, kuti kapena ukakhale mwa wina wa inu mtima woipa wosakhulupirira, wakulekana ndi Mulungu wamoyo.”—Ahebri 3:12.

N’zoona kuti panthaŵi zochepa kwambiri munthu angakhale wopanda chikhulupiriro chifukwa cha mtima woipa. Koma zimenezi si zimene zinachitikira Zekariya ndi atumwi a Yesu m’zitsanzo zimene tazitchula kale zija. Anasonyeza kupanda chikhulupiriro chifukwa anafooka kwa kanthaŵi kochepa. Koma tikayang’ana moyo wawo wonse tingaone kuti anali “oyera mtima.”—Mateyu 5:8.

Mulungu Amadziŵa Zosoŵa Zathu

Malemba amatithandiza kusiyanitsa kuda nkhaŵa wamba ndi tchimo la kupanda chikhulupiriro. Nkhaŵa ya tsiku ndi tsiku, ngakhale kulephera kusonyeza chikhulupiriro kwa kanthaŵi chifukwa cha kufooka kwa munthu, si zofanana ndi kupandiratu chikhulupiriro mwa Mulungu kumene kumachokera mu mtima woipa ndi wouma. Choncho Akristu sayenera kuganiza kuti akulakwa chifukwa amada nkhaŵa nthaŵi ndi nthaŵi.

Komabe, tiyenera kusamala kuti kuda nkhaŵa kusakule n’kufika polamulira miyoyo yathu. Choncho, Yesu ananena zanzeru pamene anati: “Musadere nkhaŵa, ndi kuti, Tidzadya chiyani? kapena, Tidzamwa chiyani? kapena, Tidzavala chiyani?” Kenaka ananena mawu olimbikitsa akuti: “Pakuti Atate wanu wa Kumwamba adziŵa kuti musoŵa zonse zimenezo. Koma muthange mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzawonjezedwa kwa inu.”—Mateyu 6:25-33.

[Chithunzi patsamba 16]

Mtumwi Paulo ankada nkhaŵa nthaŵi zina