Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuthana ndi Kusungulumwa

Kuthana ndi Kusungulumwa

Kuthana ndi Kusungulumwa

KUTHANA ndi kusungulumwa n’kovuta chifukwa chakuti munthu amakhala akuvutika kwambiri mu mtima. Kodi munthu angatani kuti athane ndi kusungulumwa? Kodi anthu ena achitapo chiyani kuti athane ndi kusungulumwa kosautsa kumeneku?

Kulimbana ndi Kusungulumwa

Helen * amakonda kukhala yekha akamaganiza mmene achitire zinthu zinazake, koma amaona kuti kusungulumwa kungakhale koopsa. Ali mwana, sankatha kulankhulana bwino ndi makolo ake. Posadziŵa chimene angachite kuti makolo akewo azimulankhula, anadzitsekera m’chipinda mwake. Iye anati: “Ndinayamba kuvutika kudya. Ndinavutika kwambiri maganizo. Mumtima mwangamu ndinkati, ‘Ndiderenji nkhaŵa ndi mavuto a makolo anga pamene iwowo sada nkhaŵa ndi mavuto anga?’ Kenaka ndinaganiza kuti ukwati ungathetse vuto langa la kusungulumwa. Ndinayamba kufuna kukwatiwa kuti ndithane ndi vuto langalo. Koma pasanapite nthaŵi yaitali ndinayamba kuganiza kuti: ‘Ndiwonongerenji moyo wa munthu wina? Choyamba, ndikonze kaye maganizo anga.’ Ndinapempha Yehova kuti andithandize, ndipo ndinamuuza nkhaŵa zanga zonse m’pemphero.

“M’Baibulo ndinapezamo mawu olimbikitsa kwambiri, monga amene ali pa Yesaya 41:10 akuti: ‘Usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; usaopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo.’ Mawu ameneŵa anandithandiza kwambiri chifukwa chakuti ndinkamva ngati ndilibe bambo. Masiku ano, ndimaŵerenga Baibulo nthaŵi zonse ndipo ndimapemphera kwa Atate wanga wakumwamba. Tsopano ndikudziŵa zochita kuti ndithane ndi kusungulumwa kwanga.”

Wokondedwa wathu akamwalira timamva chisoni, ndipo tingayambe kusungulumwa. Luisa, wa zaka 16, anafotokoza chisoni chake motere: “Bambo anga anaphedwa ndili ndi zaka zisanu. Ndinayamba kudalira agogo anga kuti anditonthoze, koma sindinaone kuti anali kundikonda. Ndili mwana, sindinakondedwe monga mmene mwana amafunikira kum’kondera. Ndili ndi zaka eyiti kapena naini, ndinafuna kudzipha katatu. Ndinaganiza kuti zimenezo zikanathandiza kwambiri banja lathu chifukwa mayi anga ankavutika kupeza chakudya cha achemwali anga atatu ndi ineyo. Ndiyeno tinayamba kucheza ndi Mboni za Yehova. Banja linalake lachinyamata linandisonyeza chidwi chochokeradi pansi pa mtima. Ankandiuza kuti, ‘Timakuona kuti ndiwe wofunika kwambiri.’ Mawu akuti ‘Ndiwe wofunika kwambiri’ anandilimbikitsa kwambiri. Nthaŵi zina ndimalephera kuuza munthu wina mmene ndikumvera, koma ndikaŵerenga nkhani za mu Nsanja ya Olonda kapena Galamukani! ndimathokoza Yehova, chifukwa kudzera m’magazini ameneŵa ndaona kuti Yehova amandikonda. Ndasintha zinthu zambiri pamoyo wanga. Masiku ano ndimatha kusekerera, ndipo ndimatha kuwafotokozera mayi anga ngati ndikumva chisoni kapena kusangalala. Nthaŵi zina ndimakumbukira zakale, koma sizindichititsa kumva ngati mmene ndinkamvera m’mbuyomo pamene ndinafuna kudzipha kapena pamene ndinasiya kulankhula ndi okondedwa anga. Nthaŵi zonse ndimakumbukira mawu amene wamasalmo Davide ananena, akuti: ‘Chifukwa cha abale anga ndi mabwenzi anga, ndidzanena tsopano, mukhale mtendere mwa inu.’”—Salmo 122:8.

Ukwati wa Martha unatha zaka 22 zapitazo, ndipo panthaŵi imeneyi analera yekha mwana wake. Iye anati: “Ndimaona kuti ndine wosafunika ndipo ndimakhala wosungulumwa ndikamaganiza kuti ndalephera kuchita chinachake.” Kodi amatani kuti athane ndi maganizo oterowo? Akufotokoza kuti: “Ndazindikira kuti njira yabwino kwambiri yolimbana ndi maganizo ameneŵa ndiyo kumuuza Yehova Mulungu nthaŵi yomweyo. Ndikamapemphera, ndimadziŵa kuti sindili ndekha. Yehova amandimvetsa bwino kwambiri kuposa mwini wakene. Ndimachita zotheka kuti ndisonyeze chidwi kwa anthu ena. Utumiki wanga wa nthaŵi zonse ndi chida champhamvu kwambiri polimbana ndi maganizo ofoola. Mukamalankhula ndi anthu ena za madalitso a Ufumu wa Mulungu n’kuzindikira kuti omvera anuwo alibiretu chiyembekezo ndipo amaona kuti mavuto awo sadzatha, mumazindikira kuti muli ndi zifukwa zabwino kwambiri zofunira kukhalabe ndi moyo ndi kupitirizabe kuyesayesa kuthana ndi mavuto anu.”

Elba wa zaka 93 amene mwana wake mmodzi yekha ndi mmishonale m’dziko lina, akutifotokozera mmene amalimbanirana ndi kusungulumwa. Iye akuti: “Mwana wanga ndi mwamuna wake atalandira kalata yowaitana ku Sukulu ya Gileadi ya Watchtower Yophunzitsa Baibulo, ndinaona kuti anali ndi chimwemwe chachikulu ndipo inenso ndinasangalala. Kenaka, atauzidwa kukatumikira kudziko lina, ndinayamba kukhala ndi maganizo odzikonda. Ndinadziŵa kuti sindikhalanso nawo pafupi, ndipo sindinasangalale. Ndinamva ngati Yefita ndi mwana wake wamkazi mmodzi yekha, amene akufotokozedwa m’buku la Oweruza chaputala 11. Ndinapemphera kwa Yehova ndikulira, kumupempha kuti andikhululukire. Ana angawo amandilembera makalata. Ndikudziŵa kuti ndi otanganidwa, koma kulikonse kumene akutumikira, amapatula nthaŵi n’kundiuza zimene akukumana nazo mu utumiki wa kumunda. Ndimaŵerenga makalata awowo nthaŵi zambirimbiri. Zimakhala ngati kuti akulankhula nane mlungu uliwonse, ndipo ndimayamikira kwambiri zimenezo. Chinanso, akulu achikristu mu mpingo wathu amasamalira anthu achikulire ndi odwalafe, ndipo amaonetsetsa kuti tili ndi njira yopitira ku misonkhano ya mpingo ndi kutisamalira m’njira zina. Ndimaona kuti abale ndi alongo anga auzimu ndi dalitso lochokera kwa Yehova.”

Inunso Mungathane ndi Kusungulumwa

Kaya ndinu wamng’ono kapena wachikulire, wosakwatira kapena wokwatira, mwana amene makolo ake alipo kapena wamasiye, ndipo kaya okondedwa anu anamwalira kapena mukuvutika ndi kusungulumwa kwa mtundu winawake, pali njira zothetsera kusungulumwa kwanuko. Jocabed, mtsikana wa zaka 18 amene bambo ake anathaŵa banja la anthu sikisi n’kukakhala ku dziko lina anati: “Muzilankhula! Ndi bwino kufotokoza zimene zikutivuta. Ngati sitichita zimenezi, palibe amene adzatimvetse.” Iye anapereka malangizo otsatiraŵa: “Lekani kuganizira kwambiri za inuyo basi. Muzifuna thandizo kwa anthu achikulire, osati achinyamata amene angakhale ndi mavuto aakulu kuposanso inuyo.” Luisa, amene tinamutchula kale uja, anati: “Kupemphera kwa Yehova kuchokera pansi pa mtima kumatithandiza kuthana ndi mavuto osoŵa nawo koloŵera.” Jorge, amene mkazi wake anamwalira, ananena zotsatirazi zokhudza mmene amalimbanirana ndi kusungulumwa: “M’pofunika khama. Kusonyeza chidwi kwa ena kumandithandiza kwambiri. ‘Kuchitira ena chifundo’ pocheza ndi anthu kungachititse macheza athu kukhala atanthauzo ndipo kungatithandize kuzindikira makhalidwe abwino a anthu ena.”—1 Petro 3:8.

Munthu angachite zambiri kuti athane ndi kusungulumwa. Koma kodi nthaŵi idzafika imene sipadzakhalanso kusungulumwa? Ngati idzafike, kodi zidzachitika bwanji? Nkhani yotsatira iyankha mafunso ameneŵa.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Mayina ena asinthidwa.

[Mawu Otsindika patsamba 8]

“Kupemphera kwa Yehova kuchokera pansi pa mtima kumatithandiza kuthana ndi mavuto osoŵa nawo koloŵera.”—Anatero Luisa

[Bokosi/Zithunzi patsamba 7]

Zimene Mungachite Kuti Muthane ndi Kusungulumwa

▪ Kumbukirani kuti zinthu zikhoza kusintha, kuti sizidzakhala chonchi mpaka kalekale ndiponso kuti pali anthu enanso ambiri amene ali osungulumwa.

▪ Musayembekezere kuchita zinthu zimene simungakwanitse.

▪ Muzikhutira ndi mmene mulili.

▪ Muzidya bwino ndi kuchita maseŵera olimbitsa thupi, ndipo muzigona mokwanira.

▪ Gwiritsani ntchito nthaŵi imene muli nokha kuchita zinthu zothandiza ndi kuphunzira luso latsopano.

▪ Samalani kuti musaweruze anthu amene mwangokumana nawo kumene poganizira zimene zinakuchitikirani inuyo m’mbuyomu.

▪ Muziona kuti anzanu ndi ofunika kwambiri ndiponso aliyense wa iwo ali ndi makhalidwe enaake abwino. Yesetsani kukhala ndi anzanu abwino angapo. Funsani nzeru kwa anthu achikulire odziŵa zambiri.

▪ Chitirani ena kanthu kenakake, monga kuwasekerera, kuwalankhula mawu okoma mtima, kapena kuwasonyeza mfundo inayake ya m’Baibulo. Kudziŵa kuti anthu ena akudalira inuyo kumathetsa kusungulumwa.

▪ Pewani kuganizira kwambiri anthu a m’mafilimu, a pa TV, a pa Intaneti, kapena a m’mabuku, kumaganiza kuti mungachite nawo chibwenzi.

▪ Ngati muli pabanja, musayembekezere kuti mwamuna kapena mkazi wanu adzachita zonse zimene mtima wanu umafuna. Phunzirani kugonjerana ndi kuthandizana.

▪ Phunzirani kulankhula ndi anthu ena ndi kumvetsera bwino. Muziganizira kwambiri ena ndi zimene amakonda. Muzimvera ena chifundo.

▪ Vomerezani kuti ndinu osungulumwa, ndipo lankhulani ndi mnzanu wachikulire amene mumamukhulupirira. Musamangovutika nokhanokha.

▪ Pewani kumwa mowa kwambiri, kapena musamamwe n’komwe. Mowa suthetsa mavuto. Pakapita nthaŵi mavutowo amabweranso.

▪ Pewani kunyada. Khululukirani anthu amene akulakwirani ndipo yanjanani nawonso. Muzitha kukhulupirira anthu ena.

[Chithunzi patsamba 6]

Kodi munthu angachite chiyani kuti athane ndi kusungulumwa?