Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Anthu Ambiri Amadwala Chimfine Chimene Chimabwera Akakhala Pafupi ndi Mungu?

N’chifukwa Chiyani Anthu Ambiri Amadwala Chimfine Chimene Chimabwera Akakhala Pafupi ndi Mungu?

N’chifukwa Chiyani Anthu Ambiri Amadwala Chimfine Chimene Chimabwera Akakhala Pafupi ndi Mungu?

Yolembedwa ndi wolemba Galamukani! ku Spain

MASO anu akuyabwa ndiponso akutuluka misozi, mukuyetsemula tsiku lonse, mamina akungotuluka, ndipo mukuvutika kupuma. N’chiyani chikuchitika? Mwina mukudwala chimfine. Koma ngati zimenezi zimakuchitikirani mukakhala pafupi ndi mungu, n’zotheka kuti muli ndi chimfine chimene chimabwera munthu akakhala pafupi ndi mungu. Ngati zili choncho, simuli nokha. Anthu amene amawapeza ndi chimfine chobwera akakhala pafupi ndi mungu akuchulukirachulukira chaka chilichonse.

“Chimfine chimene chimabwera munthu akakhala pafupi ndi mungu chimayamba thupi lathu likamakana monyanyira chinthu chimene likuchiona ngati n’chodwalitsa,” inatero magazini yakuti Mujer de Hoy. “Mphamvu yoteteza thupi ku matenda ya anthu amene thupi lawo siligwirizana ndi zinthu zina imakana zinthu zonse zimene imaziona ngati zachilendo, kuphatikizapo mungu, ngakhale kuti zimenezi si zodwalitsa.” Ndipo mphamvu yoteteza thupi ku matenda ikamakana zinthu zinazake monyanyira m’njira yotereyi, imayambitsa zizindikiro zosoŵetsa mtendere tazifotokoza koyambirira zija.

Mu 1819, dokotala wa ku Mangalande wotchedwa John Bostock anafotokoza zizindikiro za chimfine chimene chimabwera munthu akakhala pafupi ndi mungu. Anali woyamba kuchita zimenezi. Bostock anafotokoza zizindikiro zosoŵetsa mtendere zimene zinkamuchitikira iyeyo panthaŵi zinazake pachaka. Ankakhulupirira kuti zizindikirozo zinkayamba chifukwa cha udzu umene angoumweta kumene. Kenaka zinatulukiridwa kuti zinthu zimene thupi siligwirizana nazozo ndi mitundu yosiyanasiyana ya mungu. Kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1800, Bostock anapeza anthu ochepa chabe amene ankadwala nthendayi ku England konse.

Koma kodi n’chifukwa chiyani masiku ano kuli anthu ambiri amene amadwala chimfine akakhala pafupi ndi mungu? Dr. Javier Subiza, mkulu wa malo ofufuza za mphumu ndi zinthu zimene matupi a anthu ena amadana nazo otchedwa Center for Asthma and Allergies ku Madrid, Spain, anatchula zifukwa ziŵiri zimene ochita kafukufuku akupenda. Ofufuza ena amati chimene chimachititsa zimenezi ndi mainjini oyendera dizilo. Amakhulupirira kuti dizilo akamagwira ntchito pamatuluka tinthu tinatake ting’onoting’ono timene timakadzutsa mphamvu ya thupi yokana zinthu zachilendo kuti iyambe kugwira ntchito. Malinga ndi zimene ananena Dr. Juan Kothny Pommer, amene amafufuza za zinthu zimene thupi siligwirizana nazo, “m’mayiko otukuka, anthu 20 mwa anthu 100 alionse amadwala chimfine akakhala pafupi ndi mungu, ndipo odwala ambiri amakhala m’mizinda.”

Ofufuza ena amati chimene chimayambitsa vutoli ndi ukhondo wopambanitsa. ‘Timabadwira m’chipinda chaukhondo kwambiri chochitira opaleshoni, timadya zakudya zopanda tizilombo toyambitsa matenda, timalandira katemera wotiteteza ku matenda ambiri, ndipo timamwa mankhwala tikangoyamba kudwala. Choncho kuyambira tili ana, mphamvu yathupi lathu yotiteteza ku matenda imaphunzitsidwa kukana monyanyira zinthu zilizonse zachilendo,’ anafotokoza motero Dr. Subiza.

Ngati mumadwala chifukwa cha kukana zinthu monyanyira kumeneku kwa mphamvu yoteteza thupi lanu ku matenda, musataye mtima. Vutoli akalitulukira n’kukupatsani mankhwala oyenera, n’zotheka kukuthandizani kuti musamadwaledwale ndiponso kuti mukadwala zizindikiro zosoŵetsa mtendere zija zisamakhale zamphamvu kwambiri.