Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Nthaŵi Imene Sipadzakhalanso Munthu Wosungulumwa

Nthaŵi Imene Sipadzakhalanso Munthu Wosungulumwa

Nthaŵi Imene Sipadzakhalanso Munthu Wosungulumwa

NKHANI ya pa Genesis 2:18 imati munthu woyamba atalengedwa, “Yehova Mulungu ndipo anati, si kwabwino kuti munthu akhale yekha; ndidzam’pangira wom’thangatira iye.” Anthu analengedwa kuti azikhala ndi anthu ena ndipo azidalira anthu enawo.

Bwenzi labwino koposa limene tingakhale nalo ndilo Yehova Mulungu. Mtumwi Paulo anavomereza kuti Yehova ndi “Atate wa zifundo ndi Mulungu wa chitonthozo chonse, wotitonthoza ife m’nsautso yathu yonse.” (2 Akorinto 1:3, 4) Yehova amamva chisoni mtumiki wake aliyense akamavutika. Iye ndi Mulungu wachifundo ndipo “adziŵa mapangidwe athu; akumbukira kuti ife ndife fumbi.” (Salmo 103:14) Kodi simukopeka ndi Yehova Mulungu ndi kumuthokoza chifukwa chakuti amatiganizira mwachikondi, mokoma mtima, ndiponso amatimvetsa?

Yehova Amathandiza Anthu Osungulumwa

Kale, atumiki a Mulungu ambiri anakumana ndi zochitika zimene anasungulumwa nazo. Yehova anathandiza ndi kutonthoza atumiki ake ameneŵa. Mwachitsanzo, taganizirani za Yeremiya, amene anauzidwa kuti akhale mneneri akadali mnyamata. Mwa anthu 40 amene analemba Malemba, Yeremiya mwina ndi amene ananena zambiri zokhudza mmene anali kumvera. Atapatsidwa ntchito yake yoyamba ndi Mulungu, anachita mantha ndipo anadziona kuti sanali woyenera kuchita ntchitoyo. (Yeremiya 1:6) Kuti aikwanitse, anayenera kudalira Yehova kotheratu. Zoonadi, Yehova anali naye “ngati wamphamvu.”—Yeremiya 1:18, 19; 20:11.

Zaka 300 m’mbuyomo nthaŵi ya Yeremiya isanafike, Mfumukazi Yezebeli atamva kuti aneneri ake olambira Baala aphedwa, analumbira kuti apha Eliya. Eliya anathaŵa n’kuyenda ulendo wa makilomita 450 kupita ku Horebe m’dera la Sinai. Kumeneko analoŵa m’phanga kuti agone ndipo Yehova Mulungu anamufunsa kuti: “Uchitanji pano, Eliya?” Eliya anafotokoza kuti ankaona kuti mu Israyeli yense, wolambira Yehova amene anatsala anali iyeyo basi, mneneri amene anali ndi changu potumikira Mulungu. Yehova anamulimbikitsa kuti sanali yekha. Yehova anali naye, ndipo Aisrayeli anzake ena 7,000 analinso naye, ngakhale kuti iye sanali kudziŵa zimenezi. Yehova anatonthoza Eliya n’kulimbitsa chikhulupiriro chake. Anakhudza mtima wa Eliya, ndipo analimbikitsa mneneriyo kuti asasiye ntchito yake. (1 Mafumu 19:4, 9-12, 15-18) Ngati tasungulumwa kapena tayamba kudziona kuti ndife osafunika monga mmene anachitira Eliya, nafenso tingapemphere kwa Yehova kuti atilimbikitse. Chinanso, mwa kugwiritsa ntchito luso la kuzindikira, akulu achikristu angalankhule molimbikitsa anthu okhulupirika, kuwathandiza kuti aone mbali imene ali nayo pa kukwaniritsidwa kwa zofuna za Mulungu.—1 Atesalonika 5:14.

Kuchokera ku zitsanzo zimenezi ndi zina, tingaone kuti Yehova ndi wofunitsitsa kuthandiza ndi kutonthoza mwachikondi anthu amene akusungulumwa. Indedi, “Yehova adzakhala msanje kwa iye wokhalira mphanthi. Msanje m’nyengo za nsautso.”—Salmo 9:9; 46:1; Nahumu 1:7.

Munthu Wokhudzidwa Kwambiri ndi Zinthu Ndiponso Wachifundo

Yesu Kristu ndi chitsanzo chosiririka cha munthu amene, motsanzira Yehova, sanali wouma mtima. Luka anafotokoza zimene Yesu anachita atakumana ndi anthu akupita ku manda ku Nayini. Anati: “Anthu anali kunyamula munthu wakufa, mwana wamwamuna mmodzi yekha, amake ndiye mkazi wamasiye . . . Ndipo pamene Ambuye anamuona, anagwidwa ndi chifundo chifukwa cha iye, nanena naye, Usalire. Ndipo anayandikira, nakhudza chithatha; ndipo akum’nyamulawo anaima. Ndipo Iye anati, Mnyamata iwe, ndinena ndi iwe, Tauka. Ndipo wakufayo anakhala tsonga, nayamba kulankhula. Ndipo anam’pereka kwa amake.” (Luka 7:12-15) Yesu anakhudzidwa mtima kwambiri. Anali munthu wachifundo. Tangoganizirani mmene mkazi wamasiye wosungulumwayo anasangalalira Yesu ataukitsa mwana wake! Tsopano mkaziyo sanalinso wosungulumwa.

Tingalimbikitsidwe podziŵa kuti Yesu angathe “kumva chifundo ndi zofooka zathu.” Iye amamveradi chifundo anthu olungama amene akusungulumwa. Indedi, kudzera mwa iye ‘tingalandire chifundo ndi kupeza chisomo cha kutithandiza nthaŵi yakusoŵa.’ (Ahebri 4:15, 16) Mwa kutsanzira Yesu, tingamvere chifundo anthu amene ali pachisoni, amene akuzunzidwa, kapena amene akusungulumwa. Mwa kuthandiza ena, mosakayikira tidzakhala osasungulumwa. Koma palinso njira ina imene ingatithandize kuthana ndi maganizo ofoola obwera chifukwa cha kusungulumwa.

Mawu a Yehova Angatithandize Kuthana ndi Kusungulumwa

Anthu ambiri azindikira kuti ‘ndi chitonthozo cha malembo, akhala ndi chiyembekezo.’ Mawu a Mulungu ali ndi malangizo othandiza ambiri amene angatithandize kuthana ndi kusungulumwa. (Aroma 15:4; Salmo 32:8) Mwachitsanzo, Mawu a Mulungu amatilimbikitsa kuti ‘tisadziyese koposa kumene tiyenera kudziyesa.’ (Aroma 12:3) Kuti titsatire malangizo ameneŵa, tingafunike kusintha kaganizidwe kathu. Kuzindikira zolephera zathu kudzatithandiza kusayembekezera kuchita zinthu zimene sitingathe kukwanitsa. Mawu a Mulungu amatilangizanso kuti tizikhala ndi chidwi chochokera pansi pa mtima ndi anthu ena. (Afilipi 2:4) Paja amati mnzako akakuti konzu, iwenso umamuti konzu. Mukamachitira ena zinthu zabwino, nawonso adzakuchitirani zabwino. Ubwenzi wabwino ndi ena woterewu umathandiza kuthetsa maganizo oona ngati chinachake chikusoŵeka ndipo umachititsa moyo wathu kukhala watanthauzo.

Baibulo limalimbikitsa ife monga Akristu kuti ‘tisaleke kusonkhana kwathu pamodzi.’ (Ahebri 10:24, 25) Choncho chitani zinthu zopindulitsa, monga kupezeka pa misonkhano ya Mboni za Yehova nthaŵi zonse. Mosakayikira, misonkhano yachikristu ingatithandize mwauzimu, m’maganizo, ndiponso thanzi lathu. Kulankhula ndi ena za uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu ndi njira yosangalatsa yokhalira ndi zambiri zochita. Kumathandiza maganizo athu kukhala pa zinthu zabwino, kumalimbitsa chikhulupiriro chathu, ndiponso kumateteza chiyembekezo chathu.—Aefeso 6:14-17.

Yandikirani kwa Yehova mwa pemphero. Davide anatilimbikitsa kuti: “Um’senze Yehova nkhaŵa zako, ndipo Iye adzakugwiriziza.” (Salmo 55:22) Mwa kuphunzira Mawu a Mulungu, mudzakhala osangalala. (Salmo 1:1-3) Ngati muyamba kusungulumwa, sinkhasinkhani mmene Yehova amasamalira anthu mwachikondi monga momwe Mawu ake amasonyezera. Wamasalmo analemba kuti: “Moyo wanga umamatika ndi fumbi; mundipatse moyo monga mwa mawu anu.”—Salmo 119:25.

Nthaŵi Imene Sipadzakhalanso Munthu Wonena Kuti “Ndasungulumwa”

Yehova Mulungu watilonjeza dziko latsopano lopanda kuda nkhaŵa, kukhumudwa, ndiponso kuganiza zinthu zofoola. Baibulo limati: “Adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.” (Chivumbulutso 21:4) Indedi, zina mwa zoyamba zimene zidzathe ndi zinthu zimene zimatipweteka m’thupi, m’maganizo, ndi mu mtima masiku ano.

Dziko lapansi lidzadzala ndi anthu ansangala amene adzachititsa miyoyo yathu kukhala yatanthauzo. Yehova adzatichiritsa kotheratu n’kuchotsa kusungulumwa kudzera mu Ufumu wake wakumwamba wolamulidwa ndi Yesu Kristu. Adzatipatsa zinthu zatsopano ndiponso zochititsa chidwi zoti tizichita m’dziko lapansi laparadaiso. Posachedwapa, nthaŵi idzafika imene sitidzanena kuti, “Ndasungulumwa.”

[Chithunzi pamasamba 8, 9]

Ndi thandizo la Yehova sitidzasungulumwa, ngakhale pamene tili tokhatokha

[Zithunzi patsamba 10]

Kodi nkhani za m’Baibulo zokhudza Yeremiya ndi Eliya zimatiphunzitsa chiyani?