Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Kukhala Mutu wa Banja Kumatanthauzanji?

Kodi Kukhala Mutu wa Banja Kumatanthauzanji?

Lingaliro la Baibulo

Kodi Kukhala Mutu wa Banja Kumatanthauzanji?

MALINGA ndi zimene Baibulo limanena, “mutu wa mkazi ndiye mwamuna.” (1 Akorinto 11:3; Aefeso 5:23) Koma anthu ambiri amene amanena kuti amalemekeza Baibulo amaona kuti mfundo ya umutu wa mwamuna imeneyi ndi yachikale komanso yoopsa. Mwamuna ndi mkazi wina okwatirana ananena kuti: “Chiphunzitso chakuti akazi ayenera ‘kugonjera modzichepetsa’ [kwa amuna awo], mukachitengera pa m’gong’o chingachititse kuti mwamuna akhale wankhanza, ndipo azichita zinthu zopweteka mkazi wake m’maganizo.” N’zomvetsa chisoni kuti anthu ambiri amachita nkhanza akakhala mutu wa banja. Wolemba nkhani wina anati: “M’mayiko ambiri, kumenya mkazi kumaonedwa ngati ndi zimene mwamuna ayenera kuchita, kuti ndi ufulu wa mwamuna, ndipo amakutamanda m’nyimbo, miyambi, ndi m’miyambo ya ukwati.”

Anthu ena amati mfundo ya m’Baibulo ya umutu ndi imene yachititsa kuti pakhale nkhanza zoterezi. Kodi chiphunzitso cha m’Baibulo cha umutu chimanyoza akazi ndi kulimbikitsa amuna kuchita nkhanza pabanja? Kodi kukhala mutu wa banja kumatanthauza chiyani kwenikweni? *

Kukhala Mutu Sikutanthauza Kupondereza Ena

Umutu wa m’Baibulo ndi dongosolo lachikondi ndipo sutanthauza kupondereza ena m’pang’onong’ono pomwe. Kusamvera ulamuliro umene Mulungu anakhazikitsa n’kumene kunachititsa kuti amuna azipondereza akazi, kupondereza kumene nthaŵi zambiri kumakhala kwankhanza. (Genesis 3:16) Chiyambireni zimene zinachitika m’munda wa Edene, amuna nthaŵi zambiri agwiritsa ntchito molakwika mphamvu zawo, ndipo adyera masuku pamutu anthu ena mwankhanza, kuphatikizapo akazi ndi ana.

Komabe, zimenezi sizinali mbali ya cholinga cha Mulungu. Yehova amanyansidwa ndi anthu amene amagwiritsa ntchito molakwika mphamvu zawo. Iye anakalipira amuna achiisrayeli amene ‘anachitira chosakhulupirika’ akazi awo. (Malaki 2:13-16) Kuwonjezera apo, Mulungu anati “moyo wake umuda . . . iye wakukonda chiwawa.” (Salmo 11:5) Choncho amuna amene amamenya akazi awo ndi ena onse amene amachitira anzawo nkhanza sanganene kuti Baibulo n’limene limawachititsa kuti akhale achiwawa.

Kodi Kukhala Mutu Wabwino Kumatanthauzanji?

Umutu ndi dongosolo lofunika kwambiri limene Mulungu amagwiritsa ntchito kuti m’chilengedwe chonse mukhale bata ndi mtendere. Aliyense, kupatulapo Mulungu yekha, ali ndi wina amene amayenera kumugonjera. Amuna amayenera kugonjera Kristu, ana amayenera kugonjera makolo awo, ndipo Akristu onse amayenera kugonjera boma. Ngakhale Yesu amene amagonjera Mulungu.—Aroma 13:1; 1 Akorinto 11:3; 15:28; Aefeso 6:1.

Kugonjera ulamuliro n’kofunika kuti zinthu m’dziko zikhale zolongosoka bwino ndiponso zodalirika. Mofanana ndi zimenezo, kugonjera mutu wa banja n’kofunika kuti banja likhale lolimba, losangalala, ndi lamtendere. Zimenezi sizisintha m’banja mukakhala kuti mulibe mwamuna kapena atate. M’mabanja oterowo, amayi amakhala mutu. Ngati palibe makolo onse aŵiri, mwana wamkulu kapena wachibale wina angakhale mutu wa banjalo. Mulimonse mmene zingakhalire, anthu a m’banjamo amapindula ngati alemekeza munthu amene ali ndi udindo wotsogolera banjalo.

Choncho chinthu chofunika si kukana kutsatira mfundo ya umutu, koma kuphunzira kukhala mutu wabwino ndi kuuona moyenera umutuwo. Mtumwi Paulo akulimbikitsa amuna achikristu kuti akhale mitu ya mabanja awo “monganso Kristu ndiye mutu wa Eklesia.” (Aefeso 5:21-23) Pamenepa Paulo anasonyeza kuti chitsanzo chabwino kwambiri cha mmene umutu uyenera kukhalira ndi mmene Kristu anachitira zinthu ndi Eklesia, kapena kuti mpingo. Kodi Kristu anapereka chitsanzo chotani?

Ngakhale kuti Yesu monga Mesiya ndi Mfumu yam’tsogolo anali ndi ulamuliro wochokera kwa Mulungu weniweniyo ndipo anali wanzeru kwambiri ndi wodziŵa zinthu kwambiri pamoyo kuposa ophunzira ake, iye anali wachikondi ndipo ankamvera ena chisoni. Sanali wankhanza, wosamva za ena, kapena woumirira kuti anthu azichita zinthu zovuta kukwanitsa. Sankaonetsera mphamvu zake ndipo sankakumbutsa anthu nthaŵi zonse kuti iyeyo ndiye Mwana wa Mulungu. Yesu anali wodzichepetsa, wosadzikweza. Chifukwa cha zimenezi, ‘goli lake linali lofewa, ndipo katundu wake anali wopepuka.’ (Mateyu 11:28-30) Choncho anali wochezeka ndiponso womvetsa zinthu. Ndipo Paulo anati Yesu anakonda mpingo kwambiri moti ‘anadzipereka yekha m’malo mwake.’—Aefeso 5:25.

Kodi Munthu Angatsanzire Bwanji Umutu wa Yesu?

Kodi mitu ya mabanja ingatsanzire bwanji makhalidwe a Kristu? Mutu wabwino wa banja umadera nkhaŵa umoyo wa anthu a m’banja lake ndiponso moyo wawo wauzimu. Amalolera kuwononga nthaŵi yake kuti adziŵe zosowa za banja lonselo komanso kuti adziŵedi zimene aliyense payekha m’banjalo akufunikira ndipo amakwaniritsa zosowa zimenezi. Zimene mkazi wake ndi ana ake akufuna ndiponso zimene amakonda zimabwera poyamba, zake n’kumabwera m’mbuyo. * (1 Akorinto 10:24; Afilipi 2:4) Chifukwa chotsatira mfundo ndi ziphunzitso za m’Baibulo pa moyo wake wa tsiku ndi tsiku, mkazi ndi ana ake amayamba okha kumulemekeza mwamunayo chifukwa cha khalidwe lake labwino. Motsatira umutu wake wachikondi, kuyesayesa kwa onse m’banjamo kumawathandiza kuti athane ndi mavuto alionse amene angakumane nawo. Mwa kuchita umutu wake m’njira yogwirizana ndi Malemba yoteroyo, mwamunayo amamanga banja losangalala, limene limalemekeza Mulungu.

Mutu wanzeru umakhalanso wodzichepetsa. Ngati pakufunika kutero, amapepesa mosanyinyirika, ngakhale kuti zingakhale zomuvuta kuvomereza kuti analakwa. Baibulo limati “pochuluka aphungu” pali kupulumuka. (Miyambo 24:6) Zoonadi, kudzichepetsa kudzachititsa mutu wa banja kumvetsera ndiponso kukonda kufunsa maganizo a mkazi ndi ana ake ngati pali poyenera kutero. Mwa kutsanzira Yesu, mutu wachikristu udzaonetsetsa kuti umutu wake uzisangalatsa ndi kuteteza banja lake komanso uzilemekeza Woyambitsa mabanja, Yehova Mulungu.—Aefeso 3:14, 15.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Ngakhale kuti nkhani ino ikufotokoza udindo wa mwamuna ndi atate m’banja, akazi amene akulera okha ana ndiponso ana amasiye amene ayenera kusamalira abale awo angapindule ndi mfundo zimene zaperekedwa kwa mitu ya mabanja.

^ ndime 14 Buku lakuti Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova, lili ndi mfundo zothandiza za mmene mungasamalire banja lanu mwachikondi.

[Chithunzi patsamba 26]

Mwamuna womvetsa zinthu sanyalanyaza maganizo a mkazi ndi ana ake