Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Kukhulupirira Mulungu N’kusemphana ndi Sayansi?

Kodi Kukhulupirira Mulungu N’kusemphana ndi Sayansi?

Kodi Kukhulupirira Mulungu N’kusemphana ndi Sayansi?

TIKAMAŴERENGA za sayansi, si chinthu chachilendo kukumana ndi mawu okhudzana ndi chipembedzo. Mwachitsanzo, asayansi atchedwa “akulu ansembe a akatswiri amakono a za luso,” ndipo zipinda zawo zoyezera zinthu zatchedwa “akachisi.” N’zoona kuti mawu amenewo ndi ongoyerekezera zinthu chabe. Komabe, angadzutse funso lofunika kwambiri ili lakuti: Kodi palidi kusagwirizana kwakukulu pakati pa sayansi ndi chipembedzo?

Ena angaganize kuti asayansi akamaphunzira zinthu zambiri, m’pamenenso chikhulupiriro chawo mwa Mulungu chimacheperachepera. N’zoona kuti pali asayansi ambiri amene amanyoza anthu okhulupirira Mulungu. Koma pali asayansi enanso ambiri amene amakhudzidwa kwambiri ndi umboni wosonyeza kuti zinthu m’chilengedwe chathuchi zinakonzedwa bwino ndi winawake. Asayansi ena samangodabwa ndi kukonzedwa bwino kwa zinthu, komanso amayamba kuganizira za Wokonza zinthu zimenezo.

Kusintha kwa Zinthu

Chiphunzitso cha Charles Darwin chakuti zamoyo zinakhalako mwa kuchita kusanduka kuchokera ku zinthu zina chakhalako kwa zaka 150. Anthu ena ophunzira mwina anayembekezera kuti pofika panopa, anthu amene ali mbuli ndiponso ongokhulupirira zilizonse okha ndi amene akanakhalabe akukhulupirira Mulungu. Koma zimenezo sizinachitike. Asayansi ambiri amanena poyera kuti amakhulupirira kuti kuli Mlengi. N’zoona kuti mwina sangakhulupirire Mulungu wamoyo kapena Baibulo. Komabe, amakhulupirira kuti kukonzedwa bwino kwa zinthu m’chilengedwe kumasonyeza kuti pali Wokonza Zinthu wanzeru.

Kodi asayansi ameneŵa tinganene kuti ndi opereŵera nzeru? Ponena za asayansi amene amakhulupirira kuti pali winawake wanzeru amene anakonza chilengedwe ndi zamoyo zonse, nkhani ya mu nyuzipepala yotchedwa The New York Times yofotokoza za buku linalake inati: “Ali ndi madigiri apamwamba ndipo ali ndi maudindo pa mayunivesite abwino kwambiri. Mfundo zimene amatsutsa nazo chiphunzitso cha Darwin si za m’Malemba ayi, n’zasayansi.”

Nkhani yomweyo inanenanso kuti anthu amene amakhulupirira kuti pali winawake wanzeru amene anakonza chilengedwe “sanena zinthu zoduka mutu. . . . Zimene iwo amatsutsa n’zonena kuti chiphunzitso cha Darwin kapena chonena za mmene zinthu zinayambira, kuti zinangoyamba zokha pang’onopang’ono popanda woziyambitsa, n’chokwanira kufotokoza mmene zamoyo zonse zinakhalirako. Iwo amati zinthu zamoyo zili ndi umboni wochuluka wosonyeza kuti zinakonzedwa ndi munthu wanzeru, umboni umene umasonyeza bwino kwambiri kuti pali Wokonza Zinthu Wanzeru.” *

Zodabwitsa n’zakuti maganizo oti kuli Wokonza Zinthu Wanzeru ndi ofala pakati pa asayansi. Mwachitsanzo, kafukufuku amene zotsatirapo zake anazifalitsa mu 1997 anasonyeza kuti pa asayansi 10 alionse a ku United States, 4 amakhulupirira Mulungu wamoyo. Nambala imeneyo sinasinthe chiyambire 1914, pamene kafukufuku wofanana ndi ameneyo anachitika.

Koma m’mayiko amene anthu ambiri sakhulupirira Mulungu, monga ku Ulaya, m’pomveka kuti nambala imeneyo n’njotsikirapo. Komabe, nyuzipepala ya ku Britain yotchedwa The Guardian inati “pakati pa anthu amene amachita sayansi imene amatha kuŵerenga ndi kuyeza zinthu, monga sayansi ya kapangidwe ka zinthu ndi sayansi ya nthaka, pali anthu okhulupirira Mulungu ambiri, koma pakati pa anthu amene akuchita sayansi yosatheka kuŵerengera ndi kuyeza zinthu bwinobwino, monga sayansi ya kakhalidwe ka anthu, pali anthu ochepa amene amakhulupirira Mulungu.” Nyuzipepalayo inapitiriza kunena kuti: “Ku United Kingdom kuli mabungwe monga Christians in Science [Akristu Amene Ali Asayansi].” Nyuzipepalayo inanenso kuti ku Great Britain “ana asukulu amene akuphunzira sayansi amapita kwambiri ku tchalitchi kusiyana ndi amene akuphunzira luso la mitundu ina.”

Komabe, zikuoneka kuti asayansi ambiri amanyoza mfundo yoti kuli Mlengi. Kunyoza kumeneko kumachititsa kuti asayansi anzawo nawonso azikakamizika kunena kuti sakhulupirira Mulungu. Katswiri wa sayansi ya zakuthambo Allan Sandage anati “ambiri safuna kuulula kuti amakhulupirira Mulungu.” Chifukwa chiyani? “Anzako amakutsutsa ndi kukudzudzula koopsa,” iye anatero.

Chifukwa cha zimenezi, zonena za asayansi amene amanena kuti sayansi sisemphana kwenikweni ndi kukhulupirira Mlengi sizimveka poyerekezera ndi zonena za ena amene amatsutsa zokhulupirira Mlengi. Nkhani zotsatira zifotokoza makamaka za asayansi amene amakhulupirira Mlengi ameneŵa, amene nthaŵi zambiri mawu awo amanyalanyazidwa, ndiponso zimene zimawachititsa kukhulupirira kuti kuli Mlengi. Koma kodi inuyo zikukukhudzani bwanji? Kodi sayansi ingakuthandizeni kumudziŵa Mulungu? Taŵerengani nkhani zotsatirazi.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 Anthu ophunzira kwambiri ndiponso asayansi otchuka amene anena poyera kuti amakhulupirira zoti pali “Wokonza Zinthu Wanzeru” ndi anthu monga Phillip E. Johnson amene amaphunzitsa za malamulo pa yunivesite ya ku California, Berkeley; katswiri wa zimene zimachitika m’kati mwa zinthu zamoyo Michael J. Behe, amene analemba buku lakuti Darwin’s Black Box—The Biochemical Challenge to Evolution; katswiri wa masamu William A. Dembski; katswiri wa kaganizidwe ka anthu Alvin Plantinga; akatswiri a sayansi ya kapangidwe ka zinthu John Polkinghorne ndi Freeman Dyson; katswiri wa sayansi ya zakuthambo Allan Sandage; ndi ena ambiri oti sitingakwanitse kuwatchula onse.

[Mawu a Chithunzi patsamba 11]

Stars: Courtesy of ROE/Anglo-Australian Observatory, photograph by David Malin