Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mayankho Mungawapeze Kuti?

Kodi Mayankho Mungawapeze Kuti?

Kodi Mayankho Mungawapeze Kuti?

KODI nthaŵi zina mumatopa nawo mkangano wamphamvu wosatherapo pakati pa anthu okhulupirira kuti zamoyo zinachita kusanduka kuchokera ku zinthu zina ndi okhulupirira kuti zinthu zinalengedwa? Ngati mumatero, simuli nokha.

N’zovuta chifukwa chakuti kumbali imodzi ya nkhaniyo kuli asayansi ophunzira ndi akatswiri osiyanasiyana, amene nthaŵi zambiri amagwiritsa ntchito mawu ovuta kumvetsa, ndipo amanenetsa kuti ngati munthu ali wophunzira ndiponso wanzeru, ayenera kukhulupirira kuti zamoyo zinachita kusanduka kuchokera ku zinthu zina. Kumbali inayo kuli atsogoleri achipembedzo osafuna kumva maganizo a anthu ena, amene ali ndi luso lolankhula mokopa ndipo amanena kuti ngati munthu alidi ndi chikhulupiriro chenicheni, ayenera kugwirizana ndi mmene iwowo amaphunzitsira za chilengedwe.

Maganizo onyanyira oterowo amachititsa kuti anthu ambiri oganiza bwino asakhale ndi chidwi ndi nkhani imeneyi. Pofuna kudziŵa ngati kuli Mulungu kapena ayi pamafunika zambiri osati kungotsatira mfundo za anthu a maganizo osafuna kumva za ena. Nkhani imeneyi si yongofuna kudziŵa kuti awine pa mkanganowu ndani kapena wanzeru ndani, koma ndi nkhani yokhudza moyo wanu ndi tsogolo lanu.

Vuto Limene Asayansi Ambiri Ali Nalo

Monga momwe taonera, pali asayansi odziŵika ndi ophunzira bwino ambiri amene amanena kuti umboni umene ulipo umasonyeza kuti kunja kuno kuli Wokonza Zinthu kapena Mlengi. Ena samangolekera pomwepo koma amakayikira ngati asayansi anzawo amene amatsutsa kwamtuwagalu zoti kuli Mulungu amatsatiradi mfundo zimene amayenera kuyendera pa ntchito yawo.

Mwachitsanzo, katswiri wa sayansi ya nthaka John R. Baumgardner anati: “Pokhala ndi umboni wochuluka chonchi woonetsa kuti zimenezo n’zosatheka, kodi wasayansi aliyense woona mtima anganene bwanji kuti ngozi ndi imene inachititsa kuti zinthu zikhale zovuta kumvetsa ngati mmene zamoyo zilili masiku ano? Kuchita zimenezo akudziŵa bwinobwino kuti pali umboni wosonyeza kuti n’zosatheka, kwa ine ndi kuphwanya kwambiri mfundo zimene asayansi ayenera kuyendera.”

Katswiri wotchuka wa sayansi ya kapangidwe ka zinthu Richard Feynman anatchulapo mbali ina pa nkhani ya kutsatira mfundo zimene asayansi amayenera kuyendera. Polankhulapo pa mwambo wa anthu omaliza maphunziro pa yunivesite inayake, iye ananena za “mfundo ina yapadera yofunika kuitsatira pantchito yawo.” Iye anati mfundo imeneyi imaphatikizapo “kukhala okonzeka kuvomera kuti mwina mungalakwitse.” Iye anati kuchita zimenezo “ndi udindo wathu monga asayansi kwa asayansi anzathu, ndipo ndikuganiza kuti ndi udindo wathunso kwa anthu wamba.”

Kodi ndi nthaŵi zingati zimene timamva anthu okhulupirira kuti zamoyo zinachita kusanduka kuchokera ku zinthu zina akunena kuti ‘mwina tingalakwitse’ akamanena za ziphunzitso zawo? N’zomvetsa chisoni kuti ambiri a iwo alibe kudzichepetsa koteroko. Zoona zake n’zakuti, kudzichepetsa ndi kukhulupirika kuyenera kuchititsa asayansi ambiri kuvomereza kuti sayansi, imene maphunziro ake amakhudza zinthu zimene zili m’chilengedwe chathuchi, singayankhe mafunso okhudza kukhalapo kwa Mlengi. Koma bwanji za atsogoleri achipembedzo amene amaphunzitsa za chilengedwe?

Vuto Limene Atsogoleri Achipembedzo Ambiri Ali Nalo

Kudzichepetsa ndi kukhulupirika n’zosoŵanso pakati pa atsogoleri achipembedzo. Indedi, kodi munthu amene amanena kuti Baibulo limaphunzitsa zinthu zinazake zimene siliphunzitsa ndi wokhulupirika? Kodi munthu woika maganizo ake ndi miyambo imene amaikonda patsogolo pa zimene Baibulo limanena ndi wodzichepetsa? Zimenezi n’zimene anthu ambiri ophunzitsa za chilengedwe achita.

Mwachitsanzo, ophunzitsa za chilengedwe nthaŵi zambiri amanena kuti chilengedwe chonse chinalengedwa m’masiku sikisi a maola 24 enieni zaka 6000 zapitazo. Pophunzitsa zinthu ngati zimenezi, amapereka chithunzi choipa cha Baibulo, limene limati Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi “pachiyambi,” panthaŵi inayake imene sinatchulidwe, “masiku” olenga zinthu otchulidwawo asanayambe. (Genesis 1:1) N’zochititsa chidwi kuti nkhani ya mu Genesis imasonyeza kuti mawu akuti “tsiku” amagwiritsidwa ntchito m’njira zosiyanasiyana. Pa Genesis 2:4, nthaŵi yonse ya masiku sikisi ofotokozedwa m’chaputala 1 anaitcha kuti tsiku limodzi. Choncho, ameneŵa sanali masiku enieni okhala ndi maola 24, koma anali nyengo zazitali. Zikuoneka kuti iliyonse ya nyengo zimenezi inkakhala ya zaka masauzande ambiri.

Nthaŵi zambiri atsogoleri achipembedzo amaphunzitsanso zinthu zolakwa akamanena za chikhulupiriro. Ena amanena kuti chikhulupiriro chimatanthauza kukhulupirira kwambiri chinthu chinachake popanda umboni uliwonse. Kwa anthu ambiri oganiza bwino, kumeneko kumaoneka ngati kupusitsidwa maganizo. Baibulo limafotokoza chikhulupiriro mosiyana kwambiri. Limati: “Chikhulupiriro ndicho chikhazikitso [“chiyembekezo chotsimikizika,” NW] cha zinthu zoyembekezeka, chiyesero cha [“umboni wooneka wa,” NW] zinthu zosapenyeka.” (Ahebri 11:1) Choncho chikhulupiriro chenicheni sichifanana ndi kupusitsidwa maganizo. Chimazikidwa pa umboni weniweni wotsimikizika.

Choncho, kodi chikhulupiriro mwa Mulungu n’chozikidwa pa umboni wotani? Pali umboni wa mitundu iŵiri, ndipo mtundu uliwonse ndi wodalirika.

Kupenda Bwinobwino Umboniwo

Mtumwi Paulo ataona chilengedwe zinamukhudza mtima kwambiri ndipo, ponena za Mulungu, iye analemba kuti: “Zaoneka bwino zosaoneka zake ndizo mphamvu yake yosatha ndi umulungu wake; popeza zazindikirika ndi zinthu zolengedwa.” (Aroma 1:20) Kwa zaka zambiri, amuna ndi akazi anzeru atha kuona umboni wakuti kuli Mulungu m’chilengedwe.

Monga momwe taonera, sayansi ingathe kukhala chida chothandiza kwambiri kuti munthu adziŵe kuti kuli Mulungu. Tikamaphunzira zambiri zosonyeza kuti zinthu m’chilengedwe n’zovuta kumvetsa ndiponso n’zolongosoka, m’pamenenso timakhala ndi zifukwa zambiri zolemekezera amene anapanga zonsezo. Asayansi ena amavomereza umboni umenewo ndipo umawafika pamtima. Mosakayikira anganene kuti sayansi yawathandiza kumudziŵa Mulungu. Koma zikuoneka kuti asayansi ena sadzavomereza zoti kuli Mulungu ngakhale atapatsidwa umboni wochuluka motani. Nanga bwanji inuyo?

Ngati mungakonde kupenda umboni umene ulipo pankhani imeneyi, tikukulimbikitsani kuchita zimenezo. Buku lakuti Is There a Creator Who Cares About You? linakonzedwa kuti likuthandizeni kupeza mayankho ofunika kwambiri pa nkhani imeneyi. * Kuwonjezera pamenepo, lidzakuthandizani kupenda mtundu wachiŵiri wa umboni wosonyeza kuti Mulungu alipo: Baibulo.

Baibulo lili ndi umboni wochuluka wosonyeza kuti linauziridwa ndi winawake wanzeru zoposa za anthu. Mwachitsanzo, lili ndi maulosi ambiri, kapena kuti mbiri yolembedwa zinthuzo zisanachitike. Ena mwa maulosi ameneŵa amafotokoza zinthu zimene zikuchitika nthaŵi yathu ino! (Mateyu 24:3, 6, 7; Luka 21:10, 11; 2 Timoteo 3:1-5) Anthu sanganeneretu za m’tsogolo popanda kulakwitsa penapake. Kodi aliponso wina amene angachite zimenezo kupatulapo Mulungu?

Koma Baibulo sikuti limangotisonyeza ngati kuli Mulungu kapena ayi. Limatiphunzitsanso dzina lake, limafotokoza khalidwe lake, ndipo limasonyeza mmene Mulungu wakhalira ndi chidwi ndi anthu zaka zonsezi. Limafotokoza ngakhale zimene watikonzera m’tsogolo muno. Pankhani zonsezi, sayansi singatithandize kupeza mayankho. Indedi, sayansi ya anthu singatipatse chiyembekezo chenicheni m’moyo wathu. Ndiponso singatiphunzitse mfundo za makhalidwe oyenera.

Maziko a Mfundo za Makhalidwe Abwino

N’zomvetsa chisoni kuti zimene anthu ambiri akuchita potsatira sayansi masiku ano zikuoneka kuti zikuwononga makhalidwe abwino. Katswiri wa sayansi ya zinthu zamoyo Richard Dawkins, amene sakhulupirira zoti kuli Mulungu, anati: “M’chilengedwe chokhala ndi mphamvu zopanda wina wanzeru woziwongolera ndiponso chimene zinthu zimaswana popanda cholinga chilichonse, anthu ena amapwetekedwa, ena amakhala ndi mwayi, popanda chifukwa chilichonse, ndipo sipakhala zachilungamo.” Kodi simukuona kuti kaonedwe koteroko ka dziko lathuli n’kosapatsa chiyembekezo chilichonse? Kodi simukuganiza kuti anthu amafunika kukhala ndi mfundo za makhalidwe abwino zoti akazitsatira zinthu ziziwayendera bwino koma akaziphwanya azilangidwa?

Pamenepa tikupezapo kusiyana kwakukulu pakati pa mmene Baibulo limaonera anthu ndi mmene anthu osakhulupirira Mulungu koma okhulupirira kuti zamoyo zinachita kusanduka kuchokera ku zinthu zina amawaonera anthu. Mawu a Mulungu amatsindika kuti anthu ndi apadera kwambiri m’chilengedwe, koma chiphunzitso chakuti zamoyo zinachita kusanduka kuchokera ku zinthu zina chimasonyeza kuti anthu anakhalako chifukwa cha zinthu zimene zinachitika mwangozi popanda cholinga chilichonse. Baibulo limafotokoza kuti anthu anapangidwa m’chifanizo cha Mulungu wachilungamo ndi wachikondi ndipo angathe kukhala ndi makhalidwe abwino ndi moyo wosangalala. Chiphunzitso chakuti zamoyo zinachita kusanduka kuchokera ku zinthu zina, chimene chimagogomezera mfundo yakuti zamoyo zamphamvu n’zimene zimapulumuka, sichitha kufotokoza chifukwa chimene anthu amakhalira achikondi ndiponso okoma mtima.

Chiphunzitso chakuti zamoyo zinachita kusanduka kuchokera ku zinthu zina sichingatipatse chiyembekezo chenicheni kapena cholinga chokhalira ndi moyo. Baibulo limatiuza cholinga chochititsa chidwi cha Mlengi chokhudza tsogolo lathu. Iye wanena momveka bwino cholinga chake, kuti: “Ndidzakudalitsani ndi tsogolo lodzaza ndi chiyembekezo.”—Yeremiya 29:11, Contemporary English Version.

Phunzirani za Mlengi

Wamasalmo wina wanzeru anavomereza modzichepetsa kuti: “Dziŵani kuti Yehova ndiye Mulungu; Iyeyu anatilenga, ndipo ife ndife ake.” (Salmo 100:3) Kwa anthu ambiri oganiza bwino, kuvomereza zimenezi modzichepetsa n’komveka bwino kwambiri kusiyana ndi ziphunzitso zamasiku ano zakuti moyo wa anthu unangokhalako mwangozi.

Sayansi yamakono nthaŵi zina imalimbikitsa mfundo yodzitukumula yakuti maganizo ndi nzeru za anthu n’zimene zingatsogolere bwino kwambiri moyo wathu. N’zomvetsa chisoni kuti zipembedzo zodziŵika bwino nazonso zimaphunzitsa mfundo yolakwika yomweyo. Komabe, nzeru za anthu n’zopereŵera ndipo zidzapitirizabe kukhala zotero. Mtumwi Paulo ankadziŵa zinthu zambiri zauzimu, koma anakhalabe wodzichepetsa. Iye ananena modzichepetsa kuti: “Zimene tiona tsopano, timaziona ngati zithunzi chabe m’galasi . . . Tsopano ndimangodziŵa mopereŵera.”—1 Akorinto 13:12, Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chichewa Chamakono.

N’zoona kuti chikhulupiriro chenicheni mwa Mulungu sichidalira sayansi yamakono. Koma kwa munthu woganizira zinthu mofatsa, sayansi ingalimbitse chikhulupiriro chake. Chikhulupiriro chenicheni ndiponso kukonda zinthu zauzimu n’kofunika kuti munthu akhale ndi moyo watanthauzo ndi wosangalala. (Mateyu 5:3) Ngati mugwiritsa ntchito Baibulo kuti mumudziŵe bwino kwambiri Yehova ndi cholinga chake kwa anthu ndi dziko lapansili, mudzapeza maziko okhalira ndi moyo watanthauzodi ndipo mudzapeza chiyembekezo chenicheni.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 18 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Bokosi/Zithunzi patsamba 17]

Zimene asayansi eniakewo amanena

Asayansi ambiri amanena poyera kuti amakhulupirira kuti kuli Mlengi. Ngakhale kuti ena a iwo ali ndi chithunzi chosaoneka bwino kwenikweni m’maganizo mwawo cha mmene Mulungu alili, amavomerezabe kuti umboni umene ulipo umasonyeza kuti pali Wokonza Zinthu wanzeru. Taonani mawu otsatiraŵa amene asayansiwo ananena:

“Monga munthu wasayansi, ndimayang’ana m’chilengedwe chathuchi ndipo ndimaona zinthu zopangidwa m’njira yovuta kumvetsa kwambiri moti zimandipangitsa kuzindikira kuti pali winawake wanzeru amene anapanga zinthu zovuta kumvetsa zolongosoka bwino zimenezo.”—anatero Andrew Mcintosh, katswiri wa masamu wa ku Wales, ku United Kingdom

“Kuvuta kumvetsa kwa zinthu m’chilengedwe kumasonyeza poyera kuti kuli Mlengi. Munthu akamvetsa mmene zinthu zilizonse zamoyo ndi zopanda moyo zimagwirira ntchito, amaona kuti ndi zinthu zovuta kuzimvetsa kwambiri.”—anatero John K. G. Kramer, katswiri wa zimene zimachitika m’kati mwa zinthu zamoyo wa ku Canada

“Zinthu zamoyo zimasonyeza kuti n’zolinganizidwa bwino kwambiri. Zinakonzedwa ndi Mphamvu inayake yapadera imene ineyo ndimaitcha Mulungu. Pamenepa m’pamene chikhulupiriro chimagwirizana ndi sayansi. M’malo motsutsana ndi sayansi, chikhulupiriro chimathandizira pamene sayansi yapereŵera, ndipo chimatithandiza kumvetsetsa bwino chilengedwe.”—anatero Jean Dorst, Katswiri wa sayansi ya zinthu zamoyo wa ku France

“Sindingathe kuganiza kuti chilengedwe ndi moyo wa anthu zinangokhalako popanda winawake wanzeru woziyambitsa, popanda winawake wauzimu ‘wachikondi,’ wapamwamba kwambiri kuposa chilengedwe ndi malamulo ake onse.”—anatero Andrey Dmitriyevich Sakharov, katswiri wa sayansi ya nyukiliya wa ku Russia

“Nyama iliyonse m’njira inayake inapangidwa kuti iziyenerana ndi kumene imakhala, ndipo zimandichititsa kuzindikira kuti kuvuta kumvetsa kwa mmene zinthu zinapangidwira kumasonyeza kuti kunja kuno kuli Mlengi, osati mphamvu zopanda dongosolo lililonse zochititsa zamoyo kusanduka kuchokera ku zinthu zina.”—anatero Bob Hosken, katswiri wa zimene zimachitika m’kati mwa zinthu zamoyo wa ku Australia

[Bokosi/Zithunzi patsamba 18]

Nkhani ya mu Genesis yapambana ataiunika

Gerald Schroeder, amene kale anali pulofesa wa sayansi ya nyukiliya analemba kuti: “Baibulo limafotokoza m’mavesi 31, m’mawu mahandiredi ochepa okha, zinthu zimene zinatenga zaka mabiliyoni 16 kuti zichitike. Zinthu zimenezi asayansi azilemba m’mawu mamiliyoni ambiri. Baibulo limafotokoza ndondomeko yonse ya mmene nyama zinakhalirako m’ziganizo eyiti zokha. Poona mmene nkhani ya m’Baibulo imeneyi ilili yachidule, n’zochititsa chidwi kwambiri kuti ndondomeko ya mmene zinthu zinachitikira ya mu Genesis chaputala 1 imagwirizana ndi zimene sayansi yamakono yatulukira. Zimenezi n’zochititsa chidwi makamaka tikaganizira kuti mfundo zonse zimene zafotokozedwa mu Genesis chaputala 1 zinalembedwa zaka mahandiredi, mwinanso masauzande zapitazo, choncho sizinakhudzidwe m’njira iliyonse ndi zimene sayansi yamakono yatulukira. Sayansi yamakono ndi imene yagwirizana ndi nkhani ya m’Baibulo ya chiyambi chathu.”—linatero buku lotchedwa THE SCIENCE OF GOD—THE CONVERGENCE OF SCIENTIFIC AND BIBLICAL WISDOM.

[Zithunzi]

Baibulo limafotokoza nyengo sikisi pamene zinthu zinalengedwa

[Chithunzi patsamba 20]

Baibulo lili ndi umboni wamphamvu wosonyeza kuti linauziridwa ndi Mulungu