Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuyeza Dziko Lapansi ndi Ndodo

Kuyeza Dziko Lapansi ndi Ndodo

Kuyeza Dziko Lapansi ndi Ndodo

KODI munayamba mwamvapo za katswiri wachigiriki wa masamu ndi wa sayansi ya zakuthambo wotchedwa Eratosthenes? Mwina dzina lake n’lodziŵika bwino makamaka pakati pa akatswiri a sayansi ya zakuthambo. N’chifukwa chiyani amamulemekeza kwambiri?

Eratosthenes anabadwa pafupifupi m’chaka cha 276 Kristu Asanabwere ndipo maphunziro ake ena anachitira ku Athens, ku Greece. Koma nthaŵi yambiri ya moyo wake anakhalitsa ku Alexandria, m’dziko la Egypt, limene nthaŵi imeneyo linali pansi pa ulamuliro wa Agiriki. Pafupifupi m’chaka cha 200 Kristu Asanabwere, Eratosthenes anaganiza zoyeza kukula kwa dziko lapansi mwa kugwiritsa ntchito ndodo basi. ‘Sizingatheke!’ mwina mungatero. Kodi anachita bwanji zimenezi?

Mu mzinda wa Syene, (umene panopa umatchedwa Aswân), Eratosthenes anaona kuti nthaŵi ya 12 koloko tsiku loyamba la chilimwe, dzuwa linali pamutu penipeni. Anadziŵa zimenezi chifukwa panalibe chithunzi chomwe chinkaoneka kuwala kwa dzuwa kukafika pansi pa zitsime zakuya. Komabe, 12 koloko tsiku lomwelo mu mzinda wa Alexandria, umene unali pa mtunda wa mastadiya * 5,000 kumpoto kwa Syene, chithunzi chinkaoneka. Zimenezo zinamupatsa Eratosthenes nzeru zinazake.

Eratosthenes anaimika ndodo pansi. Dzuwa litafika pamutu 12 koloko, anayeza kukula kwa kona imene inalipo pakati pa ndodoyo ndi chithunzi chake ku Alexandria. Anapeza kuti konayo inali yaikulu madigiri 7.2.

Eratosthenes ankakhulupirira kuti dziko n’lozungulira, ndipo ankadziŵa kuti chinthu chozungulira chimakhala ndi madigiri 360. Choncho anagawa 360 ndi kona imene anayeza ija ya 7.2. Kodi anapeza yankho lotani? Kona yakeyo imalowamo ka 50 mu chinthu chozungulira chathunthu. Choncho anadziŵa kuti mtunda wochoka ku Syene kupita ku Alexandria, kapena kuti mastadiya 5,000, uyenera kulowamo ka 50 mu mtunda wozungulira dziko lonse lapansi. Atachulukitsa 50 ndi 5000, Eratosthenes anapeza kuti kukula kwa dziko lapansi ndi mastadiya 250,000.

Kodi nambala yakeyo n’njofanana bwanji ndi nambala imene amapeza akachita masamu a masiku ano? Nambala ya mastadiya 250,000 n’chimodzimodzi ndi makilomita 40,000 mpaka 46,000 masiku ano. Pogwiritsa ntchito zinthu zouluka m’lengalenga zimene zimazungulira dziko lapansi, akatswiri a sayansi ya zakuthambo anayeza kukula kwa dziko lapansi kuchokera kumpoto mpaka kumwera ndipo anapeza makilomita 40,008. Choncho, zaka zopitirira 2,000 zapitazo, Eratosthenes modabwitsa kwambiri anapeza nambala imene ili yosasiyana kwenikweni ndi nambala imene anthu amapeza masiku ano. Kulondola kwakeko n’kodabwitsa kwambiri makamaka tikaganizira kuti anangogwiritsa ntchito ndodo ndi masamu basi! Akatswiri a sayansi ya zakuthambo masiku ano amagwiritsa ntchito mfundo zofanana ndi za njira imeneyi poyeza kutalika kwa mitunda m’dera limene lili kunja kwa dzuwa lathuli ndi mapulaneti ake naini.

Ena angaone kuti n’zodabwitsa kwambiri kuti Eratosthenes anadziŵa kuti dziko lapansi n’lozungulira. N’zodabwitsa chifukwa chakuti pofika mpaka zaka mahandiredi ochepa okha zapitazo, ngakhale asayansi ena anzeru ankakhulupirira kuti dziko n’lophwatalala. Agiriki akale anadziŵa kuti dziko n’lozungulira chifukwa cha kafukufuku wawo wasayansi. Komabe, pafupifupi zaka 500 Eratosthenes asanakhaleko, mneneri wina wachihebri anauziridwa kulemba kuti: ‘Ndiye Iye [Mulungu] amene akhala pamwamba pa malekezero a dziko lapansi [“lozungulira,” NW].’ (Yesaya 40:22) Yesaya sanali wasayansi. Kodi anadziŵa bwanji kuti dziko lapansi n’lozungulira? Ndi Mulungu amene anamuuzira zinthu zoona zimenezi.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Mastadiya anali muyezo wachigiriki woyezera kutalika kwa chinthu. Ngakhale kuti kukula kwake kunkasiyanasiyana m’madera osiyanasiyananso, zikukhala ngati stadiya imodzi inkakhala yaitali mamita 160 mpaka 185.

[Chithunzi patsamba 10]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Kuwala kwa dzuwa

Syene

7.2°

Alexandria

7.2°