Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mayi Wanzeru

Mayi Wanzeru

Mayi Wanzeru

Mayi amene amazindikira zimene ana ake amafunikira ndipo amawasamala anawo amachita khama kuti awapatse zakudya zopatsa thanzi. Amachitanso khama ngati lomwelo powapatsa zakudya zauzimu.

Posachedwapa, mayi wina ku Brazil analemba kalata ku ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova m’dziko limenelo yoyamikira bulosha la Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? Iye analemba kuti: “Buloshalo linandikhudza mtima kwambiri. Nditaona patalipatali phunziro lonena za machitachita amene Mulungu sakondwera nawo, ndinazindikira nthaŵi yomweyo kuti ndiyenera kusonyeza zinthu zofunika zimenezi kwa ana anga, atsikana aŵiri azaka 10 ndi 11, ndi mnyamata wa zaka 5.” Iye anapitiriza kuti: “N’zofunikadi kwambiri kukhala ndi mabuku ngati ameneŵa ophunzitsira banja langa njira za Mulungu.”

Anapemphanso mabuku ena ofotokoza za m’Baibulo. Ngati nanunso mumalakalaka chakudya chauzimu cha inuyo ndi anthu a m’banja mwanu, mungalandire bulosha la Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? Ingolembani zofunika m’mizere ili m’munsiyi ndipo tumizani ku adiresi imene ili pomwepoyo kapena ku adiresi yoyenera pa maadiresi amene alembedwa pa tsamba 5 la magazini ino.

□ Popanda kulonjeza kuti ndidzachita chilichonse, ndikupempha bulosha la Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?

□ Chonde nditumizireni munthu kuti ayambe kuchita nane phunziro la Baibulo lapanyumba laulere.