Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Ukumbukire Mlengi Wako”

“Ukumbukire Mlengi Wako”

“Ukumbukire Mlengi Wako”

“Ukumbukire Mlengi wako pa masiku a unyamata wako, asanafike masiku a mabvuto, zisanafike zaka zimene udzanena kuti: Ndilibenso zondisangalatsa.”—Mlaliki 12:1, “Malembo Oyera.”

MAWU ochokera m’Baibulo amene ali pamwambaŵa ndi opangitsa munthu kuganiza. Munthu umakhala wachinyamata kamodzi kokha basi. Patsogolo, mudzakumbukira zaka zanu zaunyamata, ndipo mwina mudzasangalala nazo, kapena mudzamva nazo chisoni. Kodi inuyo zidzakukhalirani bwanji? Kodi mungatani kuti zinthu zikuyendereni bwino?

“Ukumbukire Mlengi wako,” limalimbikitsa choncho Baibulo, monga momwe mawu ali pamwambawo akunenera. Kodi mungachite bwanji zimenezo? Mwa kumvera malamulo ndi mfundo za Mulungu, zimene zalembedwa m’Mawu ake, Baibulo. Zimenezi sizikutanthauza kuti muyenera kukhala ndi moyo wosasangalala wotsatira zachipembedzo monyanyira, ndi wodzimana zinthu zonse zosangalatsa. Mosiyana ndi zimenezo, kukumbukira Mlengi wanu kudzakuchititsani kukhala ndi chimwemwe chambiri chimene chingatheke kuti munthu akhale nacho. Kodi zimenezo zingatheke bwanji?

Mwachitsanzo, tayerekezerani kuti mwapatsidwa galimoto ndi laisensi yake yoyendetsera. Muli ndi ufulu wambiri tsopano, umene ungakubweretsereni chisangalalo chochuluka. Tangoganizirani malo amene mungapiteko! Komabe, ufulu wanu umene mwangoupeza kumenewu umabweretsanso udindo waukulu. Mukamayendetsa galimotoyo, muyenera kumvera malamulo apamsewu ndi kusamala pa maloboti, kusathamanga mopitirira liŵiro lololeka, ndiponso kumvera zizindikiro zapamsewu zokuchenjezani. Kodi udindo umenewu umakulepheretsani kusangalala poyendetsa galimotoyo? Kutalitali! M’malo mwake, umakutetezani. Kuchita ngozi sikosangalatsa m’pang’onong’ono pomwe, kodi si choncho?

N’chimodzimodzi ndi ufulu umene Mlengi wanu, Yehova Mulungu, wakupatsani. Mukamakula kusanduka munthu wachikulire, iye amakulolani kusankha mmene mukufuna kukhalira moyo wanu. (Deuteronomo 30:19; Miyambo 27:11) Umenewo ndi mwayidi wapadera kwambiri. Koma ufulu umenewo umabweretsanso udindo waukulu kwambiri. M’Mawu ake, Yehova waikamo ‘malamulo apamsewu’—mfundo zimene akufuna kuti muzitsatira pamoyo wanu. Kodi mfundo zimenezi zimachepetsa chimwemwe chanu? Ayi ndithu! M’malo mwake, zimakutetezani ku mavuto aakulu amene achinyamata ambiri amakumana nawo masiku ano.

Federico, amene tsopano ali ndi zaka za m’ma 30, akudziŵa kuti zimenezo n’zoona. Ali mnyamata, anaona anzake a kusukulu akuchita zinthu zosiyanasiyana zimene iye ankadziŵa kuti ayenera kupeŵa. Iye akuti: “Ankaoneka ngati akusangalala, koma sindinaganize kuti analidi osangalala.” Poganizira zakale, Federico ndi wosangalala kuti anali ndi mfundo za m’Baibulo zoti zimutsogolere panthaŵi ya unyamata wake. “N’zoona kuti ndinali ndi mavuto oti ndilimbane nawo, monga mmene amachitira wachinyamata aliyense,” iye akutero. “Koma Baibulo linanditetezadi. Ndipo nthaŵi zonse panali Mkristu mnzanga amene akanatha kundithandiza. Kutsatira mfundo za m’Baibulo kwandipatsa chimwemwe chachikulu kwambiri kuposa mmene ndinkaganizira.”

Yehova Mulungu akufuna kuti inuyo mukhale wosangalala, kusangalala kwenikweni. Kusangalala kumeneko kumatanthauza zambiri osati kungosangalala kunja kokhaku koma mumtima muli chisoni. Baibulo limati: “Mnyamatawe, ukondwe nthawi ya unyamata wako.” Koma vesi la m’Baibulo lomwelo lilinso ndi chenjezo. Limati: “Koma udziwe kuti Mulungu adzakuitana ku mlandu chifukwa cha zonse’zo.”—Mlaliki 11:9, Malembo Oyera.

Kumbukirani Mlengi wanu mwa kugwiritsa ntchito bwino ufulu umene wakupatsani. Ngati mutero, dziŵani kuti Mlengi wanu adzakukumbukirani. Baibulo limati: “Madalitso a Yehova alemeretsa, sawonjezerapo chisoni.”—Miyambo 10:22.

Pofuna kuthandiza achinyamata kuthana ndi mavuto amene amakumana nawo akamakula, Mboni za Yehova zafalitsa buku la masamba 320 lotchedwa Mafunso Achichepere Akufunsa . . . Mayankho Amene Amathandiza. Pofika panopa, mabuku ameneŵa okwana pafupifupi 34 miliyoni asindikizidwa m’zinenero 77. Mungapeze buku lanulanu mwa kulankhula ndi Mboni za Yehova kudera kwanuko.

[Zithunzi pamasamba 8, 9]

Kuti Zinthu Zikuyendereni Bwino Monga Wachinyamata

Muzipatula nthaŵi yoŵerengera Mawu a Mulungu

Muzichita khama mu utumiki

Peŵani mayanjano oipa

Pitirizani kulankhulana bwino ndi makolo anu

[Mawu a Chithunzi]

Brochure cover: Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.