Zifukwa Zimene Asayansi Ena Amakhulupirira Mulungu
Zifukwa Zimene Asayansi Ena Amakhulupirira Mulungu
SAYANSI nthaŵi zonse ikutulukira zinthu zatsopano zokhudza chilengedwe ndi zamoyo zimene zili padziko lathuli. Ngakhale zili choncho, asayansi ndi anthu wamba amazunguzikabe ndi mafunso ofunika kwambiri monga aŵa: Kodi chilengedwe chinakhalako bwanji? Kodi chilengedwe chisanakhaleko kunali chiyani? N’chifukwa chiyani chilengedwe chimaoneka kuti chinakonzedwa kuti chikhale ndi zinthu zamoyo? Kodi zamoyo zinakhalako bwanji padziko lapansi pano?
Sayansi mpaka pano siyankhabe mokhutiritsa mafunso ameneŵa. Anthu ena amakayikira zoti idzatha kuwayankha. Choncho anthu ambiri akakamizika kupendanso maganizo ndi zikhulupiriro zawo. Tiyeni tione nkhani zitatu zovuta zimene zikuchititsa asayansi ena kuganiza kuti mwina kunja kuno kuli Mlengi.
Kodi Chilengedwe Chochunidwa Bwinochi Chinangokhalako Mwangozi?
Nkhani imodzi yaikulu ndi yokhudza kuchunidwa bwino kwa chilengedwe chathuchi. N’chifukwa chiyani chilengedwe chili ndi malamulo osasintha amene ali oyenerera kuti pakhale dziko ngati lathuli ndipo m’dzikomo mukhale zamoyo ngati zimene zili padziko lapansili?
Kodi tikati kuchunidwa bwino tikutanthauza chiyani? Mwachitsanzo, taganizirani mmene mphamvu zinayi za m’chilengedwe zinachunidwira mwanjira inayake yapadera: mphamvu ya maginito imene magetsi ali nayo, mphamvu yokoka, mphamvu yaikulu ya nyukiliya, ndi mphamvu yaing’ono ya nyukiliya. * Mphamvu zimenezi zimakhudza chinthu chilichonse m’chilengedwe. N’zochunidwa bwino kwambiri moti zitangosinthidwa pang’ono chabe, m’chilengedwe simungakhalenso zamoyo.
Kwa anthu ambiri oganiza bwino, zimenezi sizinangochitika mwangozi. John Polkinghorne, katswiri wa sayansi ya kapangidwe ka zinthu amene kale anali pa yunivesite ya Cambridge, anati: “Munthu akazindikira kuti malamulo a m’chilengedwe ayenera kukhala ochunidwa bwino kwambiri kuti chilengedwe chikhale ngati mmene timachioneramu, amazindikiranso kuti chilengedwe sichinangokhalako mwangozi, koma kuti chiyenera kukhala n’cholinga.”
Katswiri wa sayansi ya kapangidwe ka zinthu wa ku Australia Paul Davies ananena mfundo yangati yomweyo. Iye anati: “Sindikukayikira kuti pali asayansi ambiri amene . . . amanyoza anthu okhulupirira kuti kunja kuno kungakhale Mulungu, kapena ngakhale mphamvu imene inalenga zonse.” Iye anawonjezera kuti: “Ineyo pandekha sindinyoza nawo. . . . Sindingakhulupirire kuti ifeyo tinakhalapo m’chilengedwe mwangozi chabe, . . . kuti zinazake zinangosokonekera basi ifeyo n’kupangika.”
Zovuta Kumvetsa
Nkhani yachiŵiri imene ikuvutitsa asayansi masiku ano n’njakuti chilengedwe chimene timachionachi n’chovuta kumvetsa kwambiri. Aliyense amadziŵa kuti ngati chinthu chili chovuta kwambiri kumvetsa, mwachionekere sichinangochitika mwangozi. Taganizirani chitsanzo ichi:
Pali zinthu zambiri zimene ziyenera kusanganikirana m’njira inayake yapadera kuti DNA, imene ili ngati njerwa zoumbira moyo, ipangike. Zaka makumi atatu zapitazo, Dr. Frank Salisbury wa pa yunivesite ya Utah State, ku America, anachita masamu enaake kuti aone ngati DNA, imene ili yofunika kuti moyo ukhalepo, ingapangike mwangozi. Anapeza kuti n’zosatheka m’pang’onong’ono pomwe kuti zimenezi zichitike.
Nkhani ya kuvuta kumvetsa kwa zamoyo imakula makamaka zinthu zamoyozo zikakhala ndi ziwalo zopangidwa m’njira yovuta kumvetsa zimene zikanakhala zopanda ntchito pakanapanda ziwalo zina zopangidwanso m’njira yovuta kumvetsa. Tiyeni tione chitsanzo cha kubereka.
Malinga ndi ziphunzitso zakuti zamoyo zinasanduka kuchokera ku zinthu zina, akuti zamoyo zinapitirizabe kuberekana pamene zinkasintha n’kumasanduka zovuta kuzimvetsa kapangidwe kake. Koma panthaŵi inayake, zinthu zazikazi za m’mitundu ya zamoyo zina zinafunika kukhala ndi maselo oberekera ofunika kukumana ndi maselo oberekera a zinthu zazimuna zoyenerana ndi zinthu zazikazizo. Pofuna kupereka timaulusi timene timapanga DNA tokwanira bwino kwa ana ake, maselo oberekera a kholo lililonse amafunika kugaŵikana m’njira inayake yapadera kuti atsale ndi theka la timaulusi topangira DNA timene amakhala nato nthaŵi zonse. Zimenezi zimathandiza kuti mwanayo asakhale ndi timaulusi topangira DNA tochuluka kuposa timene amafunikira.
Komabe, zinthu zomwezi zinayenera kuchitikanso m’mitundu ina ya zamoyo. Choncho, kodi zinachitika bwanji kuti “mayi woyamba” wa mtundu uliwonse wa zamoyo athe kubereka atakumana ndi “bambo woyamba” wokhala kale ndi ziwalo zonse zofunika? Kodi aŵiri onsewo akanatha bwanji mwadzidzidzi kutha kuchepetsa ndi theka timaulusi topangira DNA m’maselo awo oberekera m’njira yoyenera kuti apange mwana wathanzi wofanana ndi makolo onse aŵiri? Ndipo ngati ziwalo zoberekera zimenezi zinapangika pang’onopang’ono, kodi zinthu zazikazi ndi zazimuna za mtundu uliwonse wa zamoyo zikanatha bwanji kupulumuka pamene ziwalo zofunika kwambiri zimenezo zinali zisanapangike bwinobwino?
Ngakhale mu mtundu umodzi wokha wa zamoyo, n’zosatheka m’pang’onong’ono pomwe kuti zinthu zazikazi ndi zazimuna zikhale zoyenerana chonchi mwangozi basi. Ndiye kunena kuti zimenezi zinachitika m’mitundu yosiyanasiyana ya zamoyo ndithudi n’zosamveka. Kodi chiphunzitso chopanda umboni uliwonse choti zamoyo zinachita kusanduka kuchokera ku zinthu zina chingafotokoze mmene zinthu zovuta kumvetsa zoterozo zinachitikira? Kodi zinthu zongochitika mwangozi, zopanda dongosolo lililonse, ndiponso zopanda woziyambitsa zingachititse kuti zamoyo zikhale ndi ziwalo zoberekera zoyenerana bwino choncho? Zinthu zamoyo zili ndi zizindikiro zambirimbiri zosonyeza kuti winawake anachita kuzikonza ndipo pozikonzapo anaoneratu za m’tsogolo, umboni wosonyeza kuti pali Mkonzi wanzeru.
Akatswiri ambiri a maphunziro afika pozindikira zimenezi. Mwachitsanzo, katswiri wa masamu William A. Dembski analemba kuti kukonzedwa bwino kwa zinthu kumene “kumaoneka m’mbali zosiyanasiyana za chilengedwe . . . kungatheke kukufotokoza bwino kokha mwa kukhulupirira kuti pali winawake wanzeru amene anakuyambitsa.” Katswiri wa sayansi ya zimene zimachitika m’kati mwa zinthu zamoyo Michael Behe anafotokoza mwachidule zimene umboniwo umasonyeza motere: “Munthu akhoza kukhala Mkatolika wabwino koma n’kumakhulupiriranso ziphunzitso za Darwin. Koma sayansi ya zimene zimachitika m’kati mwa zinthu zamoyo yachititsa kuti kukhale kovuta kuti munthu akhale wasayansi woganiza bwino komanso azikhulupirira ziphunzitso za Darwin.”
Umboni Wopereŵera wa Zinthu Zakale Zokwiririka Pansi
Nkhani yachitatu imene yazunguza mitu asayansi ndi yokhudza umboni wa zinthu zakale zokwiririka pansi. Ngati kusanduka kwa zamoyo kuchokera ku zinthu zina kunachitika panthaŵi yaitali kwambiri,
tiyenera kupeza zamoyo zina zooneka ngati zili pakatikati pa magulu akuluakulu a zamoyo zimene zilipo masiku ano. Komabe, zinthu zambirimbiri zakale zokwiririka pansi zimene zakumbidwa chiyambire nthaŵi ya Darwin sizinapereke umboni uliwonse woterowo. Palibe amene anapezapo zamoyo zooneka ngati zili pakatikati pa magulu akuluakulu a zamoyo zimene zilipo masiku ano.Chifukwa cha zimenezi, asayansi angapo anena kuti umboni wakuti zinthu zamoyo zinachita kusanduka kuchokera ku zinthu zina ndi wopereŵera kwambiri ndiponso umadzitsutsa wokha moti sungagwiritsidwe ntchito kusonyeza kuti zamoyo zinachita kusanduka kuchokera ku zinthu zina. Katswiri wopanga zinthu zouluka Luther D. Sutherland analemba m’buku lake lotchedwa Darwin’s Enigma kuti: “Umboni wasayansi umasonyeza kuti nthaŵi iliyonse imene zamoyo zosiyana ndi zina zinaoneka koyamba Padziko Lapansi, kuyambira pa zamoyo zokhala ndi selo imodzi kufika pa anthu, zamoyozo zinkakhala zothaitha kukonzedwa ndipo ziwalo zake zinkakhala zikugwira kale ntchito bwinobwino. Zimene tingaone kuchokera pa mfundo imeneyi n’zakuti payenera kuti panali winawake wanzeru amene
analipo zamoyo zisanayambe kukhala Padziko Lapansi.”Koma umboni wa zinthu zakale zokwiririka pansi umagwirizana kwambiri ndi ndondomeko ya m’buku la m’Baibulo la Genesis ya mmene zamoyo zinapangidwira. Donald E. Chittick, katswiri wa zimene zimachitika m’kati mwa zinthu zosiyanasiyana amene analandira digiri yapamwamba kwambiri pa yunivesite ya Oregon State, anati: “Kupenda bwino umboni umene zinthu zakale zokwiririka pansi zimapereka kumatichititsa kuzindikira kuti nyama zinkaberekana za mtundu umodzi womwewo monga momwe buku la Genesis limanenera. Sizinkasanduka kuchokera ku mitundu ina ya nyama. Umboni umene ulipo masiku ano, monga momwe zinalili pa nthaŵi ya Darwin, umagwirizana ndi zimene zinalembedwa m’buku la Genesis zoti zinthu zinachita kulengedwa. Nyama ndi zomera zikupitirizabe kuberekana za mtundu umodzi womwewo. Ndipo kusiyana kumene kulipo pakati pa umboni wochokera ku zinthu zakale zokwiririka pansi ndi ziphunzitso za Darwin n’kwakukulu kwambiri moti asayansi ena ayamba kukhulupirira kuti zamoyo zooneka ngati zili pakatikati pa mitundu ya zamoyo imene ilipo masiku ano sizidzapezeka.”
Kuzindikira Zimene Umboniwo Ukusonyeza
Zimene tafotokozazi ndi mbali yaing’ono chabe ya mafunso osayankhidwa amene amazunguza mutu anthu amene savomereza kuti kuli Mlengi. Asayansi ena azindikira kuti anthu akamakana zoti kuli Mulungu amatero osati chifukwa ali ndi umboni wodalirika ndiponso mfundo zomveka bwino, koma chifukwa cha mfundo zongopeka basi.
Choncho, pambuyo pothera moyo wake wonse akuchita kafukufuku ndi ntchito yaphindu ya sayansi, katswiri wa sayansi ya zakuthambo Allan Sandage anati: “Kuphunzira sayansi n’kumene kunandichititsa kuzindikira kuti dzikoli n’lovuta kumvetsa kwambiri moti sayansi singalifotokoze. Ndi mphamvu inayake yauzimu yokha imene ingandithandize kumvetsa mmene zinthu zinakhalirako.”
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 6 Kuti mumve zambiri, onani mutu 2 m’buku lakuti Is There a Creator Who Cares About You? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
[Bokosi patsamba 14]
Mafunso amene amazunguza mitu asayansi
▪ N’chifukwa chiyani mphamvu zinayi zofunika kwambiri m’chilengedwe zili zochunidwa bwino kwambiri, zimene zinapangitsa kuti chilengedwe ndi zamoyo zikhalepo?
▪ Kodi munthu angafotokoze bwanji chifukwa chimene zinthu zamoyo zilili zopangidwa m’njira yovuta kumvetsa ndiponso yosatheka kuifewetsako?
▪ N’chifukwa chiyani umboni wa zinthu zakale zokwiririka pansi uli wopereŵera, ndipo kodi umboni wosonyeza kuti pali zamoyo zina zooneka ngati zili pakatikati pa magulu akuluakulu a zamoyo zimene zilipo masiku ano uli kuti?
[Bokosi patsamba 16]
Kodi zinangochitika mwangozi?
Posachedwapa, magazini ya National Geographic inasindikiza chithunzi chochititsa chidwi chosonyeza chikondi cha mayi pa mwana wake pachikuto, ndipo munthu wina amene anaŵerenga magaziniyo analembera ku magaziniyo ndipo anati: “Chithunzi cha mayi ndi mwana chimene chili pachikutocho n’chitsanzo chochititsa kaso kwambiri cha chilengedwe. Sindingathe kumvetsa kuti munthu angayang’ane mwana wokongola ameneyo, amene miyezi naini yokha m’mbuyomu anali kadzira kakang’onong’ono kosati n’kuoneka n’komwe, n’kumaganiza kuti kukula kochititsa chidwi kumeneko kunangochitika mwangozi basi.”
Anthu ambiri angagwirizane n’zimene ananena munthu ameneyo. Mlembi wina amene kale anali pulofesa wa sayansi ya kapangidwe ka zinthu, Dr. Gerald Schroeder anayerekezera kuyambika kwa chilengedwe ndiponso zamoyo mwangozi, ndi kuwina katatu nthaŵi zotsatizana pa mpikisano umene amasankha munthu amene wachita mphumi. Iye anati: “Usanakatenge mphoto yako yachitatu, angakutumize kundende chifukwa chokuganizira kuti wabera pa mpikisanowo. Mwayi woti munthu angawine katatu nthaŵi zotsatizana, kapena katatu pamoyo wake wonse, ndi wochepa kwambiri moti tingangoti n’zosatheka.”
[Zithunzi patsamba 15]
Mphamvu yaing’ono ya nyukiliya imachititsa kuti dzuwa lathu liziyaka pang’onopang’ono
Mphamvu yokoka imachititsa kuti zinthu zizikhala pansi padziko pano
Mphamvu yaikulu ya nyukiliya imachititsa kuti tinthu tokhala pakati pa maatomu tizigwirana
Mphamvu ya maginito imene magetsi ali nayo ndi imene imachititsa mphenzi
Mphamvu zinayi zimenezi zikanakhala zosachunidwa bwino kwambiri, zinthu zamoyo sizikanakhalako
[Chithunzi patsamba 15]
Kodi mphamvu zopanda dongosolo lililonse zikanatha bwanji kupanga chinthu chovuta kumvetsa ngati selo limodzi lokhala ndi DNA, ndipo zikanatha bwanji kupanga munthu?
[Zithunzi patsamba 16]
Umboni wa zinthu zakale zokwiririka pansi walephera kusonyeza kuti zamoyo zinachita kusanduka kuchokera ku zinthu zina