Zosangalatsa ndi Zovuta Zimene Zimakhalapo Achinyamata Akamakula
Zosangalatsa ndi Zovuta Zimene Zimakhalapo Achinyamata Akamakula
NTHAŴI imene wachinyamata akukula ikhoza kukhala nthaŵi yosangalatsa kwambiri pamoyo wake. Indedi, kwa anthu ambiri nthaŵi imeneyi imakhaladi yosangalatsa. Ndipo achikulire ambiri amasangalala akamakumbukira nthaŵi ya unyamata wawo.
Komabe, tiyenera kuzindikira kuti tikukhala mu “nthaŵi zoŵaŵitsa.” (2 Timoteo 3:1) Zimenezi zachititsa kuti achinyamata azikumana ndi mavuto ambiri kuposa amene mibadwo ya m’mbuyomu inkakumana nawo. Mwina chimenechi n’chifukwa chake Sabrina Solin Weill, mlembi wamkulu wa magazini inayake ya achinyamata, ananena kuti nthaŵi imene wachinyamata akukula ikhoza kukhala nthaŵi yosautsa kwambiri. Zimakhala ngati kuti wachinyamatayo ali pamwamba kwambiri ndipo akuyenda pakachingwe koonda popanda chinachake pansipa choti chimuwakhe akagwa. Zoonadi, panthaŵi yosautsa imeneyi, thupi la wachinyamata limatha kumamveka ngati silake, amada nkhaŵa, ndipo amazunguzika. Weill analemba kuti: “Panthaŵi imeneyi, achinyamata sakhala ana ndiponso sakhala achikulire, ndipo amakhala akulimbana ndi vuto lokhala mwana komanso wachikulire panthaŵi imodzimodziyo.”
Ngati ndinu wachinyamata ndipo mukukula, kodi mungathane bwanji ndi mavuto amene mumakumana nawo? Ngati ndinu kholo la wachinyamata amene akukula, kodi mungathandizidwe bwanji kukumbukira mmene zaka zosautsa zimenezi zinalili, kuti muthe kumvetsa bwino zimene mnyamata kapena mtsikana wanu akukumana nazo? Mu nkhani zotsatirazi, tikupempha achinyamata ndi achikulire omwe kuti apende bwinobwino zinthu zimene zimachitika panthaŵi imene achinyamata akukula. Kuchita zimenezi kuthandiza achinyamata, osati kuti angothana ndi mavuto a nthaŵi imeneyi basi, komanso kuti zinthu ziwayendere bwino.